Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zachiwawa Zingathetsedwe?

Kodi Zachiwawa Zingathetsedwe?

Kodi Zachiwawa Zingathetsedwe?

“Ofufuza anapeza kuti akabwerebwere ambiri amapitiriza kuvutitsa anthu akatuluka m’ndende, ndipo amawonongetsa zinthu zambiri, osati ndalama zokha.”—BUKU LA INSIDE THE CRIMINAL MIND, LOLEMBEDWA NDI DR. E. SAMENOW.

KULIKONSE padziko pano, zikuoneka kuti tsiku lililonse zachiwawa zikuwonjezeka. Motero, m’pomveka kufunsa ngati kupereka chilango chokhwima, kutsekera anthu m’ndende kwa zaka zambiri, kapenanso kupereka zilango zina zotere kukuthandizadi? Kodi ndende zimasinthadi anthu khalidwe n’kukhala abwino? Komanso funso lina lofunika kwambiri ndi lakuti, Kodi njira zimenezi n’zothandizadi kukonza chimene chimayambitsa vutoli?

Pankhani ya njira zimenezi, Dr. Stanton E. Samenow anati: “Munthu akalawa ukaidi amachangamuka kwambiri, motero amapitiriza kuchita zachiwawazo koma mosamala. N’chifukwa chake chiwerengero cha anthu odziwika amene amagwidwanso akatulutsidwa m’ndende n’chochepa chifukwa enawo sagwidwa n’komwe.” Motero tingati kwenikweni ndende zili ngati sukulu zonola luso lochitira zinthu zophwanya malamulo.—Onani bokosi lakuti “Kodi Ndende ndi Sukulu Zophunzitsa Anthu Kuphwanya malamulo?” lomwe lili pa tsamba 7.

Chinanso n’chakuti anthu ambiri ochita zinthu zotere salangidwa n’komwe, moti amaona kuti akupindula nazo. Maganizo amenewa amachititsa kuti anthuwa afike pokakala mtima ndiponso kuti asamaganizeko n’komwe zosintha. Kale, mfumu ina yanzeru inati: “Popeza sam’bwezera choipa chake posachedwa atam’tsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yawo kuchita zoipa.”—Mlaliki 8:11.

Kodi Kumakhala Kusowa Ntchito Kapena N’kungofuna?

Kodi anthu ena amachita zimenezi chifukwa choti sangachitire mwina kuti apeze zofunika pamoyo? Dr. Samenow uja anati: “Ndinapeza kuti anthu amenewa, amaona kuti imeneyi ndi njira yabwino yokhayo imene angathetsere umphawi ndiponso mavuto ena pamoyo wawo.” Koma katswiriyu atafufuza kwambiri anasintha maganizo. Iye anati: “Anthu ochita zoterezi amachita kufuna. [Munthu] amaphwanya malamulo . . . chifukwa cha mmene iyeyo akuganizira, osati chifukwa cha mmene zinthu zilili pa moyo wake ayi.” Katswiriyu anawonjezeranso kuti: “Nthawi zambiri munthu amachita zimene amaganiza. Munthu amaganiza asanachite chilichonse, akamachichita, ndiponso akamaliza kuchichita.” Motero iye sanaikire kumbuyo anthu ophwanya malamulo, koma anapeza kuti “iwowo amachita kufuna dala kuti azivutitsa anthu anzawo pamoyo wawo.” *

Pamenepa mfundo ndi yakuti anthuwa amachita “kufuna dala” kuvutitsa anzawo. Ndipotu posachedwapa nyuzipepala ina ya ku Britain inali ndi mutu wakuti: “M’malo Mopeza Ntchito Achinyamata Am’tawuni Akusankha Kukhala Mbava Kuti Alemere Msanga.” Anthu ali ndi ufulu wosankha okha zoyenera kuchita, motero angathe kuchita zabwino ngakhale atakhala kuti akukumana ndi zovuta zazikulu pamoyo wawo. Palitu anthu ambirimbiri padziko lonse amene amavutika kwambiri chifukwa cha dziko lokonderali ndiponso umphawi. Enanso amakhala m’mabanja osalongosoka koma salowerera n’kuyamba kuphwanya malamulo ayi. Dr. Samenow uja anati: “Anthu oswa malamulo amachita kufuna okha, osati chifukwa cha kumene akulira, chifukwa cholekeleredwa ndi makolo, . . . kapena chifukwa cha ulova. Zimene munthu amaganiza ndi zimene zingam’chititse zinthu zoterezi, koma osati mmene munthuyo wakulira kapena kumene munthuyo amakhala.”

Khalidwe Lochita Zachiwawa Limayambira Mumtima

Baibulo limagogomezera kwambiri mfundo yakuti mtima wa munthu ndi umene umam’chititsa zoipa, osati mmene zinthu zilili pamoyo wake. Lemba la Yakobe 1:14, 15 limati: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’chilakolako cha iye mwini. Ndiye chilakolako chikatenga pathupi, chimabala tchimo; nalonso tchimo likakwaniritsidwa, limabweretsa imfa.” Munthu akamaganizira zinthu zoipa, amayambanso kulakalaka zinthu zoipa. Mapeto ake munthu uja angathenso kuchita zinthu zoipa. Mwachitsanzo, munthu akamaona zithunzi zolaula mwa apo ndi apo angathe kufika pomalakalaka kwambiri kuchita zachiwerewere moti mapeto ake angathe kufika powachita ena zachipongwe, mwina powagwiririra.

Chinanso chofunika kuchiganizira n’chakuti masiku ano anthu amangoganizira za iwowo, za ndalama, zosangalala, ndiponso zalero lokha basi. Ponena za nthawi inoyo, Baibulo linati: “M’masiku otsiriza . . . , anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . owopsa, osakonda zabwino, [ndiponso] okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.” (2 Timoteyo 3:1-5) N’zomvetsa chisoni kuti dzikoli limalimbikitsa makhalidwe amenewa kudzera m’mafilimu, masewera a pakompyuta, mabuku, ndiponso anthu otchuka a khalidwe loipa. Zimenezi zimangowonjezera zachiwawa zimene zikuchitika. * Komano aliyense payekha angathe kusankha kusatsatira zoipazi. Ndipotu pali anthu ena amene ankachita zinthu zophwanya malamulo amene panopo anasintha kwambiri.

Anthu Amasintha

Sikuti munthu yemwe wakhala akuchita zophwanya malamulo angalephere kusintha ayi. Buku lina (Inside the Criminal Mind) linanena kuti munthu amachita kusankha yekha kuti azichita zophwanya malamulo motero “angathenso kusankha kusiya khalidweli n’kukhala munthu wolongosoka.”

Pali umboni wosonyeza kuti anthu osiyanasiyana amene kale ankachita zinthu zophwanya malamulo angasinthe. * Chofunika n’chakuti munthu azikhala wofunitsitsa kusintha khalidwe lake, zolinga zake, ndiponso zimene amaganiza kuti zigwirizane ndi mfundo zosasintha za Mlengi wathu. Ndipotu, iye amatidziwa bwino kwambiri kuposa mmene timadzidziwira tokha. Kuwonjezera pamenepa, Mulungu ali ndi ufulu wotiuza zimene zili zabwino ndi zimene sizabwino. N’chifukwa chake anauzira anthu pafupifupi 40 kuti alembe Baibulo Loyera. Buku lodabwitsali limatipatsa malangizo otithandiza kukhala osangalala ndiponso kukhala ndi cholinga pamoyo.—2 Timoteyo 3:16, 17.

N’zoona kuti sizophweka kuti munthu asinthe n’kuyamba kukondweretsa Mulungu, chifukwa tili ndi chibadwa chochita zoipa. Ndipotu, munthu wina yemwe analemba nawo Baibulo anayerekezera zimenezi ndi ‘nkhondo.’ (Aroma 7:21-25) Iye anapambana nkhondoyo osati chifukwa chodzidalira yekha, koma chifukwa ankadalira Mulungu amene Mawu ake ouziridwa “ndi amoyo ndi amphamvu.”—Aheberi 4:12.

Chakudya Chabwino Chimapatsa Mphamvu

Kuti thupi likhale lathanzi, pamafunika chakudya chabwino. Chakudyacho chimafunika kutafunidwa bwino n’kugayidwa. Zonsezi zimafunika nthawi ndi khama. Izi n’zimenenso timafunikira kuti tikhale athanzi mwauzimu. Timafunika “kutafuna” mawu a Mulungu kuti agayike n’kusanduka chakudya chopindulitsa maganizo ndi mtima wathu. (Mateyo 4:4) Baibulo limati: “Zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambiri, zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse za chikondi, zilizonse zoneneredwa zabwino, khalidwe labwino lililonse, ndi chilichonse chotamandika, pitirizani kuganizira zimenezi . . . , ndipo Mulungu wa mtendere adzakhala nanu.”—Afilipi 4:8, 9.

Onani kuti lembali likuti tiyenera ‘kupitiriza kuganizira’ mawu a Mulungu ngati tikufuna kuti tisinthe makhalidwe athu akale. Pamafunika kuleza mtima, chifukwatu munthu sakula mwauzimu lero ndi lero.—Akolose 1:9, 10; 3:8-10.

Taganizirani chitsanzo cha mkazi wina amene ankagwiriridwa ali kamwana. Atasinkhuka anayamba kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo, kumwa mowa mwauchidakwa, ndiponso kusuta. Iyeyu analamulidwa kukhala m’ndende kwa moyo wake wonse chifukwa cha milandu yambirimbiri imene anapalamula. Kundendeko anayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova ndipo anayamba kutsatira zimene ankaphunzira. Kodi atatero chinachitika n’chiyani? Pang’onopang’ono anayamba kusintha n’kuyamba kukhala ndi khalidwe langati la Khristu. Tikunena pano iyeyu salinso mu ukapolo chifukwa cha maganizo osokoneza ndiponso makhalidwe oipa. Limodzi mwa malemba amene amakonda kwambiri ndi lemba la 2 Akorinto 3:17, lomwe limati: “Tsopano, Yehova ndiye mzimu; ndipo pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.” Inde, ngakhale kuti iyeyu ali m’ndende, amasangalala kwambiri chifukwa ali ndi ufulu umene sanakhalepo nawo n’kale lonse.

Mulungu Ndi Wachifundo

Yehova Mulungu saona kuti pali munthu aliyense amene sangasinthe zivute zitani. * Mwana wa Mulungu, Yesu Khristu, anati: “Ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa kuti alape.” (Luka 5:32) N’zoona kuti n’zovuta kusintha khalidwe n’kuyamba kutsatira mfundo za m’Baibulo. Koma zimatheka ndithu munthuyo akaleza mtima n’kulola kuthandizidwa ndi Mulungu, komanso Akhristu okonda zinthu zauzimu. (Luka 11:9-13; Agalatiya 5:22, 23) Pofuna kuthandiza anthu otere, padziko lonse Mboni za Yehova kawirikawiri zimakachititsa maphunziro a Baibulo ku ndende ndi amuna komanso akazi amene akufuna kusintha, omwe anamangidwa chifukwa chopalamula milandu yosiyanasiyana. * Mlungu ndi mlungu a Mboni amachititsanso misonkhano yachikhristu m’ndende zambiri.—Aheberi 10:24, 25.

Ngakhale kuti anthu ena omwe kale ankachita zoipa anasiya njira zawozo n’kukhala Akhristu oona, Baibulo limanena mosabisa kuti masiku ano pali “kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo.” (Mateyo 24:12) Monga tionere m’nkhani yotsatirayi, ulosi umenewu ndi mbali ya ulosi waukulu womwenso uli ndi nkhani yabwino kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 7 Anthu ena amachita zachiwawa chifukwa chosokonekera mutu, makamaka m’mayiko amene anthu osokonekera mitu amaloledwa kuyenda okha m’misewu komanso amatha kukhala ndi zida. Iyi ndi nkhani yovuta, koma cholinga cha nkhani ino si kufotokoza zimenezi.

^ ndime 11 Kuti mumve zambiri pankhani imeneyi, onani nkhani yakuti “Dziko Lopanda Upandu—Lidzakhalako Liti? mu Galamukani! ya March 8, 1998, tsamba 3 mpaka 9 ndiponso yakuti “Kodi Makwalala Athu Adzakhalapo Opanda Upandu?” mu Galamukani! ya June 8, 1986.

^ ndime 14 Magazini ino ndiponso inzake ya Nsanja ya Olonda, yakhala ikutchula za anthu amene kale ankachita zosokoneza koma anasintha chifukwa chophunzira choonadi cha m’Baibulo. Onani Galamukani! ya July 2006, tsamba 11 mpaka tsamba 13; ya October 8, 2005, tsamba 20 ndi 21, ndi Nsanja ya Olonda ya January 1, 2000, tsamba 4 ndi 5; ya October 15, 1998, tsamba 27 mpaka tsamba 29; ndiponso ya February 15, 1997, tsamba 21 mpaka 24.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Anthu Ambiri Amene Akuvutika ndi Umphawi Sayamba Umbava Kapena Makhalidwe Ena Otere

[Bokosi/Chithunzi pamasamba 6, 7]

“KUBWERERA KU NDENDE PASANATHE ZAKA ZIWIRI”

Uwu ndi mutu wankhani umene unali m’magazini ina (The Times) ya ku London, ku England. Nkhani yake inanena kuti ku Britain, anthu opitirira 70 pa anthu 100 aliwonse amene anamangidwapo chifukwa cha kuthyola nyumba kapena kuba, anamangidwanso pasanathe zaka ziwiri atatulutsidwa. Nthawi zambiri anthu ogwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo ndi amene amapalamula milandu yambiri. Amachita zimenezi n’cholinga chopeza ndalama zogulira mankhwala osokeneza bongowo, omwe amakhala okwera mtengo kwambiri ndiponso oononga thupi lawo.

[Bokosi patsamba 7]

“KODI NDENDE NDI SUKULU ZOPHUNZITSA ANTHU KUPHWANYA MALAMULO”?

Pulofesa John Braithwaite analemba mawu otsatirawa m’magazini ina (UCLA Law Review). Iye anati: “Ndende ndi sukulu zophunzitsa anthu kuphwanya malamulo.” M’buku lina (Inside the Criminal Mind), lolembedwa ndi Dr. Stanton E. Samenow, muli mfundo yakuti: “Anthu ambiri ophwanya malamulo amakhala kuti anachita kuphunzira khalidwe limeneli,” kungoti silikhala khalidwe limene anthu amafuna kuti munthu aphunzire. Iye anapitirira kunena kuti: “Kundende, anthu amakhala ndi mpata wophunzirira kunola luso lawo lophwanya malamulo. . . . Ndipotu pali anthu ena amene amafika pokhala akatswiri a khalidwe lotereli, moti amatha kuchita zinthu zophwanya malamulo zambirimbiri koma amakhala osamala kwambiri moti sagwidwa ayi.”

M’buku lomweli, Dr. Samenow anati: “Munthu sasintha khalidwe lake loipa chifukwa chongotsekeredwa m’ndende. Kaya watuluka m’ndende kaya ali m’ndende momwemo, amapeza anzake atsopano, amaphunzira maluso ena ophwanya malamulo, ndipo nayenso amauzako ena zinsinsi zake.” Mnyamata wina wa khalidwe lotereli anati: “Kundende n’kumene ndinakhalira namatetule pankhani yophwanya malamulo.”