Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

“Kuchokera m’ma 1970 kufika m’ma 1990, mavuto obwera chifukwa cha kusintha kwa nyengo anawonjezeka kuwirikiza katatu, mwina chifukwa cha kutentha kwa dziko lonse kapena zinthu zina.”—THE ECONOMIST, BRITAIN.

Ku Illinois, U.S.A., boma linapereka chilolezo chovomereza mwana wa miyezi 10 kukhala ndi mfuti. Bambo a mwanayo ndi amene anakatenga chilolezocho, ndipo anangofunika kutchula kuti mwanayo anali wamtali pafupifupi masentimita 70, ndipo anali wolemera makilogalamu 9. Boma kumeneku siliganizira zaka za munthu yemwe akufuna chilolezo cha mfuti.—CABLE NEWS NETWORK, U.S.A.

Asayansi apeza njira yochititsa kuti madzi oundana azitha “kutentha mopitirira mlingo umene madzi amafika akatentha kwambiri, koma asamasanduke nthunzi.” Madzi oundana ali m’magulu osiyanasiyana osachepera 11, ndipo amaundana pa mlingo wosiyanasiyana.”SANDIA NATIONAL LABORATORIES, U.S.A.

Ufulu Wopembedza ku Georgia

Khoti lalikulu ku Ulaya (The European Court of Human Rights) lagamula kuti boma la dziko la Georgia linalakwa polola zachiwawa zomwe anthu ena amachitira Mboni za Yehova. Khotilo linanena motsindika kuti Mboni za Yehova zili ndi ufulu monga chipembedzo chilichonse chodziwika chachikhristu. Motero zili ndi ufulu wosonkhana kuti zizilambira ndi kuphunzira Baibulo, ndipo lalamula kuti Mbonizo zipatsidwe chipukuta misozi. Pakati pa mwezi wa October 1999 ndi November 2002, Mboni za Yehova zachitidwapo chiwawa nthawi 138 ndipo zadandaulapo ku boma maulendo 784. Koma aboma ananyalanyaza kuifufuza bwinobwino nkhaniyi. Ndipo apolisi anakana kuteteza Amboniwo. Komabe kuyambira mu November 2003, zachiwawazi zachepa kwambiri.

Kuona Kayendedwe ka Dzuwa ku Peru

Akatswiri panopo akuti bwinja lomwe lakhalapo kwa zaka 2,300 ku Peru, kwenikweni linali malo omwe kalelo ankaonerapo kayendedwe ka dzuwa. Bwinjali limatchedwa kuti Chankillo, ndipo lili ndi nsanja 13 zomwe zili pamwamba pa mapiri. Mukakhala patali kwambiri, phirili limaoneka ngati lili ndi mano. Magazini ina (Science) inati malowo “anawamanga m’njira yoti kawiri pachaka dzuwa aziliona likutulukira kumayambiriro kwa nsanjazo ndi kulowera kumathero kwake. Chifuwa cha njira imeneyi, iwo ankatha kudziwa poyambira ndiponso pakati pa chaka.” Nsanja zomwe anazimanga pakati zinkawathandiza kuona malo osiyanasiyana amene dzuwa linkatulukira ndi kulowera. M’dera loumali, kudziwa nthawi yoyenera kubzala mbewu kunali kofunika kwambiri, “moti anthu [ankafunika] kudziwa nthawiyi molondola.”

[Chithunzi patsamba 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mu June Pakati pa chaka choyendera dzuwa Mu December

↑ ↑ ↑

Malo oonera kayendedwe ka dzuwa

[Mawu a Chithunzi]

REUTERS/Ivan Ghezzi/Handout

Zithunzi Zimene Akazi Zimawaipira

Lipoti lina la pa yunivesite ina ku America (University of Missouri-Columbia) linati “Zithunzi za akazi owonda kwambiri komanso amaonekedwe okopa, zomwe amaziika pa zikuto za magazini zimawaipira akazi onse, kaya akhale achitsikana kapena achikulire, ochepa thupi, aatali kapenanso aafupi.” Pulofesa wina wa zamaphunziro ndi zopereka malangizo, dzina lake Laurie Mintz, anati: “Poyamba anthu ankaganiza kuti akazi onenepa okha ndi amene amakhumudwa akaona zithunzi za akazi ochepa thupi kwambiri amene amajambulidwa m’magazini ndiponso amene amasonyezedwa pa TV.” Komano Mintz anati: “Tapeza kuti si akazi onenepa okha omwe anali nazo vuto zithunzizi. Akazi onse zimawaipira.”