Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Nkhani Imene Ikudetsa Nkhawa Kwambiri Makolo

Nkhani Imene Ikudetsa Nkhawa Kwambiri Makolo

Nkhani Imene Ikudetsa Nkhawa Kwambiri Makolo

BANJA la a Phiri ndi akazi awo a Zione n’losangalala, ndipo lili ndi mwana wamwamuna wa zaka zitatu yemwe ndi wochenjera ndiponso wathanzi labwino. * Banjali limasamalira bwino kwambiri mwana wawoyu, komabe kusamalira bwino mwana si kophweka masiku ano. Munthu amene ali ndi mwana amadziwiratu kuti wasenza udindo waukulu ndiponso amakhala ndi nkhawa. Izi zili choncho chifukwa pali zinthu zambiri zimene ana ayenera kuphunzitsidwa. Bambo Phiri ndi akazi awo a Zione amada nkhawa kwambiri ndi udindo wawo wina, womwe ndi kuteteza mwana wawo kuti asachitidwe zachipongwe zosiyanasiyana zokhudza kugonana. N’chifukwa chiyani amada nkhawa choncho?

A Zione anati: “Bambo anga anali chidakwa chouma mtima. Ineyo pamodzi ndi azing’ono anga ankatimenya kwambiri ndiponso ankatigwiririra.” * Anthu ambiri amavomereza kuti nkhanza zoterezi zimasokoneza kwambiri maganizo a ana kwa moyo wawo wonse. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti a Zione akufunitsitsa kuteteza mwana wawo. Nawonso a Phiri akugwirizana ndi akazi awo pankhani imeneyi.

Makolo ambiri akuda nkhawa chifuwa cha kufala kwa khalidwe logona ana. N’kutheka kuti nanunso mukuda nkhawa, komano mwina simunaonepo zimene anaona a Phiri ndi a Zione. Komabe mwamvapo nkhani zambiri zovuta kumvetsa zokhudza khalidwe limeneli. Nkhani zimenezi sizinasiye malo padziko lonse ndipo zikudetsa nkhawa kwambiri makolo.

Motero n’zosadabwitsa kuti katswiri wina wofufuza nkhani imeneyi ananena kuti ili ndi “limodzi la makhalidwe ofoola nkhongono kwambiri amene ayamba kufala kwambiri masiku ano.” Izitu n’zomvetsa chisoni kwambiri, koma n’zosadabwitsa ngakhale pang’ono kwa anthu amene amawerenga Baibulo. Mawu a Mulungu amati tikukhala mu nthawi yovuta yotchedwa “masiku otsiriza,” imene anthu ake ndi “owopsa,” “odzikonda” ndiponso “opanda chikondi chachibadwa.”—2 Timothy 3:1-5.

Khalidweli ndi lochititsa nthumanzi kwambiri, moti makolo ena amachita kuima mutu akaganizira zoti anthu aipa kwambiri n’kufika pomachita kusakasaka ana kuti agone nawo. Koma kodi vutoli n’lalikulu kwambiri moti makolo sangathane nalo? Kapena kodi pali zinthu zimene makolo angachite kuti ateteze ana awo? M’nkhani zotsatirazi tikambirana mafunso amenewa.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 2 Tasintha maina munkhani zino.

^ ndime 3 Akuluakulu ena amagona ana pofuna kukhutiritsa zilakolako zawo. Iwo kawirikawiri amachita zimene Baibulo limazitcha dama, kapena kuti por·neiʹa, zomwe zimaphatikizapo kuchita zinthu monga kuwaseweretsa maliseche, kuwagona, ndiponso kuwagona m’kamwa kapena kumatako. Zina mwa nkhanza zomwe akuluakulu amachita kwa ana ndi kuwasisita mabere, kuwanyengerera kuti achite nawo zopusa, kuwaonetsa zinthunzi zolaula, kuwaonera, ndiponso kuwaonetsa maliseche. Baibulo limaletsa zimenezi ndipo limazitcha ‘khalidwe lotayirira, lonyansa kapena ladyera.’—Agalatiya 5:19-21; Aefeso 4:19.