Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Linamuthandiza Kukamba Bwino Nkhani Kusukulu

Linamuthandiza Kukamba Bwino Nkhani Kusukulu

Linamuthandiza Kukamba Bwino Nkhani Kusukulu

Sukulu ina yophunzitsa ntchito ku Germany ili ndi ophunzira ambiri ochokera kunja. Ena n’ngochokera ku France, Georgia, India, Lebanon, Poland, Russia, South Africa, Ukraine, Vietnam, ndi dziko limene kale linali Yugoslavia.

Mmodzi wa ophunzirawo analemba kuti: “Nthawi ina kusukuluko anapempha ophunzira onse kuti amene akufuna adzipereke kukamba nkhani pamaso pa sukulu yonse ndipo ineyo ndinavomera kutero. Ndinasankha mutu wakuti ‘Mayankho Othandiza a Mafunso Amene Achinyamata Amadzifunsa,’ ndipo ndinatero potsanzira buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Ophunzira anzanga anagoma kwambiri kumva nkhani ndi malangizo abwino amene ali m’bukuli.

“Nditamaliza, ophunzira anzanga anawomba m’manja kwambiri posangalala ndi nkhaniyo. Ophunzira onsewo akuchita maphunziro a zinenero zosiyanasiyana ndiponso onse amadziwa Chingelezi, motero ndinagawira mabuku 30 a Chingelezi a Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. Ndinaperekanso buku la Chijeremani kwa mphunzitsi wina.”

Kuchokera pa tsiku limeneli wophunzira ameneyu anapitiriza kukambirana nkhani za m’Baibulo ndi anzake ena pasukulupo ndipo iwo anachita nazo chidwi kwambiri. Motero anawapatsanso mabuku ena ofotokoza Baibulo m’zinenero zotsatirazi: Chiarabu, Chibengali, Chijojiya, Chipolishi, Chirasha, Chisipanishi, ndiponso Chiviyetinamu.

N’kutheka kuti mukudziwa wachinyamata winawake amene angathandizike kwambiri ndi buku la Mafunso Achichepere Akufunsa. Bukuli lili ndi mitu 39 ndipo ina mwa iyo ndi yakuti: “Kodi Ndingapange Motani Mabwenzi Enieni?,” “Bwanji Ponena za Kugonana Ukwati Usanachitike?,” ndi “Kodi Ndingadziwe Motani Ngati Chiri Chikondi Chenicheni?” Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo zitumizeni ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire buku lomwe lasonyezedwa panoli.

□ Nditumizireni munthu kuti aziphunzira nane Baibulo panyumba kwaulere.