Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Amalikonda Kuposa Chidole Chilichonse

Amalikonda Kuposa Chidole Chilichonse

Amalikonda Kuposa Chidole Chilichonse

Kodi ana aang’ono angakonde buku kuposa zidole? Ee, angatero makamaka ngati makolo awo ayamba kuwawerengera bukulo akadali makanda. Izi n’zimene makolo ena omwe ndi Mebrahdtu ndi Angela, amene amakhala mu mzinda wa California ku America anachita. Iwo anayamba kumuwerengera mwana wawo buku lakuti Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso atangobadwa kumene.

Makolowo analemba kuti: “Chifukwa cha zimenezi, mwanayu amalikonda kwambiri buku la Mphunzitsi limeneli. Atatha miyezi 12 yokha, mwanayu yemwe dzina lake ndi Julianna anayamba kutiuza kuti akufuna kuti timuwerengere bukuli lomwe iye amalitchula kuti ndi la Yesu. Panopa iye ali ndi zaka zitatu ndipo tsiku lililonse amayembekezera mwachidwi nthawi yabwino kwambiri yomuwerengera bukuli. Sikuti tikungokokomeza zinthu kuti mwana wathuyu amakonda bukuli kuposa chidole chilichonse. Zithunzi ndiponso mafanizo ake n’zothandiza kwambiri pophunzitsa. Ifenso, makolo ake, timaphunziramo zambiri m’buku limeneli.”

Mukhoza kuitanitsa buku la zithunzi zokongola la masamba 256 limeneli, lomwe kukula kwa masamba ake n’kofanana ndi magazini ino. Mukhoza kuitanitsa bukuli polemba zofunika m’mizere ili m’munsiyi, ndipo tumizani ku adiresi yomwe ili pomwepoyo kapena tumizani ku adiresi yoyenera yomwe ili pa tsamba 5 la magazini ino.

❑ Ndikupempha kuti munditumizire buku limene lasonyezedwa panoli.

❑ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwa ulere.