Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

FOTOKOZANI FANIZOLI

1. M’fanizo la Yesu la pa Mateyo 18:12-14, kodi nkhosa ina inatani?

․․․․․

2. Kodi ntchito ya mbusa ndi yotani?

․․․․․

3. Kodi mbusa anatani atapeza chomwe amafuna?

․․․․․

Kambiranani: Kodi Yehova amafanana bwanji ndi mbusa? Kodi inuyo mumafanana bwanji ndi nkhosa?

ZINACHITIKA LITI?

Tchulani mlembi wa buku lililonse la m’Baibulo lili pansipa, ndipo lembani mzera kuchokera pa dzina la bukulo kufika pa deti limene anamaliza kulilemba.

Chaka cha 443 B.C.E. chitapita Chisanafike chaka cha 62 C.E. Chaka cha 70 C.E. chitapita

455 B.C.E. 64 C.E.

4. Malaki

5. Yakobe

6. 2 Petulo

NDINE NDANI?

7. Yakobe analemba kuti ndine wolungama chifukwa ndinachereza azondi.

NDINE NDANI?

8. Ndinali msuwani wa Baranaba, ndipo Petulo anati ndine mwana wake.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunso awa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowekapo.

Tsamba 8 Kodi Yobu anati chiyani za dziko lapansi? (Yobu 26:․․․)

Tsamba 11 Kodi Akhristu oyambirira ankawaona bwanji Malemba? (1 Atesalonika 2:․․․)

Tsamba 12 Kodi mafumu a Isiraeli anauzidwa kulemba chiyani? (Deuteronomo 17:․․․)

Tsamba 28 Kodi Baibulo limakulangizani kuzindikira chiyani? (Aroma 12:․․․)

Zinthu Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? M’mawu anuanu, fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba 27)

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Inasochera.

2. Munthu amene amatsogolera ndi kuteteza nkhosa.

3. Anasangalala.

4. Malaki, chaka cha 443 B.C.E. chitapita.

5. Yakobe, chaka cha 62 C.E. chisanafike.

6. Petulo, 64 C.E.

7. Rahabi.—Yakobe 2:25.

8. Maliko.—Akolose 4:10; 1 Petulo 5:13.