3. Nkhani Zake N’zogwirizana
Chifukwa Chake Tiyenera Kukhulupirira Baibulo
3. Nkhani Zake N’zogwirizana
Kodi mukuganiza kuti zingakhale bwanji mutapempha anthu 40 ochokera kosiyanasiyana kuti alembe buku limodzi? Anthuwo akukhala m’mayiko osiyanasiyana ndipo ena sadziwana n’komwe. Ena sakudziwa zimene anzawo alemba. Kodi mungayembekezere kuti alemba zogwirizana?
UMU ndi mmene Baibulo linalembedwera. * Linalembedwa modabwitsa kwambiri kuposa pamenepa, koma n’zochititsa chidwi kuti nkhani zake zonse n’zogwirizana.
Linalembedwa mosiyana kwambiri ndi mabuku ena. Baibulo linalembedwa kwa zaka 1,600, kuyambira mu 1513 B.C.E. mpaka cha mu 98 C.E. Ambiri a anthu pafupifupi 40 amene analilemba anakhalapo pa nthawi zosiyana kwambiri. Ankagwira ntchito zosiyanasiyana. Ena anali asodzi, ena abusa a ziweto, ena mafumu ndipo mmodzi anali dotolo.
Uthenga wake ndi umodzi. Olemba Baibulo anafotokoza mfundo yaikulu imodzi yakuti: Mulungu adzatsimikizira kuti iye ndi woyenera kulamulira anthu ndiponso adzakwaniritsa cholinga chake kudzera mu Ufumu wake wakumwamba, womwe ndi boma limene lidzalamulira dziko lonse. Mfundo yaikulu imeneyi inayamba kufotokozedwa ku Genesis, kenako m’mabuku otsatira ndipo inathera ku Chivumbulutso.—Onani nkhani yakuti: “Kodi Baibulo Limanena za Chiyani?” patsamba 19.
Ndi logwirizananso pazinthu zazing’ono. Nkhani za m’Baibulo n’zogwirizana ngakhale pazinthu zazing’ono kwambiri, koma m’nkhani zambiri n’zoonekeratu kuti olemba ake sanachite zimenezi dala. Nachi chitsanzo. Wolemba Baibulo Yohane ananena kuti, pamene khamu la anthu linabwera kudzamvetsera Yesu, Yesu anafunsa Filipo kumene angakagule mkate kuti adyetse anthuwo. (Yohane 6:1-5) Pofotokoza nkhani yomweyi, Luka ananena kuti zimenezi zinachitikira pafupi ndi mzinda wa Betsaida. Yohane asanalembe nkhani imeneyi, anali atanena kale kuti Filipo anali wa ku Betsaida. (Luka 9:10; Yohane 1:44) Choncho, Yesu anafunsa mmodzi wa anthu amene anali kudziwa bwino deralo ndipotu zimenezi ndi zomveka. Nkhani za Yohane ndi Luka n’zogwirizana koma n’zoonekeratu kuti sanachite zimenezi dala.
Kusiyana kwake n’komveka. Nkhani zina zimasiyana pang’ono, koma kodi sitingayembekezere zimenezi? Tayerekezerani kuti anthu ambiri aona zachiwawa. Ngati aliyense atafotokoza ndendende ndi zimene wina wanena, mawunso amodzimodzi, kodi simungaganize kuti achita kuuzirana? Zingakhale zomveka ngati aliyense atafotokoza nkhaniyo malinga ndi mmene waionera. Ndi mmenenso zinalili ndi olemba Baibulo.
Chitsanzo chabwino pankhaniyi n’chokhudza mtundu wa chovala cha Yesu. Kodi Yesu anavala chovala cha mtundu wapepo patsiku la kufa kwake monga mmene Yohane ananenera? (Yohane 19:2, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero) Kapena kodi chinali chofiirira, monga mmene timawerengera mu uthenga wa Mateyo ndi Maliko? (Mateyo 27:28; Maliko 15:17) Kwenikweni, zonse zikhoza kukhala zolondola. Mu mtundu wapepo mumakhalanso mtundu wofiira. Malinga ndi malo amene munthu anali komanso mmene dzuwa linali kuwalira, wina akanatha kuona chovalacho kuti ndi chofiirira, winanso kuona kuti ndi chapepo. *
Kugwirizana kwa nkhani za m’Baibulo komanso kudziwa kuti olemba ake sanachite zimenezi dala, kumasonyezanso kuti Baibulo ndi loyenera kulikhulupirira.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 4 M’Baibulo muli mabuku 66, kuyambira Genesis mpaka Chivumbulutso.
^ ndime 9 Kuti mudziwe zambiri, onani nkhani yakuti, “Kodi Baibulo Limadzitsutsa?,” m’chaputala 7 cha buku lakuti Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi chovala cha Yesu chinali chapepo kapena chofiirira?