Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Muyenera Kukhulupirira Malangizo a M’Baibulo?

Kodi Muyenera Kukhulupirira Malangizo a M’Baibulo?

Kodi Muyenera Kukhulupirira Malangizo a M’Baibulo?

‘Kodi ndikhulupirire zimene munthu ameneyu akunena?’ Anthu amafunsa funso ngati limeneli munthu akawatsatsa galimoto yakale kapena wandale akalonjeza zinthu pamsonkhano. Palibe munthu amene angafune kuwononga ndalama zake kapena nthawi yake ndi zinthu zopanda pake.

NANUNSO mwina mungafunse kuti: ‘Kodi Baibulo lili ndi phindu lililonse kwa ine? Kodi kuwerenga Baibulo si kutaya nthawi ndi mphamvu zanga pachabe?’ Yankho la mafunso amenewa limapezeka m’vesi la m’Baibulo lakuti: “Nzeru imatsimikizirika kukhala yolungama mwa ntchito zake.” (Mateyo 11:19) Indedi, “nzeru” kapena malangizo amatsimikizirika kuti ndi abwino ngati zotsatirapo zake zilinso zabwino. M’munsimu muli zimene anthu ena anena ataphunzira Baibulo. Mawu awo angakuthandizeni kuyamba kuwerenga buku lapaderali.

Mafunso Okhudza Imfa

Karen yemwe amakhala ku United States, kuyambira ali mwana, ankakhulupirira kuti anthu onse abwino amapita kumwamba akafa. Zaka zingapo zapitazo, mayi ake anamwalira ndipo chikhulupiriro chimenechi sichinamuthandize kwenikweni. Iye ankadzifunsa kuti: ‘Kodi mayi anga akuoneka bwanji panopa kumwamba kumene ali? Kodi ndidzakawapeza ali bwanji ndikadzapitako, ngati ndidzapite n’komwe? Kodi ine ndikadzafa ndidzapitanso kumwamba?’

Kenako Karen anayamba kuphunzira Baibulo mwakhama ndi Mboni za Yehova. Anaphunzira kuti anthu akufa sapita kumwamba koma amakhala ngati agona tulo. Lemba la Mlaliki 9:5 limanena kuti: “Akufa sadziwa kanthu bi.” Koma nanga kodi Karen adzaonanso mayi ake?

Iye anatonthozedwa ndipo anapatsidwa chiyembekezo ndi mawu omveka bwino a m’Baibulo awa: “Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Khristu] ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Karen anaphunzira kuti Mulungu yemwe analemba Baibulo, kudzera mwa mwana wake, adzaukitsa akufa kuti, adzakhalenso ndi moyo padziko lapansi. Karen ananena kuti, “Zimene Baibulo limanena zokhudza imfa ndi chiukiriro n’zomveka.”

Kodi Kulambira Kovomerezeka N’kuti?

Angela, mtsikana wa ku Romania, ali ndi zaka 14, mbusa wa Pentekosite anamupempherera kuti alandire mzimu woyera ndipo anayamba kulankhula m’malilime. Koma makolo ake anaona kuti zikhulupiriro za Pentekosite sizigwirizana ndi Baibulo. Banja lawo linaleka kupita ku tchalitchi ndipo linayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.

Poyamba Angela sanasangalale ndi zimenezi, koma kenako anayamba kusiyanitsa zimene zinkachitika ku tchalitchi chake ndi zimene anali kuphunzira m’Baibulo. Mwachitsanzo, anawerenga lemba la Yohane 17:3, limene limati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.” Angela anazindikira kuti anthu amafunika kudziwa kaye Mulungu kuti iye awayanje. Iye ananena kuti, “Kodi ndikanalandira bwanji mzimu wa Mulungu pomwe sindinkadziwa pafupifupi chilichonse chokhudza Mulungu?” Iye anatinso, “Ndimathokoza Yehova chifukwa chondithandiza kudzera m’Mawu ake kupeza chipembedzo choona.”

Malangizo Othandiza Anthu Kusintha

Bambo wina ku India dzina lake Gabriel, anati: “Ndinali munthu wosachedwa kupsa mtima. Munthu akandiyamba, ndinkalusa, ndinkatayataya zinthu ndiponso nthawi zina ndinkamenya kapena kutukwana anthu. Koma kuphunzira Baibulo kunandithandiza kukhala munthu woupeza mtima. Masiku ano, sindichitanso zimenezi ngakhale zinthu zivute bwanji.”

Kuti Gabriel asinthe, anawerenga malemba monga lemba la Miyambo 16:32, limene limati: “Wosakwiya msanga aposa wamphamvu; wolamulira mtima wake naposa wolanda mudzi.” Munthu winanso yemwe anali wokonda kupsa mtima, dzina lake Dhiraj, anati, “Lemba lomweli linandithandiza kuona kuti kupsa mtima ndi chizindikiro chakuti munthuwe ndi wolephera, koma kudziletsa ndi chizindikiro cha mphamvu.”

Philip wa ku South Africa anali chigawenga. Ankakonda ndewu, kuba, ndi kutukwana. Iye anamangidwapo chifukwa cha zochita zakezo. Ngakhale kuti anali ndi moyo wotere, Philip ankafunitsitsa atadziwa Mulungu. Atayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, anali ndi cholinga chotumikira Mulungu ndipo anayamba kusintha khalidwe lake. Anasiyiratu makhalidwe ake oipa ndipo analeka kuyenda ndi zigawenga. Kodi ndi malemba ati amene anamuthandiza kusintha chonchi?

Mboni za Yehova zinamuwerengera mawu a Yesu a pa Yohane 6:44, akuti: “Palibe munthu angabwere kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.” Philip anati, “Yehova anaona kanthu kenakake kabwino mwa ine ndipo anandikokera m’gulu lake labwinoli.” Philip anachita chidwi ndi malemba onena za anthu oipa amene Yehova anawachitira chifundo atalapa. Iye anati, “Malemba amenewa anandithandiza kuona kuti Yehova saumira mtima anthu opanda ungwiro akalapa.”—2 Samueli 12:1-14; Salmo 51.

Mnyamata wina wa ku Australia dzina lake Wade, ankamwa kwambiri mowa, ankagwiritsa ntchito mankhwala ozunguza bongo, anali wajuga, ndipo ankakonda kwambiri akazi. Koma anali munthu wosasangalala. Tsiku lina anacheza ndi Mboni za Yehova ndipo anavomera kuyamba kuphunzira nawo Baibulo. Kodi Wade anaphunzira chiyani?

Wade ananena kuti: “Ndinachita chidwi kwambiri ndi mmene Yesu ankaonera anthu ena. Iye ankawakomera mtima, ankawachitira chifundo, ndipo ankakonda aliyense ndi ana omwe. Kuphunzira zambiri za Yesu kunandichititsa kuti ndiyambe kutsatira kwambiri makhalidwe ake. Baibulo linandiphunzitsa kukhala mwamuna weniweni ndi kusintha khalidwe langa.” Koma nanga bwanji za zinthu zonse zoipa zimene Wade anachita? Iye ananenanso kuti: “Baibulo linandiphunzitsa kuti ngati ndilapa machimo anga onse ndi kusintha khalidwe langa, Mulungu adzandikhululukira. Ndinaphunziranso kuti nditha kudzakhala ndi moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Kenako basi, ndinapezeka kuti ndili ndi tsogolo!” (Mateyo 5:5) Wade anayeretsa moyo wake ndipo pakali pano akutumikira Yehova ndi chikumbumtima chabwino.

Zimene mwangowerengazi ndi zimene anthu ena amene anafunadi kusintha moyo wawo anena. Anafufuza m’Baibulo kuti aone ngati zimene limanena zingawathandize kulimbana ndi mavuto awo ndiponso kuyankha mafunso awo. Kutsatira malangizo a m’Baibulo kwawathandiza ndipo zimenezi zawachititsa kukhulupirira malangizo ake odalirika. Nanunso, lingakuthandizeni.

Mawu ena ouziridwa amene ananenedwa kalelo, amati: “Wodala ndi wopeza nzeru, ndi woona luntha; pakuti malonda a nzeru aposa malonda a siliva, phindu lake liposa golidi woyengeka. Mtengo wake uposa ngale; ndipo zonse zikukondweretsa sizilingana naye. Masiku ambiri ali m’dzanja lamanja lake; chuma ndi ulemu m’dzanja lake lamanzere. Njira zake zili zokondweretsa, mayendedwe ake onse ndiwo mtendere. Ndiyo mtengo wa moyo wa akuigwira; wakuiumirira n’ngodala.”—Miyambo 3:13-18.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 25]

BAIBULO LINATHANDIZA M’KAIDI

Bambo wina, dzina lake Bill, anali atangokwatira kumene ndipo anali ndi banja losangalala. Koma chaka chisanathe n’komwe, anamangidwa chifukwa cha zomwe anapalamula zaka zingapo m’mbuyomo.

Zimenezi zinamudetsa nkhawa kwambiri, koma kenako anaganiza zogwiritsa ntchito bwino nthawi yomwe akhale m’ndendemo. Iye anati, “Ndinkakonda kukhala pa kabedi kanga kuwerenga ndi kuphunzira Baibulo.” Iye ankagwiritsanso ntchito zimene ankaphunzira, chifukwa anati: “Ndinali wachifundo komanso wocheza bwino ndi akaidi anzanga, amene ankaona kuti sindinkafuna kuchita nawo zinthu zoipa. Iwo ankakonda kunena kuti: ‘Bill ali ndi zake zimene amakonda kuchita. Akufuna kuphunzira za Mulungu ndi Baibulo. Iye safuna kulimbana ndi munthu.’”

“Chifukwa chakuti akaidi ena anadziwa khalidwe langa, mikangano komanso zinthu zina zoipa sizinkandikhudza. Oyang’anira ndende anayamba kuona kuti sindikuwavutitsa. Mapeto ake, anayamba kundipatsa ntchito yosiyana ndi anzanga, choncho ndinkakhala kwandekha nthawi yaitali. Kumvera malangizo a m’Baibulo pamoyo wanga kunanditeteza kwambiri.”

Bill ankachita nawo misonkhano ya Mboni za Yehova m’ndendemo ndipo ankakonda kulalikira akaidi anzake. Anabatizidwa n’kukhala wa Mboni za Yehova m’ndende momwemo. Pokumbukira zakale, iye anati: “Ndinangowononga pafupifupi zaka 50 za moyo wanga, ndipo tsopano ndikufuna kusintha. Ndinganene motsimikiza kuti ngati mkaidi akufuna kusintha, ayenera kutsatira malangizo a m’Baibulo. Ndipo, kuti munthu adziwedi Baibulo ayenera kuphunzira ndi Mboni za Yehova. Sindinapezeponso chipembedzo china chimene chimaphunzitsa choonadi cha Baibulo kuposa Mboni za Yehova. Basi zimenezi n’zimene ndinganene.”

Pakali pano, Bill anatulutsidwa ndipo akutumikira mu mpingo wina wa Mboni za Yehova ku United States. Iye ndi mkazi wake akupitirizabe kuphunzira Mawu a Mulungu ndi kutsatira zimene amanena. Iwo amasangalala ndi mawu a pa Yesaya 48:17, 18, akuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”

[Chithunzi patsamba 23]

Karen, U.S.A.

[Chithunzi patsamba 23]

Angela, Romania

[Chithunzi patsamba 24]

Dhiraj, India

[Chithunzi patsamba 24]

Gabriel, India

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Philip ndi banja lake, South Africa

[Chithunzi patsamba 24]

Wade, Australia