Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ “N’zosachita kufunsa” kuti padziko pano payamba kutentha kwambiri ndipo “n’zoonekeratu” kuti anthu ndiwo akuchititsa vutoli.—Zachokera ku bungwe la INTERGOVERNMENTAL PANEL ON CLIMATE CHANGE (IPCC), KU SWITZERLAND.
▪ Ku Germany, pakati pa anthu 1 miliyoni ndi theka kufika pa anthu pafupifupi 2 miliyoni “ali ndi chizolowezi chomwa mankhwala asakudwala.” Vutoli lakula kwambiri ngati vuto lauchidakwa.—Zachokera m’nyuzi ya TAGESSCHAU, KU GERMANY.
▪ Ku Britain, ana osakwanitsa chaka ndiwo amaphedwa kwambiri kuposa anthu amisinkhu ina.—Zachokera m’nyuzi ya THE TIMES, KU BRITAIN.
▪ Madera ena a m’malire a dziko la United States ndi Canada n’ngowirira kwambiri moti aboma “amavutika kuti aone pamene pali malirewo.” Denis Schornack, wa m’bungwe linalake loona za malire a mayikowo (lotchedwa International Boundary Commission) anati: “Simungathe kusamalira deralo ngati malire sakudziwika.”—Zachokera ku bungwe la ASSOCIATED PRESS, KU UNITED STATES.
Thupi Limadzichiza Lokha
Pulofesa Gustav Dobos, yemwe ndi dokotala wamkulu pachipatala cha pa mgodi wina mumzinda wa Essen, ku Germany anati: “Thupi la munthu linalengedwa m’njira yoti limatha kuchiza lokha matenda 60 kapena 70 pa matenda 100 alionse.” Akuti thupi limadzichiza popanga lokha mankhwala 30 kapenanso 40 ndipo limapanganso mankhwala ena othandiza kuchotsa zotupa zopezeka mu impso. Ofufuza akudziwa pang’ono chabe mmene thupi limachitira zimenezi, koma pali zambiri zimene sakuzimvetsa. Magazini ina (yotchedwa Vital) inati: “M’njira yovuta kumvetsa, thupi limatulutsa timadzi ndiponso maselo osiyanasiyana opha matenda ndipo chinthu chinanso chimene chimathandiza ndicho kuchepetsa maganizo ofooketsa.” Magaziniyo inapitiriza kunena kuti moyo wampanipani ndiponso mavuto amene munthu akukumana nawo angathe “kufooketsa mphamvu ya thupi yachitetezo, kwa miyezi yambiri.”
Kodi Ndani Akudyerera Chuma cha Padziko Pano?
Nyuzi ina ya ku London (yotchedwa Guardian) inati: “Titati tigawe anthu apadziko lonse m’magawo 100 malingana ndi chuma chawo, ndiye kuti gawo loyamba lokhalo, lomwe lili gawo la anthu olemera kwambiri, lili ndi chuma chochuluka pafupifupi theka la chuma chonse cha padziko pano.” Nyuziyo inapitiriza kuti: “Ambiri mwa ampondamatiki oterewa ndi anthu a makampani azamalonda ndiponso a za Intaneti.” Ofufuza a bungwe la UN apeza kuti pa anthu 100 alionse olemera kwambiri, 37 amakhala ku United States, 27 ku Japan, ndipo 6 ku United Kingdom. Magawo 50 pa magawo 100 aja ndiwo akuimira anthu osaukitsitsa padziko lapansi ndipo anthu onsewa pamodzi amagwiritsa ntchito gawo limodzi lokha pa magawo 100 a chuma chonse cha padziko pano. Duncan Green, yemwe ndi mkulu wa zofufuza m’bungwe lina lothandiza anthu la ku Britain (lotchedwa Oxfam) anati: “Ichi sichilungamo ngakhale pang’ono. . . . N’zosamveka kumalola kuti anthu anzathu okwana 800 miliyoni azigona ndi njala pamene enaake akudyerera chuma chadzaoneni.”
Ku China Kukubadwa Akazi Ochepa
M’chaka cha 2005, pa anyamata 118 alionse amene ankabadwa ku China pankabadwa atsikana 100 basi. Nyuzi ina (yotchedwa China Daily) inati: “M’madera ena a dzikoli mumabadwa anyamata 130 pa atsikana 100 alionse.” Chimene chachititsa zimenezi n’chakuti anthu akumachotsa mimba akakayezetsa kuchipatala n’kudziwa kuti mimbayo ndi ya mwana wamkazi. Akuluakulu aboma anati akudziwa kuti zimenezi zikuchitika chifukwa choti ku China kuli lamulo loti m’mizinda mabanja azibereka mwana mmodzi basi. Nyuziyi inati: “Pofika chaka cha 2020, chiwerengero cha amuna a msinkhu wokwatira ku China chidzaposa cha akazi ndi 30 miliyoni, ndipo zimenezi zidzasokoneza kwambiri chikhalidwe cha anthu.”