Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku Lapadera

Buku Lapadera

Buku Lapadera

“Baibulo ndi buku lomwe lafalitsidwa kwambiri kuposa buku lina lililonse.”—The World Book Encyclopedia.

ZAKA zoposa 550 zapitazo, munthu wina wa ku Germany, dzina lake Johannes Gutenberg, anapanga makina oyamba osindikizira mabuku. Buku lodziwika loyamba kusindikizidwa pa makina akewo linali Baibulo. * Kuyambira nthawi imeneyo, mabuku mabiliyoni ambiri, pafupifupi onena za nkhani iliyonse, asindikizidwa. Koma Baibulo limaposa mabuku onsewo.

▪ Panopa, Mabaibulo athunthu kapena zigawo zake mwina pafupifupi 5 biliyoni asindikizidwa. Chiwerengerochi n’choposa kasanu chiwerengero cha buku la Tcheyamani Mao (Quotations From Chairman Mao), lomwe ndi buku lachiwiri kwa Baibulo pamabuku ofalitsidwa kwambiri.

▪ Posachedwapa, Mabaibulo athunthu kapena zigawo zake oposa 50 miliyoni afalitsidwa chaka chimodzi chokha. Magazini ina inati: “Chaka chilichonse, Baibulo ndi buku lomwe limagulidwa kwambiri kuposa mabuku ena.”—The New Yorker.

▪ Baibulo lathunthu kapena zigawo zake lamasuliridwa m’zilankhulo zoposa 2,400. Pa anthu 100 alionse, anthu oposa 90 akhoza kupeza Baibulo lathunthu kapena zigawo zake m’chilankhulo chawo.

▪ Pafupifupi theka la olemba Baibulo anamaliza kulemba mabuku awo asanabadwe Confucius, munthu wa ku China wodziwika kwambiri chifukwa cha nzeru zake, ndiponso asanabadwe Siddhārtha Gautama, yemwe anayambitsa Chibuda.

▪ Baibulo lakhudza kwambiri ntchito za luso moti mabuku, zojambulajambula, ndi nyimbo zina zotchuka kwambiri padziko lonse zinatengedwa mu nkhani za m’Baibulo.

▪ Baibulo laletsedwapo ndi maboma, laotchedwapo ndi anthu achipembedzo ndipo anthu ena ambiri akhala akulitsutsa. Palibe buku lina lililonse limene lakumana ndi zonsezi n’kukhalapobe.

Mfundo zimene tatchulazi n’zochititsa chidwi kwambiri. Komabe, mfundo ngati zimenezi pazokha si zokwanira kuti munthu ayambe kukhulupirira Baibulo. Choncho, tionanso zifukwa zisanu zimene zachititsa kuti anthu mamiliyoni ambiri azikhulupirira Baibulo.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 3 Baibulo la Gutenberg linali m’Chilatini, ndipo anamaliza kulisindikiza mu 1455.

[Zithunzi patsamba 4]

Makina a Gutenberg ndiponso tsamba la Baibulo lake

[Mawu a Chithunzi]

Press: Courtesy American Bible Society; page: © Image Asset Management/age fotostock