Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndinali Mkulu wa Asilikali Koma Tsopano Ndine “Msilikali wa Khristu”

Ndinali Mkulu wa Asilikali Koma Tsopano Ndine “Msilikali wa Khristu”

Ndinali Mkulu wa Asilikali Koma Tsopano Ndine “Msilikali wa Khristu”

Yosimbidwa ndi Mark Lewis

“Mwadzuka bwanji mfumu?” “Mwaswera bwanji wolemekezeka?” “Mwaswera bwanji apulezidenti?” Awa ndi ena mwa mawu amene sankachoka pakamwa panga panthawi imene ndinali mkulu wa asilikali oyendetsa ndege zokwera akuluakulu aboma olemekezeka ku Australia. Ndinkayendetsa anthu amenewa kupita nawo m’madera osiyanasiyana a ku Australia ndi mayiko ena. Koma panopo ndikugwira ntchito yapamwamba kwambiri kuposa imeneyi. Talekani ndifotokoze bwinobwino.

NDINABADWA mu 1951, mumzinda wa Perth, ku Western Australia ndipo bambo anga anali msilikali. Nditakwanitsa zaka 15 ndinalowa m’gulu lochita masewera oyendetsa ndege zopanda injini. Umu ndi mmene ndinayambira kuphunzira kuyendetsa ndege.

Posakhalitsa, makolo anga anapatukana, ndipo banja lathu linagawanika. Bwana wina wamkulu wa gulu la asilikali oyendetsa ndege ananditenga kuti ndizikhala ndi banja lake mpaka nditamaliza maphunziro anga a kusekondale. Chitsanzo chake chinandilimbikitsa kuti ndipite ku sukulu yophunzitsa kuyendetsa ndege za asilikali (Royal Australian Air Force Academy).

Ndinamaliza Maphunziro Anga

Patatha zaka sikisi, ndinalandira digiri ya sayansi nditamaliza maphunziro anga oyendetsa ndege za asilikali. Ntchito yanga yoyamba inali yoyendetsa ndege za asilikali zonyamula anthu ndi katundu, kumapita m’madera osiyanasiyana ku Australia, South Pacific, ndi ku Southeast Asia. Nthawi zambiri tinkadutsa m’madera a mapiri ataliatali ndi m’zigwa zakuya kwambiri ndipo ndegezo tinkatera nazo pabwalo landege la udzu. Iyi inali ntchito yoopsa kwambiri moti panthawiyi ndege zingapo zinagwa ndipo asilikali angapo odalirika anafa. Komabe ntchito imeneyi inathandiza kwambiri anthu amene ankakhala m’madera akumidzi. Tinkawapititsira katundu okonzera milatho, magalimoto okonzera misewu, thandizo la chakudya ndiponso magulu a madokotala ndi anamwino. Tinkatenganso anthu ovulala ndi odwala m’madera amene kwachitika masoka.

Mu 1978, ndinakhala mlangizi wophunzitsa asilikali kuyendetsa ndege motero ndinabwerera ku sukulu kuja. Ndili kumeneko ndinayambanso kucheza ndi mkazi wina wamasiye, dzina lake Diane, yemwe anali ndi mwana wamkazi wa zaka zitatu. Mwamuna wake ndinaphunzira naye limodzi kusukulu yoyendetsa ndege koma anamwalira pangozi inayake yandege. Ndinamufunsira n’cholinga choti tidzakwatirane koma anandiyankha kuti akaganize kaye. Zokwatiwanso ndi woyendetsa ndege zinkamuopsa.

Panthawiyi ndinayamba ntchito ya chaka chimodzi yothandiza bwanamkubwa wa ku Australia. Moyo wa ku nyumba ya boma ku Canberra unandithandiza kudziwa bwino mmene ndale zimayendera ndiponso kudziwana ndi akuluakulu ambiri aboma, a asilikali, ndiponso achipembedzo. Nditamaliza ntchito imeneyi ndinabwereranso ku ntchito yanga ya uphunzitsi ija. Kenaka ine ndi Diane tinakwatirana mu 1980.

Mu 1982, ndinapita ku United States kukagwira ntchito ngati msilikali wamkulu woyang’anira za kapewedwe ka ngozi za ndege ndiponso kufufuza zimene zimachititsa ngozizo. Ntchito imeneyi ndinaigwira kwa zaka ziwiri potenga malo a msilikali wina wa m’dzikolo yemwenso anakatenga malo anga ku Australia. Chifukwa cha ntchitoyi ndinaponda paliponse ku United States ndipo ndinafika mpaka ku Northern Ireland. Ndinkaperekanso malangizo a mmene angasinthire kapangidwe ka ndege kuti achepetse ngozi.

Ndinabwerera ku Australia

Nditabwerera ku Australia tinakhala ndi mwana wamkazi dzina lake Kerry, ndipo banja langa linakula chifukwa tsopano tinakwana anthu anayi. Koma banja lathu silinkayenda bwino chifukwa choti ndinkatanganidwa kwambiri, moti mkazi wanga Diane analinso ngati bambo wa ana athuwo. Patatha zaka zitatu, ndinakwezedwa n’kukhala mkulu wa asilikali oyendetsa ndege zokwera akuluakulu aboma olemekezeka, monga ndatchulira poyamba paja. Mu 1991, kagulu kathu ka asilikali apandege kanathandiza kwambiri bungwe la United Nations pa nkhondo ya ku Persian Gulf ndiponso m’madera ena monga ku Pakistan, Afghanistan, Africa, ndi Israel.

Mu 1992, ndinakhala wothandizira mkulu wa asilikali onse ku Australia. Ntchito imeneyi inandithandiza kwambiri kumvetsa mgwirizano umene ulipo pakati pa magulu ankhondo, andale, ndi bungwe la United Nations. Ndinaona kuti bungweli lili ndi zinthu zambiri zolakwika. Komano ndinkakhulupirira kuti ndi bungwe lokhalo limene lingabweretse mtendere. Kenaka, m’banja mwanga munachitika zinthu zimene zinandipangitsa kusintha maganizo.

Mafunso a Mkazi Wanga Anayankhidwa

Diane anali Mkatolika, ndipo mwamuna wake woyamba atamwalira, kwa nthawi yaitali iye anali ndi mafunso ambiri amene ankamuvutitsa m’maganizo makamaka pamene mwana wathu Renee, anayamba kuchita zamatsenga. Mkazi wangayu atapita ku nyumba ya mnzake kukacheza, anaona magazini ya Galamukani! yomwe inafotokoza kuti magazini yotsatira idzakhala ndi nkhani yokhudza chipembedzo cha Satana. * Panthawiyi n’kuti asanaonepo magazini iliyonse ya Galamukani! Pobwerera ku nyumba, njira yonseyo ankangodzifunsa kuti: ‘Kodi ndingaipeze bwanji magazini imeneyi?’

Patapita masiku atatu, pakhomo pathu panafika Mboni za Yehova ndipo mkazi wanga Diane anapeza magazini ankafuna ija. Kenaka anavomera kuti azimuphunzitsa Baibulo ndiponso anayamba kumapezeka pa misonkhano yawo. Zimenezi zinandisangalatsa moti nthawi zina ndinkapita nawo kumisonkhanoko, komabe ndinalibe chidwi chophunzira Baibulo. Ndinkaona kuti zopemphera zinandidutsa kumanzere. Inde, ndinkakhulupirira Mulungu koma zopemphera ndinalibe nazo ntchito kwenikweni chifukwa cha zachinyengo zimene ndinkaona m’zipembedzo. Mwachitsanzo, akuluakulu achipembedzo ankalimbikitsa nkhondo koma iwo omwewo ankalalikira za chikondi ndi mtendere.

Mkazi wanga ankaika dala magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! pamalo oonekera kuti ndiwaone n’kuwawerenga. Koma ndinkati ndikawawerenga ndinkawabwezeretsa bwinobwino kuti asadziwe. Nditayamba kulimvetsa Baibulo, panali malemba awiri amene ankandivutitsa maganizo kwambiri. Loyamba linali Chivumbulutso 19:17, 18, limene limanena kuti mbalame zidzadya minofu ya “akuluakulu a asilikali.” Lachiwiri linali Chivumbulutso 17:3, lomwe limanena za “chilombo chofiiritsa.” Sindinkamvetsa kuti n’chifukwa chiyani Amboni ankanena kuti chilombochi chikuimira bungwe la United Nations. * Komabe zonsezi ndinangozinyalanyaza.

Mu 1993, Diane anandipempha kuti ndikaonerere ubatizo wake. Ndinachita kakasi motero ndinam’funsa kuti: “Kodi pakati pa ineyo ndi Yehova ungasankhe ndani?” Iyeyo anayankha kuti “Ndingasankhe Yehova. Koma palibe chifukwa chosankhapo mmodzi pa awirinu chifukwa nonse ndinu ofunika kwa ine.” Pamenepa ndinazindikira kuti ndikufunika kum’dziwa bwino Yehovayo chifukwa ndi munthu wofunika kwa mkazi wanga. Mkulu wina mumpingo wa kwathuko anandipempha kuti azindiphunzitsa Baibulo ndipo ndinavomera.

Ndinkachita chidwi kwambiri ndi maulosi a m’Baibulo makamaka onena za asilikali ndiponso za mbiri yakale. Mwachitsanzo, pamene ndinkaphunzira zausilikali, ndinaphunzira za nkhondo zimene Agiriki akale anapambana. Tsopano ndinaphunzira kuti zambiri mwa nkhani zimenezi zinalembedwa m’buku la Danieli chaputala 8, patatsala zaka zambirimbiri kuti zichitike. Ndinafika pokhutira kuti Baibulo ndi buku louziridwadi ndi Mulungu chifukwa cha ulosi umenewu komanso maulosi ena.

Bungwe la United Nations ndinayambanso kuliona m’njira ina. Ndinadziwa kuti asilikali sangathetse mavuto a anthu, kuti nkhondo siingabweretse mtendere weniweni, ndiponso kuti bungweli silingathetse mavuto onse omwe amayambitsa nkhondo monga a zandale, a zachipembedzo ndiponso kusankhana mitundu. Ndinayamba kuona kuti ndi Mulungu yekha amene angathetse mavuto a anthu. Ndipotu ndinkaona kuti iye wayamba kale kutero pakati pa Mboni za Yehova padziko lonse. (Salmo 133:1; Yesaya 2:2-4) Komabe ndinkadzifunsa kuti: ‘Ndithu ndisiye ntchito yanga yausilikali kuti ndiyambe kutumikira Mulungu?’

Ndinayamba Kutsatira Mfundo za M’Baibulo

Zinthu zinafika pachimake m’chaka cha 1994 pomwe ndinakapezeka pa msonkhano wachigawo wa Mboni za Yehova mumzinda wa Sydney. Pamsonkhanowo panali sewero lokhudza Aisiraeli amene anafunika kusankha pakati pa kutumikira Yehova kapena Baala, mulungu wa a Kanani. M’seweroli, Eliya, yemwe anali mneneri wa Yehova, anauza Aisiraeliwo kuti: “Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, m’tsateni iye; ngati Baala, mum’tsate iyeyo.” (1 Mafumu 18:21) Mawu amenewo anandilasa mtima. Ndinaona kuti ineyo ndinkakayikakayika ngati Aisiraeli aja. Ndinafunika kusankhapo chimodzi; kutumikira Yehova kapena kupitiriza ntchito ya usilikali.

Tikubwerera ku nyumba pagalimoto, ndinamuuza mkazi wanga kuti ndikufuna kusiya ntchito kuti ndikhale wa Mboni za Yehova. Iye sanayembekezere kuti ndingasinthe maganizo mwamsanga chonchi, komabe anandilimbikitsa. Ndinatsimikizadi kuchita zimenezi, moti patapita masiku angapo ndinakapereka kalata yoti ndikusiya ntchito.

Panthawiyo, ndinali mkulu woyang’anira sukulu yophunzitsa asilikali kuyendetsa ndege zankhondo (Australian Defence Force Academy) yomwe inali ku likulu la dzikoli, ku Canberra. Ndinkayang’anira ntchito yophunzitsa usilikali ndiponso maphunziro ena. Pasukulupo panali asilikali 1,300 ophunzira nkhondo yapamtunda, yapamadzi, yam’mlengalenga ndiponso asilikali ophunzira ntchito zina. Patsiku lomaliza maphunziro awo, ndinauza gulu la ophunzira okwana 400 pamodzi ndi asilikali ena kuti ndikusiya usilikali kuti ndikayambe ntchito yoyenda khomo ndi khomo n’kumaphunzitsa anthu Baibulo mongodzipereka. Ambiri anachita chidwi moti pambuyo pake ndinakambirana nawo zinthu zambiri za m’Baibulo.

Kuyamba Utumiki wa Nthawi Zonse

Nditasiya ntchito ngati lero, mawa lake ndinayamba kulalikira ndipo ndinabatizidwa patangotha miyezi itatu, mu April 1995. Kenaka mosataya nthawi ndinalembetsa upainiya wokhazikika, kutanthauza kuti nthawi yanga yonse inkathera kulalikira.

Poti ndinali mkulu wa asilikali, ndinayenera kusintha kwambiri kuti ndifike pokhala ‘msilikali wa Khristu.’ (2 Timoteyo 2:3) Imodzi mwa ntchito zimene ndinayamba kupatsidwa mumpingo inali yoperekera maikolofoni pa misonkhano. Ndinafunikanso kuphunzira kusatuma anthu mochita kuwalamula koma mowapempha. Ndinazindikira kuti chikondi ndiponso kuganizirana n’zofunika kwambiri kuposa kuchita zinthu mwachangu ndiponso mosalakwitsa. Komabe, ngakhale panopo ndimavutikabe nthawi zina kusonyeza makhalidwe amenewa moyenerera. Komanso chifukwa choti panopo ndimapeza ndalama zochepa, banja langa limakhala moyo wosalira zambiri.

Ntchito yolalikira inandisangalatsa kwambiri ndipo ndimaikondabe mpaka pano. Nthawi ina ndikulalikira ndi mwana wanga Kerry, yemwe anali ndi zaka 9, ndinamuuza kuti azionetsetsa mmene eni nyumba akulandirira uthenga wathu. Posakhalitsa, tinaona kuti anthu ambiri anali opanda chidwi komabe panali angapo amene anali ansangala kapenanso achidwi. Zimenezi zinatilimbikitsa kwambiri. Mwana wathu wina uja anaphunzira Baibulo kwakanthawi koma pakali pano sakufuna kutumikira Yehova.

Ine ndi mkazi wanga Diane tinam’limbikitsa Kerry kuti akhale ndi cholinga chochita utumiki wa nthawi zonse. Motero ndinasangalala kwambiri posachedwapa kuti tinachita Sukulu ya Utumiki Waupainiya limodzi ndi mwana wathuyu. Aka kanali koyamba kuti iyeyu achite nawo sukuluyi, koma ine kanali kachiwiri. N’zosangalatsa kwambiri kuona mwana wathuyu pamodzinso ndi achinyamata ena akupita patsogolo mwauzimu n’kumachita utumiki wachikhristu.—Salmo 110:3.

Ndapeza Madalitso Osaneneka

Ndikayang’ana m’mbuyo, ndimayerekezera moyo wa msilikali weniweni ndi moyo wa msilikali wa Khristu. Ndimaona kuti zonsezi zimafunika kukhulupirika, kumvera, kudziletsa ndiponso kudzipereka. Koma ngakhale kuti asilikali ambiri amalolera kufera dziko lawo ndiponso anthu anzawo, Akhristu oona amalamulidwa kuti azikonda ngakhale adani awo. (Mateyo 5:43-48) Chinanso n’chakuti asilikali amapatsidwa mendulo yaulemu ngakhale akachita chinthu chimodzi chokha chosonyeza kulimba mtima. Koma Akhristu oona amayanjidwa ndi Mulungu chifukwa chokhulupirika pomutumikira mosalekeza. Nthawi zina zimenezi zimafunika kulimba mtima potsutsidwa, kunyozedwa ndiponso pokumana ndi mayesero osiyanasiyana kwa zaka zambirimbiri. (Aheberi 10:36-39) Pa anthu onse amene ndikudziwa, palibe anthu abwino kuposa Akhristu anzanga.

Masiku ano mawu amene sachoka pakamwa panga ndi akuti: “Mwadzuka bwanji mlongo?” Kapena “Mwaswera bwanji m’bale?” Kuchita utumiki wachikhristu pamodzi ndi anthu okondadi Mulungu n’kosangalatsa kwabasi. Koma chinthu chonyaditsa kwambiri ndicho kutumikira Yehova, Mulungu Wam’mwambamwamba. Pamoyo wanga palibe chinthu chopindulitsa kwambiri kuposa kutumikira Yehova.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 15 Nkhaniyi inatuluka m’magazini ya Chingelezi ya October 22, 1989, tsamba 2 mpaka 10.

^ ndime 17 Onani tsamba 240 mpaka 243 m’buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand! lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

[Mawu Otsindika patsamba 14]

Ngakhale kuti asilikali ambiri amalolera kufera dziko lawo ndiponso anthu anzawo, Akhristu oona amalamulidwa kuti azikonda ngakhale adani awo

[Chithunzi pamasamba 12, 13]

Ndikuyendetsa ndege yankhondo yonyamula akuluakulu aboma ndipo apa tinali kudutsa pa nyumba ya malamulo, ku Canberra

[Chithunzi patsamba 15]

Sewero la nkhani ya m’Baibulo pa msonkhano wachigawo m’chaka cha 1994, ku Sydney, m’dziko la Australia.

[Chithunzi patsamba 15]

Ine ndi mwana wanga Kerry pa Sukulu ya Utumiki Waupainiya

[Chithunzi patsamba 15]

Ine, mkazi wanga Diane ndi mwana wathu Kerry panopo