Mungakapume ku Vanuatu
Mungakapume ku Vanuatu
YOLEMBEDWA KU NEW CALEDONIA
Kodi mukumva kutopa ndipo mukufuna kupita kwinakwake kukapuma? Mungathe kupita kukasangalala ku chilumba china chowala bwino dzuwa. Muli kumeneku mungakasambire m’madzi oyera bwino, mungakayende m’nkhalango zowirira kapena mungakakumane ndi anthu azikhalidwe zosiyanasiyana, akomweko ndiponso ochokera ku mayiko ena. Kodi malo okongola chonchi adakalipo padziko lapansi? Inde, alipo. Amapezeka ku zilumba zakutali za Vanuatu.
DZIKO la Vanuatu limaoneka ngati chilembo cha “Y” ndipo lapangidwa ndi tizilumba ting’onoting’ono tokwana 80 kum’mwera cha kumadzulo kwa nyanja ya Pacific, pakati pa dziko la Australia ndi Fiji. Akatswiri a sayansi ya nthaka akuti, chigawo cha nthaka chinawombana ndi chigawo china n’kupanga mapiri aatali a pansi pamadzi. Mapiri aatali kwambiri anatulukira pamwamba pa madzi n’kupanga zilumba za Vanuatu. Masiku ano malo amene zigawo za nthaka zimenezi zinawombana, kumachitika zivomerezi zing’onozing’ono ndiponso kuli malo 9 kumene kumakonda kuphulika ziphalaphala zotentha zapansi pa nthaka. Anthu opanda mantha okaona malo amatha kufika pafupi kwambiri ndi kuona ziphalaphala zimenezi.
Zilumba zimenezi zili ndi nkhalango zambiri zowirira. Uku ndiye kuchimake kwa mitengo yaikulu ya mkuyu, imene imapanga mthunzi wabwino. M’nkhalangomu mulinso mitundu yokongola ya maluwa yoposa 400. Magombe okongola ndi matanthwe aatali ali m’mbali mwa madzi oyera bwino okhala ndi nsomba zokongola komanso miyala yooneka bwino. Anthu odzaona zachilengedwe ochokera m’mayiko osiyanasiyana amabwera kuno kudzasambira. Ndipo m’madzimu, makamaka pachilumba cha Epi, mumapezekanso ng’ombe za m’madzi zosalusa ndi zokonda kusewera. *
Anthu Odya Anzawo Ndiponso Olambira Chuma
Azungu oyambirira ofufuza malo anafika ku Vanuatu mu 1606. * Pazilumbazi pankakhala anthu oopsa ndipo ambiri ankadya anthu anzawo. Panthawi imeneyo, kuzilumbazi kunali nkhalango imene mitengo yake inali ndi fungo labwino yomwe inali yofunika kwambiri ku Asia. Azungu amenewa ataona kuti angapeze ndalama zambiri ndi mitengoyi anayamba kuidula mwachisawawa. Kenako anayamba kugwira anthu akumeneko ukapolo.
Anthu ogwidwawo ankapita nawo ku Samoa, Fiji, ndi ku Australia kukagwira ntchito m’minda ya nzimbe ndi thonje. Akuti anthuwa ankafuna okha kukagwira ntchito imeneyi kwa zaka zitatu koma zoona zake n’zakuti ankachita kuwatenga mowakakamiza. Ukapolo utafika pachimake m’zaka za m’ma 1800, pafupifupi theka la amuna a pazilumba zina za ku Vanuatu anatengedwa kukagwira ntchito kunja ndipo ambiri sanabwererenso. Pafupifupi anthu 10,000 ochokera ku zilumba za nyanja ya Pacific, anakafera ku Australia, ambiri chifukwa cha matenda.
Matenda ambiri a kumayiko a azungu anasakazanso kwambiri pa zilumba za ku Vanuatu. Anthu akumeneko sankachedwa kugwidwa ndi chikuku, kolera, nthomba, ndi matenda ena. Buku lina limati: “Chimfine chinapha anthu ambiri moti chinatsala pang’ono kuseseratu anthu onse.”
Amishonale a matchalitchi achikhristu anafika ku Vanuatu mu 1839 koma pasanapite nthawi yaitali anayesedwa ndiwo. Amishonale enanso amene anabwera pambuyo pake nawonso anakhwasulidwa. Patapita nthawi, matchalitchi ambiri a Chipulotesitanti ndi Chikatolika anazika mizu ku zilumba zonsezi. Masiku ano, pafupifupi anthu 80 pa anthu 100 aliwonse a ku Vanuatu amati ndi opembedza. Ngakhale zili choncho, wolemba mabuku wina dzina lake Paul Raffaele, anati: “Anthu ambiri amakhulupirira asing’anga, amene amagwiritsa ntchito miyala ya mizimu pochita matsenga ochititsa munthu kupeza chibwenzi, kunenepetsa nkhumba, kapena kupha mdani.”
Ku Vanuatu ndi kuchimakenso kwa zipembedzo zakalekale za anthu olambira chuma. Pankhondo yachiwiri ya padziko lonse, asilikali okwana 500,000 a ku America anadutsa ku Vanuatu popita ku nkhondo, ku nyanja ya Pacific. Anthu a pazilumbazi anasirira chuma ndi katundu amene asilikaliwo anabweretsa. Nkhondo itatha, asilikaliwo anabwerera kwawo. Koma anasiya katundu wa ndalama zambiri panyanja. Pofuna kunyengerera asilikaliwa kuti abwererenso, zipembedzo za anthu olambira chuma zija zinamanga madoko ndi timabwalo tandege ndipo anthu a m’zipembedzozi ankaliza zida za nkhondo. Mpaka pano, anthu a kumidzi ku chilumba cha Tanna amapemphererabe munthu wotchedwa John Frum yemwe amati ndi “Mesiya wa ku America.” Amaganiza kuti munthu ameneyo tsiku lina adzatulukira n’kuwabweretsera chuma ndi katundu wambiri.
Dziko la Zikhalidwe Zosiyanasiyana
Anthu a pa zilumba zimenezi ali ndi zilankhulo komanso zikhalidwe zambiri zosiyanasiyana. Buku lina limati: “Kutengera chiwerengero cha anthu, dziko la Vanuatu lili ndi zilankhulo zambiri kuposa dziko lina lililonse padziko lapansi.” Kuli zilankhulo zosachepera 105 ndi zinanso zing’onozing’ono. Anthu ambiri amalankhula Chibislama koma Chingelezi ndi Chifalansa ndi zilankhulo za boma.
Anthu ambiri pazilumbazi amafanana pa chinthu chimodzi, amakonda kukhulupirira mizimu. Pakachilumba ka Pentecost anthu amachita mwambo wodalitsa nthaka, umene unayambitsa masewera otchuka padziko lonse. Pochita masewera amenewa anthu amadumpha kuchoka pansanja atazimanga ndi chingwe. Chaka chilichonse panthawi yokolola zilazi, abambo ndi anyamata amadumpha kuchoka pansanja zamatabwa zotalika mamita 20 kapena 30. Kuti asafe akamagwa pansi, amazimangirira chingwe m’miyendo. Amakhulupirira kuti akakhudza pansi ndi mutu wawo, nthakayo imakhala yachonde ndipo chaka chinacho amadzakolola dzinthu zambiri.
Anthu a ku chilumba cha Malekula, ayamba posachedwapa kucheza ndi anthu a kumayiko ena. Kuno kumakhala anthu amitundu iwiri otchedwa a Nambas aang’ono ndi a Nambas aakulu. Zimamveka kuti anthu amene kale anali oopsawa, anadya munthu womaliza mu 1974. Anthu amenewa analekanso khalidwe lomanga mutu wa mwana wamwamuna ndi nsalu kuti akhale ndi mutu wautali. Masiku ano simungamvetse kuti a Nambas ndi anthu ochezeka kwambiri ndipo amakonda kufotokozera alendo za chikhalidwe chawo.
Anthu M’Paradaiso
Anthu ambiri amakonda kukachitira tchuthi chawo ku Vanuatu. Koma Mboni za Yehova zinafika ku zilumbazi zaka 70 zapitazo kudzathandiza anthu mwauzimu. Khama la Mbonizi lakhala ndi zotsatira zabwino “kumalekezero a dziko lapansi” kumeneku. (Machitidwe 1:8) (Onani bokosi lakuti “Anasiya Uchidakwa N’kukhala Mkhristu.”) Mu 2006, mipingo isanu ya Mboni za Yehova m’dzikoli, inatha maola 80,000 kulalikira uthenga wa m’Baibulo wonena za Paradaiso amene akubwera m’tsogolo. (Yesaya 65:17-25) N’zosangalatsa kudziwa kuti Paradaiso ameneyu akadzabwera, anthu adzapuma ku mavuto ndi nkhawa zonse za moyo uno.—Chivumbulutso 21:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 5 Ng’ombe za m’madzi zimenezi zimadya zomera ndipo ng’ombe yaikulu imodzi imatha kulemera makilogalamu 400.
^ ndime 7 Dziko la Vanuatu lisanalandire ufulu wodzilamulira mu 1980, linkatchedwa kuti New Hebrides.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 17]
ANTHU AKE NDI OSANGALALA
Mu 2006, bungwe lina la zachuma la ku Britain linachita kafukufuku m’mayiko 178 kuti lipeze dziko limene anthu ake amakhala ndi moyo wautali, wosangalala ndiponso osawononga kwambiri zachilengedwe. Bungweli linapeza kuti dziko la Vanuatu linaposa mayiko ena onsewo. Nyuzipepala ina inati: “Dziko la Vanuatu linaposa mayiko ena onse chifukwa chakuti anthu ake ndi osangalala, amakhala ndi moyo pafupifupi zaka 70 ndipo sawononga kwambiri zachilengedwe.”—Daily Post.
[Chithunzi]
Amavala chonchi
[Mawu a Chithunzi]
© Kirklandphotos.com
[Bokosi/Chithunzi patsamba 17]
ANASIYA UCHIDAKWA N’KUKHALA MKHRISTU
Willie yemwe amakhala pa chilumba cha Pentecost ankamwa kwambiri mowa wotchedwa kava kuyambira ali mwana. Mowa woledzeretsa umenewu umapangidwa kuchokera ku mizu ya mtengo wa tsabola. Tsiku lililonse usiku ankayenda dzandidzandi kupita ku nyumba atautunga mowa wa kava. Ngongole sizinkamuthera. Nthawi zambiri ankachita chiwawa ndipo ankamenyanso mkazi wake, Ida. Kenako munthu wina wa Mboni za Yehova amene ankagwira naye ntchito anam’limbikitsa kuphunzira Baibulo. Willie anayamba kuphunzira Baibulo koma mkazi wake sanagwirizane nazo. Komabe ataona kuti mwamuna wake wayamba kusiya khalidwe lake loipa, anasintha maganizo ake ndipo nayenso anayamba kuphunzira. Onse awiri anapita patsogolo kwambiri mwauzimu. Patapita nthawi, Willie anasiya uchidakwa ndi kusuta. Iye ndi mkazi wake anabatizidwa mu 1999 n’kukhala wa Mboni za Yehova.
[Mapu patsamba 15]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
NEW ZEALAND
AUSTRALIA
NYANJA YA PACIFIC
FIJI
[Chithunzi patsamba 16]
Anthu odumpha pansanja yaitali amachita masewera oopsa kwambiri amenewa n’cholinga choti nthaka ikhale ndi chonde
[Mawu a Chithunzi]
© Kirklandphotos.com
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
© Kirklandphotos.com
[Mawu a Chithunzi patsamba 15]
© Kirklandphotos.com
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
© Kirklandphotos.com