Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Timaopa Imfa?

N’chifukwa Chiyani Timaopa Imfa?

N’chifukwa Chiyani Timaopa Imfa?

“Palibe chinthu choipa kuposa imfa; chifukwa imfa ndiyo mapeto a zonse.”—Anatero Aristotle.

PANALI mayi wina yemwe anzake onse ankamuona kuti ndi wokondadi kupemphera ndiponso wokhulupirira kwambiri ziphunzitso za chipembedzo chake. Ena anayamba kumutchula kuti “mzati wa tchalitchi chakecho.” Kutchalitchiko anaphunzitsidwa kuti imfa kwenikweni si mapeto a moyo, koma ndi njira yopitira ku moyo wina. Komabe mayiyu atatsala pang’ono kufa, anachita mantha kwambiri. Pofuna kutsimikizira bwinobwino zimene zimachitika munthu akafa, iye anafunsa mtsogoleri wina wa tchalitchicho kuti: “Pali [ziphunzitso zambiri zokhudza zimene zimachitika munthu akafa]; ndiye kodi munthu ungadziwe bwanji zoona zenizeni?”

Pafupifupi chipembedzo chilichonse ndiponso kulikonse kumene mungapite mungapeze kuti anthu amakhulupirira kuti munthu akafa amakhalabe ndi moyo kwinakwake, kapena adzakhalanso ndi moyo wina m’tsogolo. Kodi pa zikhulupiriro zonsezi, choona n’chiti? Anthu ambiri amakayikira zoti tidzakhalanso ndi moyo wina uliwonse m’tsogolo. Kodi inuyo mumakhulupirira chiyani? Kodi munaphunzitsidwa kuti munthu akafa amakhalabe ndi moyo kwinakwake? Kodi mumakhulupirira zimenezo? Kodi imfa mumaiopa?

Anthu Amaopa Kuti Akafa Sadzakhalakonso

Ofufuza amati kuopa imfa ndi nthenda payokha. M’zaka zapitazi palembedwa mabuku ambiri ndiponso nkhani za sayansi zofotokoza zimenezi. Komabe anthu ambiri safuna kuganizira n’komwe za imfa. Ngakhale atainyalanyaza motani, amangozindikirabe kuti yatulukira. Moyo wa munthu si wolimba ayi, moti akuti anthu oposa 160,000 amafa pafupifupi tsiku lililonse. Munthu aliyense angathe kufa nthawi ina iliyonse, ndipo zimenezi zimachititsa mantha anthu ambiri.

Akatswiri amati matenda oopa imfa ali m’magulumagulu. Magulu ake ndi monga kuopa ululu, kuopa zinthu zosadziwika, kuopa imfa ya wachibale, ndiponso kuopa kufa n’kusiya achibale ali pa mavuto adzaoneni.

Kuopa kuti mukafa simudzakhalakonso ndilo vuto lalikulu kwambiri pa magulu a matenda oopa imfawa. Kaya anthu ali m’chipembedzo chanji, amachitabe mantha akaganizira kuti imfa ndiyo mapeto a moyo. Ndipo sayansi imawonjezera mantha amenewa, chifukwatu masiku ano asayansi amatha kufotokoza ntchito zambiri zimene thupi limachita. Komatu palibe wasayansi aliyense amene anapezapo umboni wakuti m’thupi mwathumu muli chinachake chimene chimakhalabe ndi moyo ifeyo tikafa. Motero, asayansi ambiri amati imfa ndi chinthu chimene chimangochitika mwachibadwa.

N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti anthu ambiri amene amaoneka kuti amakhulupirira kwambiri zoti pali moyo wina pambuyo pa imfa, amaopanso kwambiri kufa. N’zochititsa chidwi kuti Mfumu Solomo inalemba mfundo inayake pankhani ya zimene zimachitika munthu akafa ndipo anthu ena angaone kuti mfundoyo ndi yochititsa mantha kwambiri.

Kodi Tikafa Timathera ku “Fumbi” Basi?

M’buku la Mlaliki, lomwe lakhalapo kwa zaka 3,000, Solomo analemba kuti: “Amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bi, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika. Chikondi chawo ndi mdano wawo ndi dumbo lawo lomwe zatha tsopano.” Iye anawonjezera kuti: “Chilichonse dzanja lako lichipeza kuchichita, uchichite ndi mphamvu yako; pakuti mulibe ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru, kumanda ulikupitako.”—Mlaliki 9:5, 6, 10.

Solomo anauziridwa kulemba kuti “chomwe chigwera ana a anthu chigweranso nyamazo; ngakhale chowagwera n’chimodzimodzi; monga winayo angofa momwemo zinazo zifanso . . . munthu sapambana nyama . . . onse apita ku malo amodzi; onse achokera m’fumbi ndi onse abweranso kufumbi.”—Mlaliki 3:19, 20.

Ngakhale kuti mawu amenewa analembedwa ndi Mfumu Solomo, Mulungu ndiye anawauzira ndipo ali m’Baibulo, lomwe ndi Mawu ake olembedwa. Mosiyana ndi zimene anthu ambiri amakhulupirira, malemba amenewa, pamodzi ndi malemba ena ambiri m’Baibulo, amasonyeza kuti munthu alibe chinachake chimene chimakhalabe ndi moyo munthuyo akafa. (Genesis 2:7; 3:19; Ezekieli 18:4) Motero, kodi pamenepa Mulungu akutiuza kuti mapeto a anthu ndi “fumbi,” kapena kuti kusakhalakonso? Ayi si choncho.

Baibulo siliphunzitsa kuti pali chinachake mwa munthu chimene chimakhalabe ndi moyo munthuyo akafa. Koma limapereka chiyembekezo chomveka bwino kwa anthu amene amwalira. Nkhani yotsatirayi ifotokoza zifukwa zimene simuyenera kuchitira mantha poganiza kuti imfa ndiyo mapeto a moyo wa munthu.

[Bokosi patsamba 3]

MDANI WOSATHAWIKA

Imfa imatchedwa kuti mdani wa anthu. Ndi mdanidi weniweni monga timaonera tokha tsiku lililonse. Ofufuza ena ananena kuti anthu 59 miliyoni amafa chaka chilichonse, kutanthauza kuti pafupifupi anthu awiri amafa pa sekondi iliyonse. Taonani izi:

▪ Pamasekondi 102 aliwonse pamafa munthu mmodzi chifukwa cha nkhondo.

▪ Pamasekondi 61 aliwonse munthu mmodzi amaphedwa.

▪ Pamasekondi 39 aliwonse munthu mmodzi amadzipha.

▪ Pamasekondi 26 aliwonse munthu mmodzi amafa pa ngozi yapamsewu.

▪ Pamasekondi atatu aliwonse munthu mmodzi amafa ndi njala.

▪ Pamasekondi atatu aliwonse mwana mmodzi wosakwanitsa zaka zisanu amafa.

[Bokosi patsamba 4]

AKUNGODZIVUTA

Pa November 9, 1949, munthu wina, dzina lake James Kidd, anasowa m’mapiri a ku Arizona, m’dziko la United States. Iyeyu ankagwira ntchito m’migodi ya miyala ya kopa ndipo anali ndi zaka 70. Patatha zaka zingapo khoti litanena kuti munthuyo ayenera kuti anafa, anapeza pepala limene iyeyu analembapo kagawidwe ka chuma chake chankhaninkhani. Papepalapo munthuyu analemba kuti ndalama zake zipite ku ntchito yofufuza “umboni wogwirizana ndi sayansi wosonyeza kuti thupi lili ndi mzimu umene umachoka m’thupimo kupita kwina munthuyo akafa.”

Posakhalitsa anthu oposa 100 omwe ankati ndi ofufuza ndiponso asayansi anapempha ndalamazo kuti akachite kafukufukuyo. Kwa miyezi yambiri, khoti linakambirana za omwe ayenera kupatsidwa ndalamazo ndipo panali anthu ambiri onena kuti ali ndi umboni woti munthu ali ndi mzimu umene suufa. Koma potsiriza, khoti linapereka ndalamazo ku magulu awiri odziwika bwino pankhani yofufuza zinthu. Tsopano patha zaka zoposa 50 chichitikireni zimenezi, ndipo ofufuzawo sanapezebe “umboni wogwirizana ndi sayansi wosonyeza kuti m’thupi muli mzimu umene umachokamo munthuyo akafa.”