Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusamalira Chilengedwe?

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusamalira Chilengedwe?

Zimene Baibulo Limanena

N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kusamalira Chilengedwe?

N’KUTHEKA kuti zochita za anthu panopo zikuwononga kwambiri chilengedwe padziko pano kuposa kale lonse. Popeza mavuto monga kutentha kwa dziko akukulirakulira, asayansi, mayiko, komanso makampani okhala ndi mafakitale ayamba kuchita khama kwambiri pantchito zothandiza kuchepetsa mavutowa.

Kodi ife patokhapatokha tili ndi udindo wothandiza pa ntchito yosamalira chilengedwe? Ngati tili nawo, kodi ndi udindo waukulu motani? Baibulo limatchula zifukwa zabwino kwambiri zosamalilira chilengedwe padziko pano. Limatithandizanso kuchita zinthu mosanyanyira pankhani imeneyi.

Zochita Zathu Zizigwirizana ndi Cholinga cha Mlengi Wathu

Yehova Mulungu analenga dziko lapansi kuti likhale munda wokongola woti anthu azikhalamo. Zinthu zonse zimene analenga ananena kuti “zinali zabwino” kwambiri ndipo munthu anapatsidwa ntchito ‘yolima dziko lapansi ndi kuliyang’anira.’ (Genesis 1:28, 31; 2:15) Kodi Mulungu amamva bwanji akamaona mmene dziko lilili masiku ano? N’zoonekeratu kuti Mulungu sasangalala m’pang’ono pomwe akamaona mmene anthu akuwonongera dzikoli, chifukwatu lemba la Chivumbulutso 11:18 limalosera kuti iye ‘adzawononga iwo owononga dziko lapansi.’ Motero, ifenso tizikhudzidwa tikamaona dzikoli likuwonongedwa.

Baibulo limatitsimikizira kuti zinthu zonse zimene anthu akuwononga zidzakonzedwanso Mulungu ‘akadzapanga zinthu zonse kukhala zatsopano.’ (Chivumbulutso 21:5) Komabe, tisaganize kuti palibe vuto kuwononga dziko panopo chifukwa choti Mulungu adzakonzanso zinthu zonse m’tsogolo. Ayi, maganizo amenewo n’ngolakwika. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikugwirizana ndi cholinga cha Mulungu choti dzikoli lidzakhale paradaiso?

Kuchita Zinthu Zothandiza Kuyeretsa Dziko

Pazinthu za tsiku ndi tsiku zimene anthufe timachita pamakhala zinthu zina zoyenera kutaya. Mwanzeru, Yehova anakonza dzikoli m’njira yakuti lizichotsa zinthu zoterezi, monga mu mpweya, m’madzi, ndiponso m’nthaka. (Miyambo 3:19) Motero zochita zathu zizigwirizana ndi zimene dzikoli limachita mwachilengedwe. N’chifukwa chake pamafunika kusamala kusachita dala zinthu zomwe zingawonjezere kuwononga dzikoli. Kuchita zimenezi kumasonyeza kuti timakonda anzathu monga mmene timadzikondera. (Maliko 12:31) Taganizirani chitsanzo chochititsa chidwi ichi, cha m’nthawi za m’Baibulo.

Mulungu analangiza mtundu wa Isiraeli kuti zonyansa zochoka m’thupi mwa munthu zizikwiriridwa “kunja kwa chigono.” (Deuteronomo 23:12, 13) Zimenezi zinkathandiza kuti malowo azikhala aukhondo ndiponso kuti zonyansazo ziziwolerana msanga. Masiku anonso, Akhristu oona amayesetsa kutaya zinyalala ndi zonyansa zina mwamsanga ndiponso m’njira yoyenerera. Zinthu zapoizoni zimafunika kutayidwa mosamala kwambiri.

Zinthu zambiri zofunika kutaya zingathe kugwiritsidwanso ntchito kapena kukonzedwanso kukhala zinthu zina zatsopano. Ngati malamulo a kwanuko amanena kuti zinthu zokataya ziyenera kukonzedwanso kuti zikhale zatsopano, mverani malamulowo chifukwa ndi mbali ya ‘kupereka zinthu za Kaisara kwa Kaisara.’ (Mateyo 22:21) Inde, kuchita zimenezi ndi ntchito yaikulu, koma mumasonyeza kuti mukufuna kuti dziko likhale loyera.

Kusawononga Chilengedwe

Timagwiritsira ntchito zinthu zachilengedwe kuti tipeze zimene timafunikira pamoyo wathu monga chakudya, pogona, ndiponso zinthu monga nkhuni ndi mafuta. Kagwiritsidwe ntchito kathu ka zinthu zimenezi n’kamene kamasonyeza ngati timazindikira kuti zinthu zonsezi ndi mphatso zochokera kwa Mulungu. Aisiraeli ali m’chipululu anayamba kulakalaka nyama, ndipo Yehova anawapatsa zinziri zambiri. Koma chifukwa cha dyera, iwo ankagwira zinziri zambirimbiri, moti Yehova Mulungu anapsa mtima kwambiri. (Numeri 11:31-33) Panopo sikuti Mulungu anasintha ayi. Motero, Akhristu achikumbumtima chabwino amapewa dyera mwa kuyesetsa kusagwiritsira ntchito zinthu mowononga.

Anthu ena angaganize kuti ndi ufulu wawo kugwiritsira ntchito zinthu zachilengedwe mmene akufunira. Komatu sibwino kugwiritsira ntchito zinthu zimenezi mowononga ngakhale titaona kuti n’zochuluka kapena n’zosavuta kupeza. Yesu atadyetsa chikhamu cha anthu m’njira yozizwitsa, analamula kuti asonkhanitse nsomba ndi mkate zimene zinatsala. (Yohane 6:12) Iye anachita zinthu mosamala kuti asawononge chakudya chimene Atate wake anaperekacho.

Tizichita Zinthu Mosanyanyira

Tsiku lililonse timachita zinthu zimene zingathe kuwononga chilengedwe. Motero, kodi tiyenera kupeweratu kuchita zinthu zina ndi anthu anzathu poopa kuti tingawononge chilengedwe? Baibulo sililangiza anthu kuchita zinthu monyanyira choncho. Taganizirani chitsanzo cha Yesu. Ali padziko lapansi pano, iye ankakhala monga mmene munthu wina aliyense ankakhalira, ndipo zimenezi zinamuthandiza kukwaniritsa ntchito yake yolalikira, imene Mulungu anam’patsa. (Luka 4:43) Kuphatikizanso apo, Yesu anakana kulowerera m’ndale chifukwa anadziwa kuti si njira yothetsera mavuto amene anthu anali nawo m’nthawi yake. Iye ananena momveka bwino kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.”—Yohane 18:36.

Komabe ndi bwino kuti tikamasankha zogula zathu zam’nyumba, zoyendera, komanso zinthu zosangalatsa, tiziganizira mmene zinthuzo zingakhudzire chilengedwe. Mwachitsanzo, anthu ena amasankha kugula zinthu zimene popanga kapena pozigwiritsa ntchito siziwononga kwambiri chilengedwe. Ena amayesetsa kuchepetsa kuchita zinthu zimene zimawononga kapena kusakaza chilengedwe.

Palibe chifukwa chakuti munthu aziuza anzake kuchita zinthu zimene iyeyo payekha amaona kuti n’zothandiza kwambiri pankhani yosamala chilengedwe. Anthu komanso madera osiyanasiyana angakhale ndi njira zawozawo zothandiza posamalira chilengedwe. Komabe, aliyense payekha ali ndi udindo woyesetsa kuchita zimene angathe pankhaniyi. Baibulo limati: “Aliyense ayenera kunyamula katundu wakewake.”—Agalatiya 6:5.

Mlengi anapatsa anthu udindo wosamalira dzikoli. Chifukwa choyamikira udindo umenewu ndiponso chifukwa cholemekeza Mulungu komanso zinthu zimene analenga, tiziganizira kwambiri mmene zochita zathu zingakhudzire dzikoli.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi Mulungu adzathetsa mavuto omwe ali padziko pano okhudza chilengedwe?—Chivumbulutso 11:18.

▪ Kodi Mulungu anapatsa anthu udindo wotani pankhani yosamalira dziko?—Genesis 1:28; 2:15.

▪ Kodi Yesu Khristu anapereka chitsanzo chotani pankhani yopewa kuwononga zinthu?—Yohane 6:12.