Mphatso Yamtengo Wapatali
Mphatso Yamtengo Wapatali
Onse awiri, wopatsa ndi wolandira amasangalala ngati mphatso imene yaperekedwa ili yofunika komanso ngati wolandirayo wathokoza. Osati kale kwambiri, mayi wina wogwira ntchito yofunika kwambiri m’boma ku Mexico, analembera kalata ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova kuthokoza chifukwa chomutumizira buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Mwa zina, m’kalata yake anati:
“Buku limeneli n’lamtengo wapatali. Ndaona kuti ngakhale mfundo zake zikuchokera m’buku lakale kwambiri, zikumveka zatsopano komanso n’zothandiza pamoyo wathu wa tsiku ndi tsiku.
“Ndamvetsa kuti makolofe tiyenera kuphunzitsa ana athu mfundo zimene zingawathandize kukhala oganiza bwino komanso odziwa zinthu, kutinso akhale aulemu ndi oona mtima ngakhale kuti makhalidwe amenewa akusowa masiku ano. Koposa zonse, tiyenera kuwathandiza kuzindikira kuti kuli Mlengi wachikondi, wokoma mtima, ndi wanzeru kwambiri. Dziwani kuti buku limene mwanditumizirali lindithandiza pantchito yanga komanso pa udindo umene Mlengi wapereka kwa makolofe wothandiza ana athu kukula monga anthu okonda anzawo.”
Mkulu waboma ameneyu anazindikira kufunika kophunzira kuchokera ku zimene Yesu Khristu anaphunzitsa komanso zitsanzo zake zomwe zili m’buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Inunso tingakutumizireni buku lokongola la masamba 256 limeneli, lomwe mapepala ake n’ngaakulu ngati mapepala a magazini ino. Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli lembani zofunika m’mizere ili m’munsiyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenera imene ili patsamba 5 la magazini ino.
❑ Ndikupempha kuti munditumizire buku limene lasonyezedwa panoli.
❑ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo panyumba kwa ulere.