Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizakudya Tokoma Tam’tchire

Tizakudya Tokoma Tam’tchire

Tizakudya Tokoma Tam’tchire

YOLEMBEDWA KU FINLAND

M’MAYIKO a kumpoto kwa Ulaya, monga Norway, Sweden, Denmark ndi Finland, mabanja ambiri amakonda kupita kutchire kukathyola zipatso. Mwachitsanzo, ku Finland, anthu okonda kuyenda m’tchire amapatsidwa ufulu wolowa m’tchire lililonse ngakhale litakhala la munthu wina, bola asawonongemo kanthu kapena kuyandikira kwambiri nyumba za eni. M’mayiko amenewa mulibe malamulo opereka ufulu umenewu, koma n’zololeka kutero pachikhalidwe chawo. Motero, kulikonse amatha kuthyola maluwa am’tchire, zipatso, ndiponso kuzula bowa.

M’dziko la Finland muli zipatso zam’tchire zambiri zamitundumitundu, ndipo zambiri mwa zipatsozi n’zodyedwa. Pali mitundu itatu ya zipatso za m’gulu la mabulosi zomwe zimapezeka kwambiri kumeneko.—Onani mabokosi amene ali m’nkhani ino.

Mitundu yosiyanasiyana ya zipatso zoterezi imakomanso mosiyanasiyana ndipo ndi yopatsa thanzi kwambiri. Buku lina lofotokoza za zipatso zam’tchire (lotchedwa Luonnonmarjaopas) linati: “Zipatso za m’mayiko amenewa zimene zimakhwima m’chilimwe zimakhala zokongola m’maso, zonunkhira bwino, ndiponso zimakhala ndi mavitamini ambiri.” Kudya zipatso zimenezi kumathandizanso kuti shuga ndiponso mafuta asachuluke kwambiri m’thupi. Akutinso zipatso zimenezi zimathandiza m’njira zambiri kuti munthu akhale wathanzi.

Kodi anthuwa amavutikiranji n’kukathyola zipatso kutchire? Jukka, yemwe amakonda kutero, anati: “Zimathandiza kwambiri kuti musawononge ndalama chifukwa choti zipatso zotere n’zokwera mtengo kwambiri. Ndipo mukathyola nokha zipatsozo mumadziwa kuti sizinagone.” Mkazi wake Niina anatchulaponso phindu lina lochitira zimenezi. Iye anati: “Kuthyola zipatsozi kumatipatsa mwayi wochitira zinthu pamodzi.”

Niina anapitiriza kunena kuti: “Koma ngati mwapita ndi ana, ndi bwino kuwayang’anira mosamala kuti asadye zipatso zosadziwika bwino ndiponso kuti asasowe.” M’pofunika kusamala chifukwa choti zipatso zina zakutchire n’zakupha.

Jukka ndi Niina amakonda kwambiri kupita kutchire monga amachitira anthu ambiri a m’mayiko a kumpoto kwa Ulayako. Niina ananena kuti: “Kunena zoona, kupita kutchire kumandisangalatsa. Kumakhala kwabata ndipo kumakhala mpweya wabwino kwambiri. Kupita kutchire kumanditsitsimutsa kwabasi. Ana nawonso amasangalala zedi akapita kutchire.” Jukka ndi Niina amaona kuti kutchire ndi malo abwino oti banja lawo lizichezerako n’kumasinkhasinkha.

Zipatso za m’gulu la mabulosi zimakoma kwabasi ndiponso zimakhala zopatsa thanzi kwambiri ngati mwangozithyola chakumene. Koma zipatsozi sizichedwa kuwonongeka. Kuti muzisunge bwino mpaka nyengo yadzinja, pamafunika kuzisamala bwino. Kale, anthu ankasunga zipatso zimenezi m’chipinda cha pansi pa nyumba yawo, koma masiku ano amangoziika m’filiji. Zipatso zambiri zamtundu umenewu amapangiranso jamu ndi juisi.

Mpake kuti wolemba mabuku wina wa ku Sweden, analemba m’buku lake lofotokoza zipatso zimenezi (lotchedwa Svenska Bärboken) kuti: “Mukasunga zipatso za m’nyengo yachilimwezi, ndiye kuti mukudzazifuna m’nyengo yadzinja mungathe kungozitulutsa m’mabotolo amene munazisungamo, n’kumasangalala poganizira kuti nyengo ina yachilimwe ikubweranso.” Zipatsozi zimagwiritsidwa ntchito m’njira zosiyanasiyana. Zimakoma kwambiri kuziika m’zakudya zosiyanasiyana zodya m’mawa. Nthawi zina amagwiritsanso ntchito zipatso zimenezi pokometsera zakudya zina monga masikono ndi zina zotere. Ndipo pali zakudya zosiyanasiyana zimene zimapatsa madyo kwambiri akazipaka zipatso zimenezi.

Anthu ambiri amagula zipatso zimenezi m’masitolo. Koma tangoganizirani kuti kunja kwacha bwino, ndiye muli phee kutchire, kamphepo kali yeziyezi, kwinaku mukufunafuna zipatso zimene zikuoneka kuti zapsa. Iyitu ndi njira yabwino yopezera zakudya zaulere koma zokoma kwambiri. Zimenezi zimatikumbutsa mawu a wamasalmo akuti: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”—Salmo 104:24.

[Bokosi/Zithunzi pamasamba 24, 25]

ZABULUU

Anthu ochuluka amakonda kwambiri zipatso zotsekemerazi. Nthawi zambiri zipatso zimenezi amapangira zinthu monga jamu, juisi, ndi zinthu zina zokometsera m’zakudya. Amazithiranso m’tizakudya tosiyanasiyana totafunatafuna. Zipatso zimenezi zimakoma kwambiri akangozithyola chakumene n’kuzisakaniza ndi mkaka. Koma musadzayerekeze kudya zipatso zimenezi mobisa, chifukwa choti mtundu wake wa buluu umakanirira m’kamwa ndiponso pamilomo motero mudzadziwikabe kuti mwadya zipatsozi. Zipatso zimenezi zimatchedwanso kuti zipatso zoyambitsa miseche.

[Bokosi/Zithunzi patsamba 25]

ZACHIKASU

Zipatso zimenezi zimakonda m’madambo akumidzi. Ku Finland zimakonda kupezeka chakumpoto. Zipatso zimenezi zili ndi vitamini A ndi C ndipo n’zamadzi okoma kwambiri komanso n’zopatsa thanzi. Zili ndi vitamini C wambiri kuposa malalanje. Chifukwa choti anthu amazikonda kwambiri, nthawi zina zipatsozi zimatchedwa kuti golidi wa m’madambo. N’zotsekemera kwambiri ndipo zimakometsa kwambiri totafunatafuna. Zipatsozi amapangiranso mtundu winawake wa mowa.

[Mawu a Chithunzi]

Reijo Juurinen/​Kuvaliiteri

[Bokosi/Zithunzi patsamba 25]

ZOFIIRA

Zipatso zofiira kwambirizi n’zotchuka kwambiri ku Finland ndi ku Sweden. Amapangira jamu, juisi, ndiponso zinthu zina zokometsera m’zakudya. Zipatsozi siziwonongeka msanga chifukwa choti zimakhala ndi madzi owawasa kwambiri moti zimatenga nthawi kuti munthu ayambe kuzikonda.

[Bokosi patsamba 25]

N’kantchito Ndithu

Kuthyola zipatso zam’tchirezi n’kosangalatsa koma n’kantchito ndithu. * Pasi ndi mkazi wake Tuire amakhala ku Lapland ndipo amathyola zipatso zam’tchire kuti azigulitsa ndiponso kudya. Nthawi zina akamathyola zipatsozi amavutika chifukwa cha tizilombo tosiyanasiyana touluka, monga udzudzu ndiponso tintchentche. Tuire anati: “Tizilomboti timasowetsa mtendere kwambiri. Timalowa paliponse ngakhale m’maso ndi m’kamwa.” Koma nkhani yabwino ndi yakuti mungathe kudziteteza ndithu povala zovala zoyenera ndi kudzola mafuta a fungo lothamangitsa tizilombo.

Kuyenda m’tchire n’kantchitonso pakokha makamaka ngati mukuyenda m’madambo. M’madera oterewa mungadabwe kupeza kuti malo ooneka ngati abwinobwino ndi a thope lokhalokha. Komanso, Pasi ndi Tuire ananena kuti ntchito yothyola zipatsozi ndi yotopetsa kwambiri. Msana ndi miyendo zimawawa kwambiri mukawerama kwa maola ambiri.

Komanso kupeza zipatso zimenezi nthawi zina kumavuta. Pasi anati: “Mumafunika kufufuza kwa nthawi yaitali kuti mupeze malo amene pali zipatso zambiri.” Nayenso Tuire anati: “Nthawi zambiri ntchito yofufuza zipatsoyi imatopetsa kwabasi kuposa kuthyola kwenikweniko.” Kutsuka zipatso zimene mwathyolazo n’kantchitonso pakokha.

Ena amaona kuti m’malo movutika ndi chintchito chimenechi, ndi bwino kungosiyira zipatsozi nyama zakutchire ndi mbalame. Komabe, pali anthu ena akhama kwambiri okonda kuthyola zipatsozi, monga Pasi ndi Tuire, omwe amalowabe m’tchire chaka ndi chaka ndi kuyendayenda m’madambo. Kwa iwowa kuthyola zipatso zimenezi n’kosangalatsa zedi moti ntchitoyi sadandaula nayo ngakhale pang’ono.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 25 Si zipatso zonse zam’tchire zimene zili zodyedwa. Zina n’zakupha. Musanathyole zipatsozo, yambani mwafunsa ngati zili zodyedwa.