Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Posachedwapa Zachiwawa ‘Zidzatha’

Posachedwapa Zachiwawa ‘Zidzatha’

Posachedwapa Zachiwawa ‘Zidzatha’

“Katsala Kanthawi Ndipo Woipa Adzatha Psiti.”—SALMO 37:10.

MLENGI wathu Yehova Mulungu amatiganizira kwambiri anthufe. Iye sanaiwaleko za ife, monga mmene anthu ena amaganizira. (Salmo 11:4, 5) Komanso, ngakhale kuti anthu sangathe kuona zonse, iye amaona zachiwawa zonse zimene zikuchitika komanso kusowa chilungamo konse. “Maso a Yehova ali ponseponse, nayang’anira oipa ndi abwino.” (Miyambo 15:3) Motero, musakayike kuti anthu onse oipa ali “poterera.”—Salmo 73:12, 18.

Komabe, anthu olungama ndiponso amakhalidwe abwino, ngakhale atakhala osauka komanso oponderezedwa, ali ndi tsogolo labwino kwambiri. Wamasalmo Davide, analemba kuti: “Tapenya wangwiro, ndipo taona woongoka mtima! Pakuti ku matsiriziro ake a munthuyo kuli mtendere.”—Salmo 37:37. Mawu amenewa angatilimbikitse kwambiri masiku ano, chifukwa tili ndi chiyembekezo choti posachedwapa tidzaona akukwaniritsidwa padzikoli.

Tikukhala M’masiku Otsitiriza

Zaka 2,000 zapitazo, ophunzira a Yesu anam’funsa funso lomwe limakhudza anthu mpaka panopo. Iwo anati: ‘Tiuzeni, kodi chizindikiro cha . . . mapeto a dongosolo lino la zinthu chidzakhala chiyani?’ (Mateyo 24:3) Zimene Yesu anayankha zinalembedwa mwatsatanetsatane mu chaputala 24 cha buku la Mateyo, chaputala 13 cha buku la Maliko, ndiponso chaputala 21 cha buku la Luka. Machaputala a Mauthenga Abwino amenewa amafotokoza masiku otsiriza a dongosolo lino la zinthu, lomwe n’lodzaza ndi nkhondo, njala, matenda, zivomezi zikuluzikulu, ndiponso kuchuluka kwa anthu osamvera malamulo.

Nthawi yovuta imene Yesu analoserayi inayamba mu 1914. Katswiri wina wa mbiri yakale, dzina lake Eric Hobsbawn, ananena mawu otsatirawa m’buku lake lina (Age of Extremes) lonena za zaka za m’ma 1900. Iye anati: “Kunena zoona, zaka zimenezi zinali zaka zoopsa kwambiri pa zaka zonse.”

Pankhani ya kufala kwa zoipa kwa masiku anoku, Baibulo limati: “Chakuti pophuka oipa ngati msipu, ndi popindula ochita zopanda pake; chitero kuti adzawonongeke kosatha.” (Salmo 92:7) Inde, n’zosachita kufunsa kuti kuchuluka kwa anthu osamvera malamulo kwa masiku anoku kwenikweni ndi chizindikiro chakuti oipa atsala pang’ono kuwonongedwa. Kodi imeneyi si nkhani yabwino?—2 Petulo 3:7.

“Olungama Adzalandira Dziko Lapansi”

Lemba la Salmo 37:29 limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” Kupanda chilungamo komanso zoipa za mtundu ulionse zidzakhala mbiri yakale. Motero, sipadzakhalanso zinthu ngati ma alamu odziwitsa kuti kwabwera akuba, sipadzakhalanso maloko, mabwalo a milandu, anthu oimira anzawo pa mlandu, apolisi ndiponso ndende. Baibulo limalonjeza kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.”—Yesaya 65:17.

Inde, dziko lapansi lidzasintha kwambiri ndiponso anthu onse adzasangala ndi zinthu zatsopano zomwe sizinaonekenso n’kale lonse. (Yesaya 11:9; 2 Petulo 3:13) Mboni za Yehova sizimakayika kuti zimenezi zidzachitika, motero zikufunitsitsa kuti inunso mufufuze nokha kuti muone ngati zimenezi n’zoona. Kumbukirani kuti Mulungu yemwe anauzira Malemba Oyera ‘sanganame.’—Tito 1:2.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 9]

KUTHANDIZA AKAIDI MWAUZIMU

Kwa zaka zambiri, Mboni za Yehova ku United States zakhala zikulandira makalata kuchokera kwa akaidi a m’ndende zokwanira 4,169. Ena anali m’zipatala kuti akalandire chithandizo cha matenda kapena kuti awathandize kuti asiye kugwiritsa ntchito mankhwala osokoneza bongo. Ena mwa akaidiwa amapempha mabuku ofotokoza Baibulo ndiponso kuti aziphunzitsidwa Baibulo kwaulere. Mboni za Yehova zimapeza anthuwa n’kuwathandiza. Ndipotu padziko lonse Mboni za Yehova zimapita ku ndende kawirikawiri kukaphunzira Baibulo ndi akaidi omwe akufuna kuthandizidwa mwauzimu, aamuna ndi aakazi omwe. Ambiri mwa akaidiwa asintha kwambiri khalidwe lawo, abatizidwa n’kukhala Akhritsu ndipo akatuluka amakakhala anthu omvera malamulo.