Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Kodi Banja Lingapirire Mavuto Aakulu? (July 2006) Ndimakonda kuwerenga magazini ya Galamukani! Ndine Mkatolika, koma magazini anu amandisangalatsa ndipo ndimaphunziramo zambiri. Komabe ndafuna kuti nditchulepo kuti sindikugwirizana ndi mawu amene munanena akuti: “Mu 1983 tchalitchichi chinafewetsa malamulo ake okhudza ukwati ndipo chinachititsa kuti Akatolika asamavutike kuthetsa mabanja awo.”
G.V.M., Zambia
Yankho la “Galamukani!”: Polemba mawu amenewa tinali kunena za kusintha kwa zinthu zina ndi zina zokhudza lamulo la tchalitchi cha Katolika kumene kunachitika mu 1983. Kusintha kumeneku kwachititsa kuti zinthu zisinthe kwambiri, makamaka ku United States. Bishopu wina wa Roma Katolika, dzina lake Mark A. Pivarunas, ananena kuti ku United States maukwati 338 okha anathetsedwa kutchalitchi mu 1968. Koma pofika mu 1990 anali maukwati 62,824. N’chifukwa chiyani anawonjezeka chonchi?
Katswiri wina wodziwa malamulo a tchalitchichi, dzina lake Edward Peters, anati: “Pali zinthu zikuluzikulu zimene zasinthidwa zokhudza lamulo la tchalitchichi pa zaka 30 zapitazo. Anafewetsa kadulidwe ka chisamani chothetsera banja ndipo anafewetsanso mfundo zovomereza kuthetsadi banjalo.” Peters atanena zina mwa zimene zinasinthazo, anatchulapo kuti: “Malamulo onse amene anasinthidwa ku likulu la Akatolika achititsa kuti mabanja ambiri athe movomerezedwa ndi tchalitchi.” Zilibe kanthu kuti cholinga chosinthira malamulowo chinali chotani, koma monga Galamukani! inanenera, kusintha kumeneku kwachititsa kuti ku United States, mwinanso ngakhale m’mayiko ena: “[Tchalitchichi] chithandize Akatolika kuthetsa mabanja awo mosavuta.”
Kodi Mlengi Alipo? (September 2006) Magazini ya Galamukani! yapaderayi inali yambambande. Inali ndi mfundo zosavuta kumvetsa, zamphamvu, zotsatirika, ndiponso zogwira mtima. Ndinasangalala kwambiri ndi mmene munailembera, chifukwa magazini yonseyo inafotokoza mbali zosiyanasiyana za nkhani imodzi basi.
A. B., Spain
Zikomo kwambiri chifukwa cha magazini yolembedwa bwino kwambiri imeneyi komanso yochititsa chidwi kwabasi. Mfundo ndiponso zitsanzo zambirimbiri zimene zili m’magazini imeneyi n’zolemekeza Yehova. Yehova n’ngoyeneradi kutamandidwa.
R. B., Switzerland
Ndinakhutitsidwa ndi mfundo zake zosavuta kufotokoza zotsimikizira kuti zinthu zinachita kulengedwa. Magaziniyi inafotokoza mosanyoza kuti chiphunzitso chakuti zamoyo zinangokhalako pazokha n’chabodza ndipo inatero popereka umboni wonse umene umafunika pa sayansi kuti mutsimikizire mfundo inayake.
L. G., France
Anthu Otchedwa Aromani—Zaka 1,000 za Chimwemwe ndi Chisoni (October 2006) Anthu amenewa amandisangalatsa kwambiri. N’zomvetsa chisoni kuti mpaka pano anthu akuwasalabe. Ndikukhulupirira kuti nkhani yanuyi ithandiza anthu ambiri. N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Yehova alibe tsankho ndiponso kuti anthu a fuko limeneli ali m’gulu la anthu om’lambira.
B. B., France
Ifeyo ndife anthu a mtundu umenewu, wotchedwa Roma. Bambo anga sanakhale wa Mboni za Yehova, ndipo sakonda kwenikweni kuwerenga. Koma ataona magaziniyi ananena kuti akuifuna, ndipo tikunena pano ali nayo.
A. G., Finland