Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amakhululuka Machimo Akuluakulu?

Kodi Mulungu Amakhululuka Machimo Akuluakulu?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Amakhululuka Machimo Akuluakulu?

CHIFUNDO ndi khalidwe limodzi lalikulu la Mulungu. (Salmo 86:15) Koma kodi chifundo cha Mulungu chimafika pati? Wamasalmo analemba kuti: “Mukasunga mphulupulu, Yehova, adzakhala chilili ndani, Ambuye? Koma kwa Inu kuli chikhululukiro, kuti akuopeni.” (Salmo 130:3, 4) Wamasalmo anatinso: “Monga kum’mawa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu. Monga atate achitira ana ake chifundo, Yehova achitira chifundo iwo akumuopa Iye. Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.”—Salmo 103:12-14.

N’zoonekeratu kuti chifundo cha Yehova n’chachikulu zedi ndipo chimakhudza zinthu zonse. Yehova amatisonyeza chifundo poganizira zomwe sitingathe kuchita ndiponso poti ndife anthu ochokera ku “fumbi.” Kuti tione kukula kwa chifundo cha Mulungu, tiyeni tiganizire zitsanzo za m’Baibulo izi.

Mtumwi Petulo anakana Khristu katatu konse. (Maliko 14:66-72) Ndipo mtumwi Paulo asanakhale wokhulupirira anazunza kwambiri otsatira Khristu, moti mmene ena a iwo ankaphedwa, Paulo anagwirizana nazo. Ndipo nthawi ina anavomereza kuti Mkhristu wina aphedwe. (Machitidwe 8:1, 3; 9:1, 2, 11; 26:10, 11; Agalatiya 1:13) Asanakhale Akhristu, anthu ena mu mpingo wa ku Korinto anali zidakwa, olanda ndipo ena anali akuba. (1 Akorinto 6:9-11) Komabe onsewa anayamba kuyanjidwa ndi Mulungu. N’chifukwa chiyani Mulungu anawakhululukira?

Zinthu Zitatu Zoyenera Kuchita Kuti Munthu Ayanjidwe ndi Mulungu

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Anandichitira chifundo chifukwa ndinali wosadziwa ndi wopanda chikhulupiriro.” (1 Timoteyo 1:13) Mawu oona amene mtumwiyu ananena akusonyeza chinthu choyamba chomwe munthu angachite kuti Mulungu amukhululukire. Chinthucho ndi kudziwa zinthu zolondola zokhudza Yehova ndi mfundo zake zimene zimapezeka m’Baibulo. (2 Timoteyo 3:16, 17) Kunena zoona, n’zosatheka kusangalatsa Mlengi wathu ngati sitikumudziwa bwino. Yesu popemphera anati: “Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekha woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munam’tuma.”—Yohane 17:3.

Anthu a mitima yabwino akamudziwa bwino Mulungu, amamva chisoni kwambiri ndi zoipa zomwe ankachita ndipo amasonyeza kuti alapadi moona mtima. Chimenechi ndi chinthu chachiwiri chimene munthu angachite kuti Mulungu amukhululukire. Lemba la Machitidwe 3:19 limati: “Chotero lapani, ndi kutembenuka kuti machimo anu afafanizidwe.”

Vesi limeneli limatchulanso kuti chinthu chachitatu chimene tingachite ndicho kutembenuka. Kutembenuka kumatanthauza kusiya khalidwe lakale n’kuyamba kutsatira mfundo za Mulungu ndiponso kuyamba kuona zinthu monga mmene iye amazionera. (Machitidwe 26:20) Mwachidule, tingati munthu amasonyeza kuti walapadi ngati wasintha khalidwe lake n’kupempha Mulungu moona mtima kuti amukhululukire.

Kukhululuka kwa Mulungu Kuli ndi Malire

Pali machimo ena amene Mulungu sakhululuka. Paulo analemba kuti: “Ngati timachita uchimo dala pambuyo podziwa choonadi molondola, sipatsalanso nsembe ina ya machimo athu. Koma pamakhala chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo. (Aheberi 10:26, 27) Mawu akuti ‘kumachita tchimo dala’ amasonyeza kuti munthuyo ali ndi mtima woipa kwambiri ndipo amachita tchimo koma safuna kulapa.

Yudasi Isikarioti anali ndi mtima woterewu. Yesu anati: “Zikanakhala bwino munthu ameneyu akanapanda kubadwa.” (Mateyo 26:24, 25) Ndipo ponena za atsogoleri ena a chipembedzo a m’nthawi yake, Yesu anati: “Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi . . . Pamene akunena bodza, amalankhula za m’mutu mwake, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.” (Yohane 8:44) Anthu amenewa anali oipa kwambiri ngati tate wawo Satana. Iwo sanamve chisoni ndi machimo omwe anachita, koma anaumitsa mitima yawo n’kupitirizabe kuchita zoipa. * N’zoona kuti nthawi zina, chifukwa cha kupanda ungwiro, Akhristu oona amatha kuchita machimo akuluakulu. Koma iwo sachita zimenezi chifukwa chokhala ndi mtima woipa kwambiri.—Agalatiya 6:1.

Anasonyeza Chifundo Mpaka Imfa

Yehova samangoona tchimolo koma amaonanso mmene wochimwayo akumvera. (Yesaya 1:16-19) Mwachitsanzo taganizirani za anthu awiri ochimwa amene anapachikidwa pamodzi ndi Yesu. Zikuoneka kuti anthu amenewa anachita machimo akuluakulu. Tikutero chifukwa chakuti mmodzi anavomereza kuti: “Ifetu tikulandiriratu zonse zotiyenera malinga ndi zimene tinachita; koma munthu uyu [Yesu] sanachite chilichonse cholakwa.” Mawu a munthu wochimwayo akusonyeza kuti ankadziwa zinazake zokhudza Yesu ndipo zimenezo ziyenera kuti zinamuthandiza kusintha khalidwe lake. Tikutero chifukwa kenako anam’pempha Yesu kuti: “Mukandikumbukire mukakalowa mu ufumu wanu.” Kodi Khristu anayankha bwanji pempho lochokera pansi pa mtimali? Iye anati: “Ndithu ndikukuuza lero, Iwe udzakhala nane m’Paradaiso.”—Luka 23:41-43.

Tangoganizani: Mawu omaliza a Yesu analinso wosonyeza chifundo munthu amene anavomera kuti anali woyenera chilango cha imfa. Zimenezi n’zolimbikitsa kwambiri, ndipo sitingakayike kuti Yesu ndiponso Atate wake, Yehova, adzachitira chifundo anthu onse amene alapa moona mtima, ngakhale kuti anachita machimo akuluakulu.—Aroma 4:7

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Onani nkhani yakuti “Kodi Mwachimwira Mzimu Woyera?” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2007, tsamba 16.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ Kodi chifundo cha Mulungu mungachifotokoze motani?—Salmo 103:12-14; 130:3, 4.

▪ Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu atiyanje?—Yohane 17:3; Machitidwe 3:19.

▪ Kodi Yesu analonjeza chiyani kwa munthu wina wochimwa?—Luka 23:43.

[Chithunzi patsamba 10]

Yesu anasonyeza kuti machimo akuluakulu angathe kukhululukidwa