Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ “Pafupifupi mwana aliyense wa zaka 6 ku Britain amakhala ataonera TV kwa nthawi yokwana chaka chathunthu, ndipo ana oposa theka pa ana onse azaka zitatu a kumeneku ali ndi TV m’chipinda chawo.”—Inatero nyuzipepala ya THE INDEPENDENT, ku BRITAIN.
▪ Pakafukufuku wina amene anachitika ku China pakati pa anthu a zaka zoposa 16 anapeza kuti pafupifupi anthu 32 pa anthu 100 aliwonse ananena kuti ndi opembedza. Ngati chiwerengero chimenechi chikuimira anthu onse m’dzikomo ndiye kuti “anthu pafupifupi 300 miliyoni ndi opembedza . . . zomwe ndi zosiyana kwambiri ndi chiwerengero cha 100 miliyoni chodziwika ndi boma.”—Inatero nyuzipepala ya CHINA DAILY, ku CHINA.
N’zothandiza Koma Zikubweretsa Mavuto Ambiri
Zaka zingapo zapitazo, anthu andale ndiponso oteteza chilengedwe a ku Netherlands ankaganiza kuti apeza njira yabwino kwambiri yopangira mphamvu za magetsi yosawononga chilengedwe. Njira yake ndi yogwiritsa ntchito mafuta opangidwa kuchokera ku zomera monga maolivi kuti aziyendetsera majenereta. Ngakhale kuti anapeza zimenezi nyuzipepala ina (ya The New York Times) inati: “Njira imeneyi ndi yowononga kwambiri chilengedwe.” Nyuzipepalayo inapitiriza kuti: “Chifukwa choti anthu ambiri a ku Ulaya akugwiritsa ntchito kwambiri mafuta a maolivi, nkhalango zambiri za kum’mwera cha kum’mawa kwa Asia zikuwonongedwa polima minda ya maolivi ndiponso akugwiritsa ntchito kwambiri feteleza amene akuwononga nthaka.” Akamalima m’nkhalangozo, amatulutsamo madzi, n’kudulamo mitengo ndi kuiwotcha ndipo imatulutsa utsi wambiri wowononga chilengedwe. Malinga ndi nyuzipepala ija, dziko la Indonesia ndi “lachitatu pa mayiko amene amatulutsa mpweya wambiri wowononga chilengedwe ndipo asayansi akukhulupirira kuti zimenezi zikupangitsa kuti dziko lapansi lino lizitentha kwambiri.”
Nthawi ya pa “Wotchi ya Tsiku la Chiwonongeko” Yafulumizidwa
Magazini ina (ya Bulletin of Atomic Scientists) inanena kuti nthawi ya pa wotchi ya tsiku la chiwonongeko yafulumiza ndi mphindi ziwiri posonyeza kuti dziko latsala pang’ono kuwonongedwa ndi zida za nyukiliya. Zimenezi zikutanthauza kuti kwatsala mphindi zisanu kuti 12 koloko yausiku ikwane yomwe “imaimira kutha kwa dziko.” Pazaka 60 zimene wotchi imeneyi yakhalapo, anthu akhala akukokera nthawiyi maulendo 18. Nthawi ya pa wotchiyi inakokeredwa komaliza mu February 2002, malikulu azamalonda padziko lonse ku New York atawonongedwa. Chifukwa choti zida za nyukiliya zikupangidwabe ndiponso sizikuyang’aniridwa bwino, magazini ija inapitiriza kuti “chimenechi ndi chizindikiro chakuti anthu padziko lonse akulephera kuthetsa mavuto amene akubwera chifukwa cha zidazi.” Komanso inati, “mavuto obwera chifukwa cha kusintha kwa nyengo ndi oopsa kwambiri mofanana ndi zida zanyukiliya.”
Mayi Wapakati Akamada Nkhawa
Kafukufuku waposachedwapa wasonyeza kuti mayi wapakati akamada nkhawa chifukwa chokanganakangana ndi mwamuna wake kapena kumenyedwa kumene, zimakhudza kwambiri ubongo wa mwana wosabadwayo. Pulofesa Vivette Glover, wa pa Imperial College ku London anati: “Mayi wapakati akamachitiridwa nkhanza ndi mwamuna wake zimakhudza kwambiri mmene mwanayo adzakulire. Motero, zochita za bambo zimakhudza kwambiri kakulidwe ka mwana.” Iye anatinso, kaya makolowo akugwirizana kapena akukanganakangana, “thupi la mayi limatulutsa timadzi tinatake timene timakhudza kwambiri ubongo wa mwana wosabadwayo.”
Madalaivala Otayirira
Katswiri wina wa za pamsewu pa yunivesite ya Duisburg-Essen, ku Germany, dzina lake Michael Schreckenberg ananena kuti madalaivala omwe amadutsa msewu umodzimodzi tsiku lililonse nthawi zambiri saganizira n’komwe mmene akuyendera pa msewupo. Akamadutsa m’misewu yomwe akuidziwa kwambiri amatanganidwa kwambiri ndi zinthu zina m’malo moonetsetsa mmene akuyendetsera. Chifukwa cha zimenezi sazindikira msanga kuti angachite ngozi. Katswiriyu analimbikitsa madalaivala kuti azisamala kwambiri m’malo motanganidwa ndi zinthu zina.