Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’zothetsa Nzeru Ndiponso Zowononga Chikhulupiriro

N’zothetsa Nzeru Ndiponso Zowononga Chikhulupiriro

N’zothetsa Nzeru Ndiponso Zowononga Chikhulupiriro

“MITEMBO inali ngundangunda paliponse, ndipo sitinadziwe n’komwe kuti nyumba yathu inali pati,” anatero bambo wina m’dziko la Sri Lanka, mudzi wawo utafafanizidwa ndi tsunami, mu December 2004. M’nkhani yonena za tsokali, mkonzi wa nkhani zachipembedzo m’nyuzipepala ina, anafotokoza kuti nthawi zina “ndimapemphera nditakwiya kwambiri.”

Anthu ambiri amaganiza kuti masoka achilengedwe ndi chilango chochokera kwa Mulungu. Bambo wina wolemba nkhani za pa Intaneti anafotokoza mphepo yamkuntho imene inachitika m’dera linalake kuti inali “chibakera cha Mulungu.” Ku United States, atsogoleri ena a zipembedzo anafotokoza kuti masoka monga mphepo yamkuntho ya Katrina ndi “mkwiyo wa Mulungu” pa “mizinda yochimwa kwambiri.” Ku Sri Lanka, magulu ena a Abuda olimbikitsa kwambiri chipembedzo chawo ananena kuti Akhristu ndiwo anachititsa tsunami ndipo izi zinangokulitsa kwambiri udani wa pakati pa zipembedzozi. Mkulu wina wa pakachisi wa Ahindu anakhulupirira kuti mulungu wotchedwa Shiva wakwiya chifukwa cha khalidwe loipa la anthu. Ponena za masoka achilengedwe, mtsogoleri wina wa chipembedzo cha Abuda ku United States anati: “Sitikudziwa chifukwa chimene zinthu zimenezi zimachitikira. Ndipo sitikudziwanso chifukwa chimene tinakhalira padziko pano.”

Mukaona zithunzi za nyumba zowonongeka, mitembo ya anthu, ndiponso za anthu othedwa nzeru, kodi nthawi zina mumadzifunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani Mulungu amalola kuti mavuto oterewa azichitika?’ Kapena mumaganiza kuti, ‘Mulungu ayenera kukhala ndi zifukwa zomveka zololera kuti zinthu zimenezi zizichitika koma kungoti sanatidziwitse zifukwazo.’ M’mitu yotsatirayi tikambirana nkhani imeneyi. Tionanso zinthu zomwe anthu angachite popewa kuvulala kwambiri ndiponso kufa kumene ngati zikuoneka kuti masoka achilengedwe atsala pang’ono kuchitika kapenanso ngakhale atachitika.

[Chithunzi patsamba 3]

Atsogoleri ambiri a zipembedzo sadziwa chifukwa chimene Mulungu amalolera kuti pazichitika masoka achilengedwe