Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira”

“Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira”

“Sonyezani Kuti Ndinu Oyamikira”

▪ Baibulo limanena mobwerezabwereza kuti olambira Mulungu azikhala oyamikira. Mwachitsanzo, lemba la Salmo 92:1 limati: “N’kokoma kuyamikira Yehova.” Nayenso mtumwi Paulo analimbikitsa kuti: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”—Akolose 3:15.

M’pomveka kuti tiziyamikira chifukwatu pulofesa Robert Emmons wa ku yunivesite ya California, mumzinda wa Davis, anati: “Zimene akatswiri ofufuza nkhani ya kuyamikira akupeza, zikusonyeza kuti mtima woyamikira umathandiza kwambiri anthu kuti asamavutike mu mtima ndi mavuto a tsiku ndi tsiku, makamaka mavuto obwera chifukwa chopanikizika ndi zochitika zosiyanasiyana pa moyo. Umathandizanso munthu kuona kuti iyeyo n’ngofunika.”

Magazini ina (yotchedwa Time) inatchulaponso ubwino wina wa mtima woyamikira. Inati: “Anthu amene amakonda kunena kuti amayamikira zakutizakuti . . . nthawi zambiri amakhala ndi thupi lamphamvu ndipo sakonda kudandaula ndi zinthu, samva kuti n’ngopanikizika chifukwa cha zochitika zosiyanasiyana pamoyo, ndipo kawirikawiri sadwala matenda ovutika maganizo.”

Komano n’zomvetsa chisoni kuti anthu ochuluka akuchita zimene Baibulo linalosera, zakuti “m’masiku otsiriza,” anthu ambiri adzakhala “odzikonda” ndiponso “osayamika.” (2 Timoteyo 3:1-5) Kodi Mkhristu woona angapewe bwanji mtima umenewu? Mlembi wa Baibulo anati: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” (Yesaya 48:17) Tikamamvera malamulo a Mulungu, timapewa mavuto ambiri amene anthu ochita zinthu mongoganizira za iwo okha amakumana nawo. Komanso Yehova amatitsimikizira kuti amaona zabwino zimene tikuchita ndipo adzatipatsa mphotho yoyenerera. (Aheberi 6:10) Tikaganizira madalitso amenewa, timalimbikitsidwa kwambiri ‘kuyamika Yehova.’—Salmo 107:8.