Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu ndi Khristu Amaona Akazi Motani?

Kodi Mulungu ndi Khristu Amaona Akazi Motani?

Kodi Mulungu ndi Khristu Amaona Akazi Motani?

KODI tingatani kuti tidziwe bwinobwino mmene Yehova Mulungu amaonera akazi? Njira imodzi ndiyo kuona maganizo ndiponso zochita za Yesu Khristu, yemwe ndi “chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo,” komanso maganizo ake amasonyeza ndendende mmene Mulungu amaonera zinthu. (Akolose 1:15) Tikayang’ana mmene Yesu ankachitira zinthu ndi akazi a m’nthawi yake, timaona kuti Yehova ndi Yesu amalemekeza akazi ndipo sasangalala ndi nkhanza zimene akazi akukumana nazo m’madera ambiri masiku ano.

Mwachitsanzo, taganizirani nthawi imene Yesu analankhula ndi mayi wina pachitsime. Nkhani ya m’buku la Yohane imati: “Mayi wina wa mu Samariya anafika kudzatunga madzi. Yesu anati kwa iye: ‘Mundipatseko madzi akumwa mayi.’” Yesu analankhula poyera ndi mayi wachisamariya ngakhale kuti Ayuda ambiri sankafuna kuchita chilichonse ndi Asamariya. Buku lina linati, Ayuda ankaona kuti “kulankhula ndi mkazi poyera ndi chinthu chochititsa manyazi kwambiri.” (International Standard Bible Encyclopedia) Komano, Yesu ankalemekeza akazi ndipo ankachita zinthu mowaganizira. Analibe tsankho ndipo sankachita zinthu motengera kuti uyu ndi mkazi kapena mwamuna. Moti munthu woyamba amene Yesu anamuuza mwachindunji kuti iyeyo ndi Mesiya anali mkazi wachisamariyayo.—Yohane 4:7-9, 25, 26.

Panthawi ina, mayi wina amene anali atadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12, anafika pamene panali Yesu. Matendawa anali ochititsa manyazi komanso ofoola kwambiri. Mayiyu atakhudza Yesu, anachiriratu nthawi yomweyo. “Yesu anatembenuka, ndipo anaona mayiyo ndi kunena kuti: ‘Mwanawe, limba mtima; chikhulupiriro chako chakuchiritsa.’” (Mateyo 9:22) Malingana ndi Chilamulo cha Mose, mkazi akakhala ndi matenda otero sankayenera kukhala pagulu la anthu, ngakhalenso kuwakhudza. Ngakhale zinali choncho Yesu sananyoze mayiyu. M’malo mwake anamutonthoza n’kumulankhula mom’patsa ulemu. Zimenezi ziyenera kuti zinam’khazika mtima pansi mayiyu. Ndipotu Yesu anasangalala kwambiri kumuchiritsa.

Yesu ataukitsidwa, anaonekera koyamba kwa Mariya Mmagadala ndi wophunzira wake wina, amene Baibulo limamutcha kuti “Mariya wina.” Yesu akanafuna akanatha kuyamba kuonekera kwa Petulo, Yohane, kapena wophunzira wake wina wamwamuna. Koma iye analemekeza akazi powalola kuti akhale anthu oyamba kumuona atauka. Mngelo analangiza akaziwo kuti akauze ophunzira aamuna a Yesu za nkhani yodabwitsayi. Yesu anauza akaziwo kuti: “Pitani, kauzeni abale anga.” (Mateyo 28:1, 5-10) Apa n’zoonekeratu kuti Yesu sankachita zinthu motsatira maganizo olakwika a Ayuda ambiri apanthawiyo, omwe sankalola kuti akazi akhale mboni m’khothi.

Motero, Yesu sankaderera akazi kapena kulekerera khalidwe lowapondereza, lomwe linali lofala panthawiyo. M’malo mwake iye anasonyeza kuti akazi ankawalemekeza ndipo ankawaona kuti n’ngofunika kwambiri. Zimene Yesu ankaphunzitsa zinali zosemphana kwambiri ndi khalidwe lochitira nkhanza akazi ndipo n’zosakayikitsa ngakhale pang’ono kuti ankaona zinthu mofanana ndi Atate wake Yehova.

Mmene Mulungu Amasamalilira Akazi

Pofotokoza mmene anthu ambiri akale ankaonera akazi, buku lina lofotokoza mawu a m’Baibulo limati: “M’madera onse ozungulira nyanja ya Mediterranean kapena ku Near East munalibe dera lililonse limene akazi ankapatsidwa ufulu umene akazi amakhala nawo m’mayiko a azungu. Nthawi zambiri akazi ankangotsatira zofuna za amuna awo, monga mmene akapolo ankachitira kwa ambuye awo ndiponso ana kwa achikulire. . . . Ana aamuna ankapatsidwa ulemu kwambiri kuposa ana aakazi, ndipo nthawi zina makanda aakazi ankangosiyidwa kuti afe.” N’zoonadi, nthawi zambiri akazi ankangoonedwa ngati akapolo.

Baibulo linalembedwa panthawi imene chikhalidwe cha anthu chinali choterechi. Komabe malamulo a Mulungu opezeka m’Baibulo ankasonyeza kuti akazi n’ngofunika kulemekezedwa kwambiri, ndipotu maganizo amenewa anali osiyana kwambiri ndi maganizo a anthu ambiri panthawiyo.

Timadziwa kuti Yehova amaganizira akazi chifukwa cha zimene iye anachita nthawi zingapo pothandiza akazi amene amamulambira. Kawiri konse, iye anateteza Sara, mkazi wokongola wa Abulahamu, kuti asagwiriridwe. (Genesis 12:14-20; 20:1-7) Mulungu anakomera mtima Leya, mkazi amene Yakobo sankam’konda kwenikweni, ‘potsegula mimba yake,’ kuti abereke mwana wamwamuna. (Genesis 29:31, 32) Azamba awiri oopa Mulungu achiisiraeli anaika moyo wawo pachiswe kuti apulumutse ana aamuna achiheberi amene Aiguputo ankafuna kuwapha. Poyamikira, Yehova “anawamangitsira mabanja,” kapena kuti anawapatsa mabanja. (Eksodo 1:17, 20, 21) Anayankhanso pemphero limene Hana anapereka mochoka pansi pamtima. (1 Samueli 1:10, 20) Yehova anathandizanso mkazi wina wamasiye, yemwe mwamuna wake anali mneneri. Mkaziyo anavutitsidwa ndi wangongole amene ankafuna kungomulanda ana atalephera kubweza ngongoleyo. Mwachikondi, Yehova anapatsa mphamvu mneneri Elisa kuti achulukitse mafuta amene mkaziyo anali nawo moti anatha kubweza ngongoleyo n’kukhalanso ndi mafuta okwanira kuphikira zakudya pabanjapo. Motero mkaziyo anatha kupulumutsa banja lake ndi kudzisungira ulemu wake.—Eksodo 22:22, 23; 2 Mafumu 4:1-7.

Aneneri kawirikawiri ankatsutsa khalidwe lodyera akazi masuku pamutu kapena kuwachitira nkhanza. Moimira Yehova, mneneri Yeremiya anauza Aisiraeli kuti: “Tamvani mawu a Yehova, Inu mfumu ya Yuda, amene mukhala pa mpando wa Davide, inu, ndi atumiki anu, ndi anthu anu amene alowa pa zipata izi. Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m’dzanja la wosautsa; musachite choipa, musam’chitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.” (Yeremiya 22:2, 3) Patsogolo pake, anthu olemera ndiponso otchuka a ku Isiraeli anawadzudzula chifukwa choti ankathamangitsa akazi ndiponso ankazunza ana awo. (Mika 2:9) Mulungu wachilungamo amaona komanso amatsutsa khalidwe lozunza akazi ndi ana.

“Mkazi Wangwiro”

Wolemba buku la Miyambo anafotokoza mmene mkazi wabwino kwambiri amakhalira. Tikudziwa kuti umu ndi mmene Yehova amaonera akazi chifukwa chakuti analola kuti zimenezi zilembedwe m’Mawu Ake. Mkazi wotere saponderezedwa kapena kuonedwa ngati wapansi ayi, koma amalemekezedwa ndi kukhulupiriridwa.

“Mkazi wangwiro” wotchulidwa m’chaputala 31 cha buku la Miyambo amagwira ntchito mwakhama ndiponso modzipereka kwambiri. Amalimbikira kwambiri ‘kuchita mofunitsa ndi manja ake,’ kapena kuti kuchita zimene manja ake afuna motero amayamba mabizinesi ngakhalenso kuyendetsa nkhani zokhudza zinthu monga kupeza malo. Amaona munda n’kuugula. Amasoka zovala n’kuzigulitsa. Amapereka malamba kwa anthu amalonda. Amajijirika pakhomopo. Komanso anthu amayamikira mawu ake anzeru ndiponso chikondi chake. Motero, mwamuna wake, ana ake komanso makamaka Yehova amamuona kuti ndi wofunika kwambiri.

Sizoyenera kuti akazi aziponderezedwa ndi amuna, powadyera masuku pamutu, kapena powazunza m’njira zina. M’malo mwake mkazi wokwatiwa ayenera kukhala wosangalala ndiponso “wom’thangatira” mwamuna wakeyo.—Genesis 2:18.

Apatseni Ulemu

M’kalata yopita kwa amuna achikhristu yonena za mmene ayenera kuchitira zinthu ndi akazi awo, Petulo anauziridwa kulemba mawu olimbikitsa amuna kutsanzira maganizo a Yehova ndi Yesu Khristu. Iye analemba kuti: “Inunso amuna, pitirizani . . . kupatsa ulemu mkazi.” (1 Petulo 3:7) Kupatsa munthu ulemu kumasonyeza kuti mumaona kuti n’ngofunika kwambiri ndipo mumamulemekeza kwabasi. Motero, munthu amene amalemekeza mkazi wake sam’chititsa manyazi, kumunyozetsa, kapena kum’chitira nkhanza. M’malo mwake, iye amasonyeza mwa mawu ndi zochita zake, pagulu ngakhalenso paokha, kuti amakonda mkazi wakeyo ndi kumuchengeta.

N’zosachita kufunsa kuti kulemekeza mkazi kumathandiza kuti m’banja mukhale chimwemwe. Taonani chitsanzo cha Carlos ndi Cecilia. Panthawi ina atakwatirana, iwo ankakonda kumangokangana popanda kugwirizana pa mfundo imodzi. Nthawi zina, ankangosiyiratu kulankhulitsana. Sankadziwa kuti angathetse bwanji mavuto awo. Mwamunayo anali wovuta ndipo nayenso mkazi anali wofuna zambiri komanso wonyada. Koma atayamba kuphunzira Baibulo n’kumagwiritsira ntchito zimene anaphunzira, anaona kuti zinthu zayamba kusintha. Cecilia ananena kuti: “Ndikudziwa kuti zimene Yesu anaphunzitsa ndiponso chitsanzo chimene anapereka zasintha kwambiri moyo wanga komanso wa mwamuna wanga. Chifukwa cha chitsanzo cha Yesu, panopo ndinakhala munthu wodzichepetsa ndiponso womvetsa. Ndaphunzira kufunafuna thandizo la Yehova popemphera, monga ankachitira Yesu. Naye Carlos waphunzira kukhala munthu wololera ndiponso wodzigwira kwambiri n’kumandilemekeza monga mmene Yehova amafunira.”

Inde, sikuti banja lawo n’langwiro ayi, komabe lakhala kwa zaka zambiri. Chaposachedwapa iwowa anakumana ndi mavuto osaneneka, pamene Carlos anachotsedwa ntchito ndiponso anachitidwa opaleshoni chifukwa cha matenda a khansa. Ngakhale kuti anakumana ndi mikwingwirima yonseyi, banja lawo silinagwedezeke ngakhale pang’ono, m’malo mwake linapitirira kulimba.

Kuchokera panthawi imene anthu anachimwa n’kukhala opanda ungwiro, akazi m’madera osiyanasiyana padzikoli akhala akunyozedwa kwambiri. Akhala akuzunzidwa m’njira zosiyanasiyana monga zokhudza thupi lawo, maganizo awo, ndiponso nkhani zakugonana. Komatu izi si zimene Yehova anafuna kuti akazi azikumana nazo. Baibulo limasonyeza momveka bwino kuti akazi onse ayenera kulemekezedwa kwambiri mosaganizira za chikhalidwe cha kumene akukhalako. Mulungu ndiye anafuna zimenezi.

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Mayi wachisamariya

[Chithunzi pamasamba 4, 5]

Mkazi wodwala

[Chithunzi patsamba 4, 5]

Mariya Mmagadala

[Chithunzi patsamba 6]

Yehova anateteza Sara kawiri konse

[Chithunzi patsamba 7]

Banja la Carlos ndi Cecilia linali pangozi

[Chithunzi patsamba 7]

Carlos ndi Cecilia panopa