Nyumba ya Mphamvu Zamagetsi Iyamba Kuwala Mwauzimu
Nyumba ya Mphamvu Zamagetsi Iyamba Kuwala Mwauzimu
YOLEMBEDWA KU ITALY
▪ Kumayambiriro kwa m’ma 1900, ku Pistoia, m’dziko la Italy kunayambika chitukuko chomanga mafakitale. M’derali anamangamo njanji ya sitima zoyendera magetsi kuti azitha kutumiza kapena kutenga katundu kumalowa. Njanji yotalika makilomita 15 imeneyi anaitsegulira pa June 21, 1926, ndipo imayenda mokhotakhota kudutsa m’mapiri.
Magetsi oyendetsa sitimazo ankachokera ku nyumba ya mphamvu zamagetsi imene anaimanga chapafupi (onani chithunzi cha pamwambachi). Koma patapita nthawi sitima zambiri zinasiya kuyenda m’njanjiyi, motero mu 1965 anangoitseka. Nangano chinachitika n’chiyani ndi nyumba za m’mphepete mwa njanjiyi? Zina zinawonongeka chifukwa chosasamalidwa ndipo zina anazisandutsa malo omwerako mowa komanso malo okwerera mabasi.
Nyumba ya mphamvu zamagetsi ija anaikonzanso. Mu 1997 bungwe la Mboni za Yehova (lotchedwa San Marcello Pistoiese Association of Jehovah’s Witnesses) linagula nyumbayi n’kuisandutsa Nyumba ya Ufumu. Iyitu ndi imodzi mwa Nyumba za Ufumu zokongola kwambiri m’dera la Tuscany (onani chithunzi cha m’munsichi). Anthu a mumpingo umene umasonkhana m’nyumbayi akuchita khama ‘powala monga zounikira’ m’dera lamapirili. Akutero mwa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Afilipi 2:15; Mateyo 24:14) Inde, nyumba imene poyamba inali ya mphamvu zamagetsi tsopano ikugwiritsidwa ntchito younikira mwauzimu.—Mateyo 5:14-16; 28:19, 20.