Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi Mungayankhe Bwanji?

Kodi pa Chithunzichi Pakusowa Chiyani?

Werengani 1 Samueli 17:38-51. Ndiyeno yang’anani pa chithunzipa. Kodi ndi zinthu zotani zomwe zikusowapo? Lembani mayankho anu pa mizere ili munsiyi, ndipo malizitsani kujambula chithunzichi mwa kuika zinthu zomwe zikusowapo.

1. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

2. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

3. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

KAMBIRANANI:

N’chifukwa chiyani Davide anatha kugonjetsa Goliati? Kodi nkhaniyi ingakulimbikitseni bwanji pokumana ndi mavuto?

Kuchokera M’magazini Ino

Yankhani mafunso awa ndipo tchulani mavesi a m’Baibulo omwe akusowa.

TSAMBA 7 Kodi n’chiyani chimene amuna ayenera kupitiriza kupatsa akazi awo? 1 Petulo 3:․․․

TSAMBA 20 Posankha masewera apakompyuta, kodi tiyenera kutsimikizira chiyani? Aefeso 5:․․․

TSAMBA 29 N’chifukwa chiyani akazi ayenera kugonjera amuna awo? 1 Akorinto 11:․․․

TSAMBA 29 Kodi amuna ayenera kupitiriza kuchita chiyani? Aefeso 5:․․․

Zithunzi Zoti Ana Apeze

Kodi mungathe kupeza zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.

Kodi Ndani Ali mu Mzere Wobadwira wa Yesu?

Werengani malembawa amene angakuthandizeni kupeza mayankho. Ndiyeno lembani mayina olondola pa mizereyo.

4. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Ndinkatchedwa mwana wa mwamuna wa Adamu, amene anabadwa “m’chifanizo chake.”

Werengani Genesis 5:3.

5. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: “Anthu anayamba kutchula dzina la Yehova” m’nthawi yanga.

Werengani Genesis 4:26.

6. ․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․․

ZOKUTHANDIZANI: Mdzukulu wanga yekha ndi amene anakhala ndi moyo wautali kundiposa.

Werengani Genesis 5:18-21, 27.

▪ Mayankho ali pa tsamba 14

MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31

1. Lupanga la Goliati.

2. Mkondo wa Goliati.

3. Choponyera miyala cha Davide.

4. Seti.—Luka 3:38.

5. Enosi.—Luka 3:38.

6. Yaredi.—Luka 3:37.