Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunde Sangapose Zimenezi Ngakhale Atatalika Motani

Mafunde Sangapose Zimenezi Ngakhale Atatalika Motani

Mafunde Sangapose Zimenezi Ngakhale Atatalika Motani

Yosimbidwa ndi Karl Heinz Schwoerer

Ndinabadwa mu 1952 ku Pittsburgh, m’boma la Pennsylvania, m’dziko la United States, koma ndinakulira mu mzinda wam’mphepete mwa nyanja wotchedwa New Smyrna Beach, ku Florida. Ndili mnyamata ndinkakonda kwambiri kuchita masewera omakwera mafunde utaima pakathabwa. Masewerawa anafika pondilowerera moti anakhala chinthu chofunika kwambiri pamoyo wanga.

MU 1970, ndinayamba sukulu yophunzira kuyendetsa ndege pa Embry-Riddle Aeronautical University ku Daytona Beach, m’boma la Florida. Koma, monga ankachitira achinyamata ambiri panthawiyi, ndinasiya sukulu chifukwa chokhumudwa kwambiri ndi nkhondo yomwe dziko lathu linkamenya ku Vietnam. Choncho ndinafika ponyansidwa kwambiri ndi zonse za m’dzikoli ndipo ndinalowerera. Ndinayamba kusunga tsitsi lambiri komanso kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo.

Posakhalitsa ndinakumana ndi Susan, yemwe anali mtsikana wokonda kupita kumalo osiyanasiyana komanso waluso lojambula zithunzi pamanja komanso ndi kamera. Nditachita masamu, ndinaona kuti ngati titamakhala moyo wosafuna zambiri, ndingathe kugwira ntchito ya zomangamanga ku Florida kwa miyezi 6 kapena 8 ndipo miyezi ina yonse tingathe kumapita m’dziko la Mexico ku Central America, n’kumakasangalala kunyanja.

Kuzindikira Zosowa Zauzimu

Kunena zoona ine ndi Susan tinkasangalala kwambiri ndi moyo wathu wosalimbana ndi zambiriwu, chifukwa tikapita kunyanja Susan ankajambula zithunzi kwinaku ine ndikusewera ndi mafunde. Koma patatha zaka zingapo, tinaona kuti moyo wathu sunali wosangalatsa. Umasoweka chinachake. Motero, cha m’katikati mwa 1975, tikukhala kunyanja ya Pacific, ku Costa Rica, ndinayamba kufunafuna zinthu zauzimu. Ndinayamba kuwerenga mabuku a zipembedzo za ku Asia ndiponso ofotokoza nzeru zosiyanasiyana, omwe anali otchuka panthawiyi.

Ambiri mwa mabukuwo ankagwira mawu Baibulo pofuna kutsimikizira kuti mfundo zawo n’zolondola. Chifukwa cha zimenezi ndinaona kuti Baibulo liyenera kuti limanena zoona. Motero ndinapeza Baibulo la King James Version, posinthanitsa ndi bowa winawake wozunguza bongo. Tsiku lililonse ndinkasewera ndi mafunde m’mawa wonse ndipo masana ndinkawerenga Baibulo. Komabe, ngakhale kuti ndinkafunitsitsa kwambiri kuphunzira Baibulo, sindinkalimvetsa kwenikweni.

“Kodi Muli ndi Mafunso Aliwonse a M’Baibulo?”

Mu August 1975, tikubwerera ku United States kuchoka ku Costa Rica, ine ndi Susan tinaima pa sitolo ina yogulitsira mankhwala ku El Salvador kuti tigule mankhwala. Chifukwa choti sitinkamvana bwinobwino ndi wogulitsayo, kasitomala wina anatithandiza pomasulira zimene tinali kunena. Iyeyu anali mtsikana wa zaka 16 wa ku America, dzina lake Jenny, ndipo ankalankhula bwinobwino Chispanya. Anatiuza kuti iyeyo ndi makolo ake ndi a Mboni za Yehova ndipo anasamukira ku El Salvador kuti adzaphunzitse anthu Baibulo.

Jenny anandifunsa kuti: “Kodi muli ndi mafunso aliwonse a m’Baibulo?”

Ndinamuyankha kuti “Inde, ndili nawo!” Ngakhale kuti sitinkaoneka bwino, iye nthawi yomweyo anatiitana kuti tipite ku nyumba kwawo kukakumana ndi makolo ake, Joe ndi Nancy Trembley. Tinavomera ndipo titafika tinayamba kuwafunsa mafunso a m’Baibulo mpaka dzuwa kulowa. Tinagoma kwambiri ndi mmene Joe ndi Nancy anali kuyankhira mafunsowo. Poyankha funso lililonse iwo ankati: “Werengani lemba lakutilakuti m’Baibulo.”

Tinangozindikira kuti kunja kwada, motero banjali linatiuza kuti tigone. Komabe iwo sanalole kuti ine ndi Susan tigone chipinda chimodzi, chifukwa tinali osakwatirana. Susan ndi Jenny sanagone msanga chifukwa anali kukambirana nkhani zambirimbiri za m’Baibulo.

Baibulo Lachikuto Chobiriwira

Tsiku lotsatira, tisananyamuke ulendo wathu, Joe ndi Nancy anatipatsa Baibulo, magazini ambirimbiri a Nsanja ya Olonda ndi a Galamukani! komanso mabuku angapo. Baibulo limene anatipatsa linali Baibulo la Dziko Latsopano, lomwe panthawiyi linali ndi chikuto chobiriwira. Joe anatitenga kuti tikaone Nyumba ya Ufumu. Sinali nyumba yapamwamba ndipo Mboni za Yehova zimaphunzirirako Baibulo. Ndinaona kuti, ‘zinali zosiyana kwambiri ndi Matchalitchi ena omwe amakhala ndi nyumba zazikulu kwadzaoneni koma saphunzitsamo mfundo zenizeni za m’Baibulo.’

Tsiku lomwelo, apolisi anatiimitsa pa rodibuloko tikulowa m’dziko la Guatemala. Vuto linali Baibulo lachikuto chobiriwira lija. Apolisiwo anadabwa chifukwa ankadziwa kuti Mboni za Yehova ndi zimene kwenikweni zimagwiritsira ntchito Baibulo limeneli. Koma ifeyo sitinkaoneka ngati Mboni za Yehova ngakhale pang’ono. Komabe, patatha mphindi zingapo apolisiwo anatilola kudutsa. Zimenezi zinatidabwitsa kwambiri chifukwa choti nthawi zambiri galimoto komanso katundu wathu, ankamufufuza, kuti aone ngati tanyamula mankhwala osokoneza bongo kapena ngati tatenga katundu wosaloleka. Chifukwa cha zimenezi Baibulo lachikuto chobiriwira lija tinayamba kuliona ngati chithumwa chathu chobweretsa mwayi.

Tinapitiriza kuwerenga Baibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo mpaka kufika pokhutitsidwa kuti tapeza choonadi chonena za Mulungu. Tikudutsa ku Mexico, ndinayamba kuganizira za milungu iwiri imene tikakhale mumzinda wa Puerto Escondido, komwe ndinkakonda kuchitirako masewera anga okwera mafunde. Nditamaliza kusangalala ndi mafunde aatali bwino a kumeneku, ndinatsimikiza kuti ndikabwerera ku Florida ndikakhala mtumiki wa Yehova.

M’milungu iwiri yotsatira yomwe ndinakhala kumeneko, ndinkangokhalira kusewera m’nyanja m’mawa uliwonse. Masana ndinkakhala m’phepete mwa nyanja n’kumawerenga Baibulo ndi mabuku ena ofotokoza Baibulo. Kamtsikana kena ka zaka 8 kanaona Baibulo lachikuto chobiriwiralo, ndipo kanalimbikira kwambiri kuti madzulo tipitire limodzi kwinakwake. Sitinamvetse kuti kamtsikanako kakufuna kupita nafe kuti, koma tinkadziwa kuti kakufuna tipite kumeneko chifukwa cha Baibulo lachikuto chobiriwira lija. Tinakana, koma kamtsikanako kankangotivutitsabe. Patatha masiku angapo tinaganiza zopita nako. Kanapita nafe ku Nyumba ya Ufumu ya Mboni za Yehova. Kanali kanyumba ka msungwi kofolera ndi udzu. Aliyense kumeneko anatipatsa moni ndipo anatikumbatira ngati kuti tinadziwana kale.

Tinagoma kwambiri ndi ulemu umene aliyense ankasonyeza. Ana ena ankangotiyang’anitsitsa, koma mwina n’chifukwa choti anali asanaonepo anthu atsitsi lachizungu lalitali choncho. Makolo awo ankangokhalira kuwaletsa n’kuwauza kuti azimvetsera msonkhanowo. Komatu chonsecho, Yehova anagwiritsira ntchito kamwana ngati ana amenewa kuti tiyambe kufika pamisonkhano.

Tinatsimikiza Kutumikira Yehova

Nditasangalala ndi mafunde kwa milungu iwiri, ndinagulitsa matabwa ochitira masewerawa, ndipo tinanyamuka ulendo ku Florida. Kumeneko tinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova komanso kupita kumisonkhano yonse yampingo. Pofunitsitsa kutumikira Yehova, tinasiya kukhalira limodzi ndi kucheza kwambiri ndi anzathu akale. Ndinameta ndevu ndi tsitsi langa, ndipo Susan anagula madiresi angapo. Patatha miyezi inayi tinakwatirana, ndipo mu April 1976, tinabatizidwa posonyeza kuti tadzipereka kutumikira Mulungu.

Tsopano tinali ndi cholinga pamoyo wathu. Poyamikira Yehova chifukwa chotipatsa madalitso amenewa, tinkafunitsitsa titabwerera ku dziko lomwe anthu ake amalankhula Chispanya, kuti tikalalikire uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Koma akulu a mumpingo wathu anatilangiza kuti: “Musapite panopo. Yambani mwalimbitsa kaye moyo wanu wauzimu kuti mukapita kumeneko mukathedi kuthandiza ena mwauzimu.” Tinamvera malangizo awowo, ndipo kuyambira nthawi imeneyo cholinga chathu chinali kukhala apainiya, dzina la atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova.

Susan anayamba upainiya mu January 1978. Inenso ndinkafuna kuchita upainiya, koma ndinali ndi ngongole yaikulu chifukwa sindinamalize kulipira ndalama ku yunivesite. Ndinaganiza nzeru yabwino yoti ndingouza boma kuti ndilibe ndalama zobwezera ngongoleyo. Potero ndikanatha kuchita upainiya.

Komabe akulu anandilangiza kuti ndisachite zimenezo, ndipo anandifotokozera kuti kuchita zimenezi n’kotsutsana ndi mfundo za m’Baibulo, zimene zimati ‘tizichita zinthu zonse moona mtima.’ (Aheberi 13:18) Motero ndinapitiriza kugwira ntchito kuti ndibweze ngongoleyo. Mu September 1979, ndinakwanitsa cholinga changa choyamba kuchita upainiya pamodzi ndi Susan. Kenako tinafewetsa kwambiri moyo wathu, moti mlungu uliwonse ndinkangogwira ntchito kwa masiku ochepa chabe kuti tizitha kupeza zofunika pamoyo wathu.

Kutumikira pa Beteli ya ku Brooklyn

Titachitira limodzi upainiya kwa chaka chathunthu, mu April 1980 tinalandira kalata yomwe sitinaiyembekezere. M’mbuyomo, analengeza kuti ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova, ku Brooklyn, mumzinda wa New York kukufunika anthu omanga, motero ifeyo tinalemba makalata ofunsira utumiki wa pa Beteli. Ndiyeno tsopano tinalandira kalata yotiitana kuti tipite pakatha masiku 30. Tinasangalala komanso tinadandaula chifukwa tinkakonda kwambiri upainiya. Posadziwa chochita, tinakambirana ndi akulu awiri za nkhaniyi ndipo akuluwo anatithandiza kuona kuti umenewu unali mwayi waukulu kwambiri. Iwo anatilangiza kuti: “Pitani ku Beteli mukayese kutumikira kwa chaka chimodzi n’kuona ngati mungakwanitse.” Choncho, tinagulitsa zinthu zathu zonse ulendo ku Brooklyn.

Nditagwira ntchito yomanga kwa zaka ziwiri, anandiuza kuti ndikagwire ntchito mu ofesi yoona zojambula mapulani (Construction Engineering Office), ndipo anandiphunzitsa ntchito yojambulayi. Kwa chaka chathunthu, Susan anagwira ntchito mu dipatimenti yomata mabuku ndipo kenaka anapita ku dipatimenti yokonza zithunzi ndiponso maonekedwe a mabuku. Chaka chilichonse pa tsiku limene tinakwatirana, tinkakhala pansi n’kukambirana mmene zinthu zayendera pamoyo wathu chaka chimenecho, n’kuonanso zolinga zathu ndipo tinaganiza zotumikirabe pa Beteli.

Pazaka zimenezo tinapeza mabwenzi ambiri apamtima. Komanso, chifukwa choti kutumikira pa Beteli kunatithandiza kutumikira Yehova ndiponso abale athu a padziko lonse, tinatsimikiza zopitirizabe utumiki wathuwo. Mu 1989 tinayamba kuphunzira Chispanya, ndipo zimenezi zinatithandiza kuti tipite ku mpingo wa Chispanya ku Brooklyn. Motero tinkaona kuti tikupha mbalame ziwiri ndi mwala umodzi, chifukwa tinkatumikira pa Beteli kwinaku n’kumatumikira mumpingo wachinenero china.

Tsiku lina Jenny, yemwe tinakumana naye pa sitolo uja, anabwera kudzationa ku Beteli, ku Brooklyn. Ndipo tinasangalala kwambiri akutiuza mmene tinakumanira ku El Salvador. Anati pa tsiku limenelo iyeyo anapita kukachititsa phunziro la Baibulo koma kenaka anayamba kuona kuti sakumva bwino m’thupi. Akubwerera kunyumba anaganiza zogula mankhwala. Ndiye m’malo mopita ku sitolo imene ankapitako nthawi zonse, iye anaganiza zopita ku sitolo kumene ifenso tinali kugulako mankhwala panthawiyo.

Kutumikira M’mayiko Ena

Tsiku lina mu 1999, m’bale amene amayang’anira dipatimenti yathu anandifunsa mosayembekezera kuti: “Kodi mungakonde kukatumikira kwa miyezi itatu ku ofesi ya nthambi ku Australia kuti mukagwire ntchito inayake ku ofesi yoona zomangamanga?”

Nthawi yomweyo ndinayankha kuti: “Inde ndingakonde.” Posakhalitsa, tinayamba ulendo wathu wopita ku Australia, komwe tinatumikirako zaka zitatu. Zinali zosangalatsa kwambiri kuthandiza nawo pa ntchito yolemba mapulani omangira nyumba zingapo za ofesi ya nthambi ku Asia ndi ku zilumba za ku South Pacific. Titabwerera ku Brooklyn mu 2003, tinalandiranso madalitso ena amene sitinkawayembekezera. Anatipempha kuti tikatumikire kunja, mu ofesi yoona zomanga Nyumba za Ufumu (Regional Kingdom Hall Office) ku ofesi ya nthambi ya Brazil, yomwe ili patali pang’ono ndi mzinda waukulu wa São Paulo.

Kuno n’kumene tili mpaka pano. Ofesi imeneyi imayang’anira ntchito yomanga Nyumba za Ufumu m’mayiko ambiri a ku South America. Zina mwa zinthu zimene ndimachita pantchito yanga ndi monga kupita ku malo osiyanasiyana kukathandiza ntchito zomanga ndi kulimbikitsa anthu amene akugwira ntchitozo, ndipo konseku ndimapita ndi mkazi wanga Susan.

Kupitiriza Kuika Zinthu Zofunika Patsogolo

Kunena zoona, ndimakondabe kusewera ndi mafunde, koma panopo ndimaona kuti ngakhale mafunde atatalika motani sangapose utumiki umene ndikuchita. Motero ndimachita masewera amenewa panthawi yake, monga masewera chabe. Ndi thandizo la chikondi la mkazi wanga Susan, nthawi yanga imathera pa ntchito yofunika kwambiri yotumikira Mulungu wathu wachikondi, Yehova.

Panopo timangoganizira zogwiritsira ntchito moyo ndiponso luso lathu kupititsa patsogolo ntchito ya Ufumu ndiponso kulambira Yehova Mulungu m’njira yoyenera. Taphunzira kuti chinthu chofunikira kwambiri si kumene tikutumikira Yehova ayi, koma kutumikira Yehovayo ndi moyo wathu wonse kulikonse kumene tingakhale.—Akolose 3:23.

[Chithunzi patsamba 25]

“Ndimakondabe kusewera ndi mafunde, koma panopo ndimaona kuti ngakhale mafunde atatalika motani sangapose utumiki umene ndikuchita”

[Chithunzi pamasamba 22, 23]

Chithunzi changa ndikusewera ndi mafunde, chomwe chinaikidwa pa mapepala oitanira anthu kuti akasangalale kunyanja panthawi ya tchuthi

[Chithunzi patsamba 23]

Ndili ndi zaka 13

[Chithunzi patsamba 23]

Ndinaona kuti moyo wanga wapanthawiyi sunali wosangalatsa

[Chithunzi patsamba 25]

Pamwamba: Ndikuthandiza kumanga Nyumba ya Ufumu Kumanja: Ndili ndi Susan panopo