Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Zingakhale Bwino Aliyense Atawerenga Buku Limeneli”

“Zingakhale Bwino Aliyense Atawerenga Buku Limeneli”

“Zingakhale Bwino Aliyense Atawerenga Buku Limeneli”

Munthu amene analemba mawu amenewa ankanena za buku lakuti Yandikirani kwa Yehova. Iye anapitiriza kunena kuti: “Chifukwa choti panopo chikondi cha Yehova ndachimvetsa bwino kwambiri, ndiyamba kusonyeza kwambiri chikondi kwa anthu ena.” Munthu wina amene anayamikira kwambiri bukuli anafotokoza kuti: “Ndasangalala ndi kupindula kwambiri ndi buku limeneli moti ndikuchita kusowa chonena kuti ndithokoze. . . . Nthawi iliyonse ndikamawerenga bukuli, ndimalimbikitsidwa kwambiri.”

Buku lakuti Yandikirani kwa Yehova lili ndi zigawo zinayi zimene zimafotokoza makhalidwe akuluakulu a Mulungu monga mphamvu, chilungamo, nzeru, ndi chikondi. Wowerenga wina anati: “Buku limeneli landithandiza kuona makhalidwe abwino kwambiri a Atate wanga wakumwamba. Landithandiza kuona kuti ndingathe kutsanzira makhalidwe ake ngati nditalola kuti mzimu wake woyera uzinditsogolera.”

Atawerenga mutu 26 wakuti “Mulungu ‘Wokhululukira,’” mayi wina wachitsikana wa ku Poland, dzina lake Joanna, anati: “Mfundo za m’buku limeneli ndimaziona ngati chuma chamtengo wapatali chimene chandithandiza kwambiri pamoyo wanga.”

Sitikukayika kuti nanunso muona kuti buku la masamba 320 limeneli n’lothandiza ndiponso n’lolimbikitsa. Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire buku lomwe lasonyezedwa panoli.

□ Nditumizireni munthu kuti aziphunzira nane Baibulo panyumba kwaulere.