Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Akasupe a Madzi Otentha

Akasupe a Madzi Otentha

Akasupe a Madzi Otentha

ZAKA zoposa 2,000 zapitazo, anthu otchedwa Aselote anakhazikika m’dera la kufupi ndi malo okhala ndi akasupe ndipo malowa anawapatsa dzina loti Ak-Ink, kutanthauza kuti “Madzi Ambirimbiri.” Masiku ano dera limeneli limatchedwa Budapest, ndipo ndi likulu la dziko la Hungary. Mzindawu ndi umodzi mwa mizinda yakale kwambiri ku Ulaya. Anthu amene anayamba kufika kumeneku ankasangalala kwambiri posambira m’mayiwe a madzi otentha omwe ankawathandiza kuchotsa totsinatsina tinan’tina m’matupi awo.

M’nthawi ya atumwi, chigawo cha Ulaya chimenechi chinayamba kulamulidwa ndi Aroma. Aromawa anakuza malowa ndipo anamanganso malo a asilikali omwe anawapatsa dzina lakuti Aquincum. Akuti mwina dzinali linachokera ku chinenero cha Chiselote kapena ku mawu a Chilatini (aqua quinque) otanthauza kuti “madzi asanu.”Aroma anamanga ngalande zamadzi akumwa, za madzi oipa, ndiponso malo osambira. Malo osambirawa anali magulu awiri, ena a boma ndipo ena anali a anthu. Motero malo osambira a ku Budapest ndi akale kwambiri.

Malo osambirawa anayamba kutchuka kwabasi patapita zaka zambiri Ufumu wa Aroma utatha. M’zaka za m’ma 1400, olemba mabuku ankayamikira kwambiri malo osambira omwe anali kufupi ndi mzinda wa dziko la Hungary. Zimenezi zinachititsa kuti dzikoli litchuke. Mfumu Matthias Corvinus yemwe analamulira dziko la Hungary kuchokera m’chaka cha 1458 mpaka 1490, akuti anamanga njira yokhala ndi denga pofuna kulumikiza malo ake osambira, otchedwa Rácz Bath, ndi nyumba yake yachifumu. Motero ankatha kupita ku malowa ngakhale mvula ikugwa.

Cha m’ma 1500 ndi m’ma 1600, anthu a ku Turkey ankalamulira mbali yaikulu ya dziko la Hungary, kuphatikizapo likulu la dzikolo. Iwo anamanga malo osambira okhala ndi nthunzi ndiponso ena okhala ndi madzi otentha. Malowa ndi ofunika kwambiri pa miyambo ya Asilamu. Komanso ndi malo ofunika kwa anthu onse a ku Turkey. Malo okongolawa kwenikweni anali ngati damu lokhala ndi denga ndiponso masitepe ozungulira damu lonselo. Madzi ake anali akuya kufika m’mapewa. Malowa analinso ndi mabafa osambira ndiponso malo opumira omwe ankagwiritsidwa ntchito ndi amuna komanso akazi mosinthanasinthana. Ena mwa mabafa amenewa akugwiritsidwabe ntchito mpaka pano.

M’chaka cha 1673, magazini ina inafotokoza za malo osambira omwe ali ku dera limene panopo limatchedwa kuti Budapest. Magaziniyi inati malowa ali m’gulu la malo abwino kwambiri osambirako ku Ulaya konse chifukwa “kuli akasupe ambiri a madzi otentha, omwe amathandiza kuchiza mavuto ena a m’thupi. Malowanso ndi otakasuka komanso okongola.” Cha m’ma 1800 madera ambiri anayamba kukhala ndi malo osambira chifukwa choti ku Finland anayamba kupanga mabafa otulutsa nthunzi yotentha kwambiri, ndipo mabafawa anatchuka. M’kupita kwa nthawi, mabafa osiyanasiyana okhala ndi madzi otentha, nthunzi, ndiponso madzi ozizira anamangidwanso ku Budapest.

Mmene Derali Lilili

Patsiku, madzi okwana malita 70 miliyoni amatuluka mu akasupe 123 a madzi otentha a ku Budapest ndi akasupe enanso 400 a madzi owawa. Kodi madzi onsewa amachokera kuti makamaka? Kuti tiyankhe funsoli, m’pofunika kuti tione kaye mmene derali lilili.

Mtsinje wa Danube, umene umachoka ku Budapest, umadutsa pakati pa mapiri otchedwa Buda, omwe ali cha kumadzulo, ndiponso mapiri a Pest, omwe ali cha kum’mawa. Kalekale dera lonseli linali nyanja ndipo n’chifukwa chake muli miyala ya laimu ndi miyala inanso yotere. Miyala imeneyi inakutidwa ndi dothi, miyala ina, mchenga ndiponso malasha.

Ming’alu ya pansi padziko imathandiza kuti madzi azifika pansi penipeni, n’kutenthetsedwa ndi miyala yotentha. Madziwa akatentha amabwerera kumtunda mothovoka, ndipo amatulukira m’ming’aluyo kapena m’zitsime.

Zimenezi sizichitika ku Budapest kokha koma m’dziko lonse la Hungary. Motero m’madera ambiri a m’dzikoli mumapezeka madzi abwinowa ndiponso malo okongola osambirako. Anthu ena amakhulupirira kuti kusamba m’malowa kumathandiza kuchiza mavuto osiyanasiyana a m’thupi. *

Kuyambira kale, anthu ambiri m’madera osiyanasiyana padziko lonse, akhala akukonda akasupe amadzi otentha. Malo ena oterewa anawatulukira m’chipululu chotchedwa Seir, chomwe chili pakati pa nyanja ya Dead Sea ndi chigwa cha Aqaba, ndipo anawatchula ngakhale m’Baibulo.—Genesis 36:24.

Padakali zinthu zambiri zovuta kumvetsa zokhudza dzikoli zimene anthu sanazidziwebe. Mwachitsanzo, kodi Mulungu anayala bwanji maziko a dziko lapansili? Nanga anapanga bwanji zinthu zake zosiyanasiyana zodabwitsazi? Kuganizira mafunso amenewa kumathandiza anthu oopa Mulungu kugoma kwambiri ndi nzeru zopanda malire za Mlengiyu.—Yobu 38:4-6; Aroma 1:20.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Galamukani! siilangiza anthu kutsatira njira zinazake zachithandizo chamankhwala.

[Chithunzi pamasamba 24, 25]

Malo Osambira a madzi otentha pa hotela yotchedwa Gellért

[Chithunzi patsamba 24]

Malo osambirapo otchedwa Rudas, omwe anamangidwa ndi anthu a ku Turkey

[Chithunzi pamasamba 24 25]

Malo osambirapo a madzi otentha otchedwa Széchenyi, mu nyengo yozizira

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

All photos: Courtesy of Tourism Office of Budapest