Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

ZINACHITIKIRA KUTI?

Werengani nkhani ya m’Baibulo ya pa Mateyo 2:1-16, ndi kuyankha mafunso otsatirawa.

1. Kodi poyamba nyenyeziyo inawalondolera kuti okhulupirira nyenyeziwa?

Lembani mzere wozungulira yankho lanu pa mapupo.

Yeriko

Yerusalemu

Betaniya

Betelehemu

◆ Kodi Mfumu Herode anafuna kuti okhulupirira nyenyeziwo achite chiyani?

․․․․․

◆ N’chifukwa chiyani Herode anafuna kudziwa kumene kunali Yesu?

․․․․․

Kambiranani: Kodi mukuona kusiyana kotani pakati pa nkhani ya m’Baibuloyi ndi zimene anthu amachita pa Khrisimasi?

ZINACHITIKA LITI?

Tchulani anthu amene analemba mabuku a m’Baibulo amene ali m’munsiwa, ndipo lembani mzere wolumikiza buku ndi nthawi imene mwina anamaliza kulilemba.

50 C.E. 65 C.E. 77 C.E. 96 C.E. 98 C.E.

2. 1 Yohane

3. Yuda

4. Chivumbulutso

NDINE NDANI?

5. Yohane anandiyamikira chifukwa cha kuchereza kwanga alendo ndiponso chikondi changa.

NDINE NDANI?

6. Ngakhale kuti ndine wachisanu ndi chiwiri kuchokera pa Adamu, ulosi wanga unalembedwa m’buku la Yuda.

KUCHOKERA M’MAGAZINI INO

Yankhani mafunso awa, ndipo lembani vesi kapena mavesi a m’Baibulo omwe akusowapo.

Tsamba 4 Akufa sadziwa chiyani? (Mlaliki 9:․․․)

Tsamba 8 Kodi Mulungu adzatani nayo imfa? (Yesaya 25:․․․)

Tsamba 10 Kodi Mulungu adzawatani anthu amene akuwononga dziko? (Chivumbulutso 11:․․․)

Tsamba 14 Kuti mupewe kuona zithunzi zolaula, muyenera kuphunzira kuchita chiyani? (Psalm 97:․․․)

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

(Mayankho ali pa tsamba 28)

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Yerusalemu

◆ Akapeze khandalo n’kudzamuuza.

◆ Ankafuna kuti akamuphe.

2. Mtumwi Yohane, 98 C.E. 3. Yuda, m’bale wake wa Yesu, 65 C.E. 4. Mtumwi Yohane, 96 C.E.

5. Gayo.—3 Yohane 1, 3-6.

6. Inoke.—Yuda 14.