Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zachiwawa Zafika Poipa Zedi?

Kodi Zachiwawa Zafika Poipa Zedi?

Kodi Zachiwawa Zafika Poipa Zedi?

▪ Mnyamata wina wosokonekera mutu anatenga mfuti n’kupha anzake pamodzi ndi aphunzitsi kusukulu.

▪ Achiwembu anaba kamtsikana n’kusiya makolo ake ali ndi nkhawa yadzaoneni.

▪ Mwana wina anapha munthu pofuna kungoona mmene zimakhalira, ndipo anzake amene anawasonyeza mtembowo anam’sungira chinsinsi kwa milungu ingapo yathunthu.

▪ Achidyamakanda amauzana zinsinsi zawo pa intaneti kuti adziwitsane mmene angakopere ana n’kuwachita zachipongwe.

IZI ndi zina chabe za nkhani zochititsa kakasi zimene zafala masiku ano. Kodi kwanuko mumatha kuyenda bwinobwino mopanda mantha, makamaka usiku? Kodi inuyo kapena wina m’banja mwanu anakumanapo ndi achifwamba kapena zoopsa zina? Anthu ambiri padziko lonse, ngakhale m’mayiko amene kale simunkaopsa, amati akukhala mwamantha kwambiri chifukwa cha zachiwawa. Taganizirani zitsanzo zochepa chabe zochokera m’mayiko osiyanasiyana.

JAPAN: Nyuzipepala ina (Asia Times) inati: “Kale, dziko la Japan linali limodzi la mayiko otetezeka kwambiri padziko lonse . . . Koma panopa, anthu amachita mantha kwambiri ndipo ambiri amangokhalira kuda nkhawa poopa zauchigawenga.”

LATIN AMERICA: Nyuzipepala ina mu 2006, inanena kuti akuluakulu ena ku Brazil akuona kuti m’tsogolo muno mumzinda wa São Paulo mukhala zipolowe zosaleletseka. M’dzikolo munachitika zipolowe kwa milungu ingapo moti pulezidenti analamula kuti asilikali ayambe kulondera m’misewu ya mumzindawo. Nyuzipepala ina (Tiempos del Mundo) inati ku Central America ndi ku Mexico kuli achinyamata pafupifupi 50,000 omwe ali m’magulu achifwamba, moti nthawi zonse akuluakulu aboma kumeneku sagona tulo. Nyuzipepalayi inapitiriza kuti: “M’chaka cha 2005 chokha, anthu pafupifupi 15,000 anaphedwa ndi magulu achifwambawa ku El Salvador, Honduras, ndi Guatemala.”

CANADA: Mu 2006, magazini ina (USA Today) inati: “Akatswiri akuda nkhawa kwambiri ndi kuchuluka kwa magulu achifwamba. Apolisi . . . anapeza kuti mumzinda wa Toronto muli magulu 73 achifwamba oyendayenda m’misewu. Magazini yomweyi inanena kuti mkulu wa apolisi ku Toronto anavomereza kuti zimenezi n’zovuta kuzithetsa.

SOUTH AFRICA: Patrick Burton, yemwe ndi katswiri wofufuza nkhani za chiwawa, ananena m’nyuzipepala ina (Financial Mail) kuti: “Achinyamata ku South Africa amangokhalira kuchita mantha poganizira zachiwawa zimene angakumane nazo.” Nyuzipepalayo inatinso iwo amaopa zinthu monga “akuba a mfuti, olanda magalimoto ndi oba m’mabanki.”

FRANCE: Anthu ambiri okhala m’nyumba zomangidwa ndi boma kapena mabungwe osiyanasiyana, tsiku lililonse amangokhala mwamantha “akafika ku nyumba n’kupeza kuti kwathyoledwa, kapena akafuna ku malo oimitsa galimoto n’kuona kuti kwaopseratu. Iwowa amachitanso mantha kwambiri akakwera basi kapena sitima usiku.”—Guardian Weekly.

UNITED STATES: Magulu achifwamba akuwonjezera zachiwawa zomwe zikuchitika. Nyuzipepala ina (The New York Times) inati m’boma lina lakumeneko, apolisi anapeza kuti pa zaka zinayi zokha m’magulu 700 a achifwambwa mwawonjezeka achinyamata 10,000 moti panopo muli anyamata ndi atsikana pafupifupi 17,000.

BRITAIN: Magazini ina ya ku London (The Times) inathirira ndemanga lipoti la bungwe la UNICEF. Magaziniyo inati: “Achinyamata ambiri ku Britain akuphedwa ndi mfuti . . . ndipo masiku ano anthu amene akupha ndiponso kuphedwa ndi mfuti ndi ana aang’ono kwambiri.” Akaidi ayamba kuchuluka kwambiri ku England ndi ku Wales, moti afika pafupifupi 80,000.

KENYA: Nyuzipepala ina inati mayi wina ndi mwana wake wamkazi anawomberedwa mu msewu winawake waukulu, atalephera kutuluka mwamsanga m’galimoto yawo yomwe mbava zimafuna kulanda. Ndipo anthu a mumzinda wa Nairobi, womwe ndi likulu la dziko la Kenya, akukumana ndi zachiwawa zambiri, monga kulandidwa galimoto, kuchitidwa zauchifwamba zosiyanasiyana ndiponso kuopsezedwa m’nyumba zawo.

Kodi zachiwawa zafika poipa zedi? Kodi n’chiyani kwenikweni chimachititsa zachiwawa zimenezi? Kodi pali zifukwa zomveka zotichititsa kuyembekezera kuti tsiku lina anthu azidzatha kukhala mwamtendere, popanda kuopa chilichonse? Nkhani zotsatirazi ziyankha bwinobwino mafunso amenewa.