Kuchokera kwa Owerenga
Kuchokera kwa Owerenga
Chingalawa cha Nowa Chinapangidwa Mwaluso (January 2007) Ndinkadziwa ndithu kuti chingalawa chinapangidwa mogometsa, koma sindinkadziwa kuti panagona luso lalikulu motani. Nkhani imeneyi inafotokoza zimenezi m’njira yosavuta kumva. Inanenanso mmene kukula kwa chingalawachi m’litali, m’lifupi, ndiponso msinkhu wake kupita m’mwamba kunathandizira kuti chithe kuyandama bwinobwino. Ndinaganiza zopanga chingalawa chongoyerekezera pamodzi ndi ana a mumpingo wathu. Tinatero pogwiritsira ntchito chithunzi chimene chinali m’magaziniyi. Tinapanganso tizinyama pogwiritsira ntchito mapepala n’kutiika m’chingalawacho ndipo tinajambulanso zithunzi zosonyeza Nowa ndi banja lake. Zimenezi zinatithandiza kuti timvetse zinthu zambiri zokhudza nkhani imeneyi. Zikomo kwambiri.
T. A., Japan
Mwana wanga wa zaka 6 amakonda kupanga tizidole ta zinthu zosiyanasiyana. Ine ndi iyeyo tinasangalala kwambiri titawerenga nkhaniyi n’kuona kuti kumapeto kwake kuli chingalawa chongoyerekezera komanso malangizo a mmene tingachipangire. Tsiku limenelo tinasangalala kwambiri, chifukwa cha nkhani yosangalatsayi. Masiku ano anthufe timatanganidwa kwambiri ndipo mlungu uliwonse ana athu amakumana ndi zovuta zosiyanasiyana kusukulu, moti ndi madalitso aakulu zedi kukhala ndi magazini monga Galamukani!, yothandiza makolo kulera ana awo m’njira yosangalatsa Yehova.
M. F., United States
Zimene Achinyamata Amadzifunsa: Kodi Ndingathetse Bwanji Chizolowezi Chimenechi? (November 2006) Nditawerenga nkhaniyi, ndinakhudzidwa mtima kwambiri pozindikira kuti Yehova amatiganizira kwambiri ndipo amatithandiza kuthana ndi mavuto athu. Ngakhale kuti nthawi zina timaiwaliza, Yehova “ndi wokhululukira.” (Salmo 86:5) Kuzindikira zimenezi kumatithandiza achinyamatafe ‘kuthawa zilakolako za unyamata.’—2 Timoteyo 2:22.
V.F.F., Brazil
Zimene Achinyamata Amadzifunsa: N’chifukwa Chiyani Amandiikira Malamulo Ambirimbiri? (December 2006) Ndakhala ndikuphunzira Baibulo kwa zaka 6. Ngakhale kuti makolo athu amatiikira malamulo okhwima, ndikudziwa kuti amatero chifukwa cha chikondi. Nditawerenga nkhaniyi, inandithandiza kwambiri kumvetsa zifukwa zimene makolo anga amakhalira ndi nkhawa ndipo yandithandizanso kuona kuti Yehova amandiganizira ineyo pandekha.
K. T., Thailand
Ndinali Mwana Wolowerera (December 2006) Ndadziwa Yehova kuyambira mu 1992. Koma pali nthawi inayake pamoyo wanga imene ndinkafuna kukhala moyo womangochita zofuna zanga, osati za Yehovayo ayi. Monga anachitira Meros Sunday, moyo wanga wokonda zosangalatsa unalinso ndi zovuta zina, ndipo patatha zaka zitatu nditasiya Yehova, ndinayamba kum’pempha kuti andithandize. Tsopano ndabwereranso kwa Yehova. Zikomo kwambiri, mwagwira ntchito.
D. K., Ukraine
Zimene Achinyamata Amadzifunsa: Kodi Ndingayambe Chibwenzi Nditafika Msinkhu Wotani? (January 2007) Panopo ndili ndi zaka 15. Nthawi inayake ndinapita ku nyumba kwa azakhali anga kuti ndikawaone, iwowo ndi amuna awo. Kumeneko ndinakumanako ndi mnyamata wa zaka 17, yemwenso anali wa Mboni. Tinayamba kulankhulana pa Intaneti, ndipo poyamba tinkangolankhulana mwa apo ndi apo. Koma posakhalitsa tinayamba kulankhulana tsiku lililonse, ndipo tinayamba kukondana. Koma nditawerenga nkhani imeneyi ndinazindikira kuti zimene timachitazo kwenikweni ndi chibwenzi. Motero makolo anga komanso nkhani ya mu Galamukani! ija, inandithandiza kuganiza zothetsa chibwenzicho posiya kulankhulana ndi mnyamatayo. Sikuti panopo tinadana ayi, koma ndinayamba kuika patsogolo ubwenzi wanga ndi Yehova. Ndikuthokoza kwambiri chifukwa chakuti nkhaniyi inanditsegula m’maso.
D. D., Canada