Baibulo Ndi Umboni Wosatha wa Chikondi cha Mulungu
Baibulo Ndi Umboni Wosatha wa Chikondi cha Mulungu
ANTHU ambiri ankachita chidwi ndi zinthu zodabwitsa 7 za padziko za nthawi ya makedzana. Komabe, pa zinthu zonsezi ndi ziliza zazitali kwambiri za mafumu a ku Igupto zokha zimene zilipobe mpaka lero. Koma Baibulo, ngakhale kuti linalembedwa kalekale ndi anthu wamba komanso analilemba pa zinthu zosachedwa kuwonongeka, lidakalipobe mpaka pano ndipo nkhani zake sizinasinthidwe. Choncho, tingalikhulupirire kwambiri buku lapadera limeneli.—Yesaya 40:8; 2 Timoteyo 3:16, 17.
Yehova Mulungu akanangosiya anthu kuti aziuzana ndi pakamwa uthenga wake, uthengawo ukanasintha chifukwa anthu amatha kuiwala. Koma pofuna kuti zimenezi zisachitike, Yehova anauza anthu kuulemba m’Baibulo. Komanso, anthu amene Mulungu anauza kulemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu osavuta kumva kuti anthu ambiri, ngakhale osaphunzira kwenikweni, azitha kuliwerenga ndi kulimvetsa. (Machitidwe 4:13) Kodi umu si mmene buku lolembedwa ndi Mlengi kudzera mwa olemba ouziridwa liyenera kukhalira? Ndipotu, kupezeka paliponse kwa Baibulo ndi umboni woti Mulungu amatikonda kwambiri, kaya timakhala kuti kapena timalankhula chilankhulo chotani. (1 Yohane 4:19) Kunena zoona, ngakhale kuti Baibulo n’lofala kwambiri, sizikutanthauza kuti n’losafunika kwenikweni koma m’malo mwake ndi umboni woti n’lofunika zedi.
Umboni winanso wakuti Mulungu amatikonda ndi zimene zinalembedwa m’Baibulomo. Monga taonera mu nkhani zapitazi, Mawu a Mulungu amafotokoza mmene moyo unayambira, chifukwa chake uli waufupi ndiponso wodzala ndi mavuto, komanso mmene Mulungu adzathetsera mavuto pogwiritsa ntchito Ufumu wake. Taonanso malangizo ena abwino kwambiri a m’Baibulo a mmene tingakhalire ndi moyo wosangalatsa ngakhale panopo. (Salmo 19:7-11; Yesaya 48:17, 18) Chinthu chofunika kwambiri n’chakuti taphunzira mmene Mlengi wathu adzayeretsera dzina lake limene Satana waliipitsa ndi mabodza ake.—Mateyo 6:9.
Kodi pali buku lina limene lili ndi malangizo othandiza kwambiri ndiponso limene limapatsa anthu chiyembekezo kuposa Baibulo? Indedi, mosiyana ndi zinthu zodabwitsa 7 za padziko za nthawi ya makedzana, zomwe zambiri zinamangidwa n’cholinga cholemekeza milungu yonama kapena anthu amphamvu, Baibulo ndi umboni wosatha wakuti Yehova amakondadi anthu.
Ngati simunawerengepo Baibulo, bwanji osawerenga ndi kuliphunzira kuti mudziwe zimene limanena? Panopo, Mboni za Yehova zikuchititsa maphunziro a Baibulo aulere ndi anthu oposa 6 miliyoni padziko lonse. Iwo amaona kuti ndi mwayi wapadera kuthandiza anthu ofunitsitsa kuona okha kuti Baibulo ndi loyenera kulikhulupirira, ndiponso ndi louziridwa ndi Mulungu.— 1 Atesalonika 2:13.