Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Baibulo lonse la Dziko Latsopano likupezeka m’zinenero 43 ndipo likupezekanso m’zilembo za akhungu m’zinenero zitatu. Baibulo la Dziko Latsopano Lomasulira Malemba Achigiriki Achikhristu likupezeka mu zinenero zinanso 18 ndi m’zilembo za akhungu m’chinenero chinanso chimodzi. Pofika mu July 2007, Mabaibulo a Dziko Latsopano okwana 143,458,577 anasindikizidwa.

Chigawo chakale kwambiri cha Baibulo chimene chilipo ndi chimene chimatchedwa Madalitso a Wansembe, chomwe chili pa Numeri 6:24-26. Chinazokotedwa pa njirisi ziwiri zasiliva zooneka ngati mipukutu, zomwe zinali za chakumapeto kwa zaka za m’ma 600 kapena chakuchiyambi kwa zaka za m’ma 500 B.C.E.—Zachokera m’magazini ya BIBLICAL ARCHAEOLOGY REVIEW, U.S.A.

Pofika pa December 31, 2006, Baibulo lathunthu kapena zigawo zake linali m’zinenero 2,426, ndipo chiwerengerochi chinaposa cha chaka cha 2005 ndi zinenero 23.—Zachokera ku UNITED BIBLE SOCIETIES, BRITAIN.

Anthu a ku United States pafupifupi 28 pa 100 alionse amaona kuti Baibulo ndi “mawu enieni a Mulungu . . . omwe tingawakhulupirire,” ndipo anthu 49 pa 100 alionse amaona kuti Baibulo ndi “mawu ouziridwa ndi Mulungu koma sikuti nkhani zake zonse n’zoona,” ndiponso anthu 19 pa 100 alionse amaliona kuti ndi “buku la nthano basi.”—Zachokera ku GALLUP NEWS SERVICE, U.S.A.

Kodi Ndi Baibulo la Chitchaina Lakale Kwambiri?

“Nkhani yakale kwambiri yonena za Baibulo la Chitchaina lomasuliridwa ku Baibulo la Chiheberi inapezedwa pa mwala wosema [kumanzereku] womwe unasemedwa ndi kuimikidwa mu 781 CE,” anatero Yiyi Chen, katswiri wamaphunziro ku yunivesite ya Peking. Mwala umenewu, womwe unaimikidwa ndi Akhristu otsatira ziphunzitso za Nestorius, unapezeka m’mzinda wa Xi’an mu 1625. Chen ananenanso kuti: “Dzina la Chitchaina la mwala umenewu limamasuliridwa kuti ‘Chikumbutso cha Kufalitsa mu China Chipembedzo Chounikira chochokera ku Daqin’ (. . . mu Chitchaina, mawu akuti Daqin amatanthauza Ufumu wa Roma). Pamwalawo pali mawu ena a Chitchaina akuti ‘mabuku enieni a m’Baibulo’ ndiponso ‘kumasulira Baibulo.’”

[Mawu a Chithunzi patsamba 30]

© Réunion des Musées Nationaux/Art Resource

Anapeza Chuma M’dambo

Mu 2006, anthu amene anali kukumba m’dambo ku Ireland anapeza buku la Masalmo lolembedwa m’Chilatini, lomwe akuganiza kuti ndi la zaka za m’ma 700 C.E. Bukuli, lomwe ndi limodzi mwa mabuku ochepa kwambiri a m’nthawi imeneyo omwe alipo, limaonedwa kuti ndi chuma. Masamba ake oposa 100 achikopa adakali omangidwa pamodzi ndipo ndi apamwamba kwambiri. Nyuzipepala ina ku London inati: “Tizidutswa ta mphasa ndi tizigamba ta chikwama chachikopa tomwe anapezanso timasonyeza kuti buku la Masalmo limeneli linabisidwa dala mwina kuti lisawonongedwe ndi a Viking, omwe anaukira kumeneko zaka 1,200 zapitazo.” (The Times) Ngakhale kuti masamba ake anamatirirana ndipo anawola pang’ono, akatswiri akukhulupirira kuti angawalekanitse ndi kuwakonza.

Anapeza Zinthu Zakale Zambiri

Malipoti akuti akatswiri a zinthu zakale amene akhala akufufuza m’dothi lofukulidwa pamalo pamene kale panali kachisi wa ku Yerusalemu apeza zinthu zambiri, zina zakale kwambiri mtundu wa Isiraeli kulibe ndipo zina za m’nthawi yathu. Pazinthu zomwe anapezazo panali mutu wa muvi wofanana ndi umene ankagwiritsa ntchito asilikali a Nebukadinezara, amene anawononga kachisi woyamba wa Ayuda wa pamalopa. Chinthu chochititsa chidwi kwambiri chimene anapeza ndi chidindo chadongo cha m’ma 600 kapena m’ma 500 B.C.E, chimene amati chili ndi dzina la Chiheberi lakuti Gedalyahu Ben Immer Ha-Cohen. Gabriel Barkai, katswiri wa zinthu zakale, anati zikuoneka kuti mwini wake “anali mchimwene wa Pashur Ben Immer, yemwe Baibulo [Yeremiya 20:1] limati anali wansembe ndiponso kapitawo wamkulu mu kachisi.”