Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Imfa Yofunika Koposa M’mbiri Yonse ya Anthu

Imfa Yofunika Koposa M’mbiri Yonse ya Anthu

Imfa Yofunika Koposa M’mbiri Yonse ya Anthu

N’chifukwa chiyani imfa ya Yesu Khristu inali yofunika kwambiri?

N’chifukwa choti imfa yake inasonyeza kuti Mulungu ndi wolungama ndiponso inali umboni woti n’zotheka kuti munthu akhale wokhulupirika kwa Mulungu.

Imfa ya Yesu inapereka mwayi woti anthu adzathe kukhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso pa dziko lapansi.

Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake kutatsala tsiku limodzi kuti afe. Mwambowu unali wosachulukitsa zochita zambirimbiri. Ndipo pamwambowu Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Muzichita zimenezi pondikumbukira ine.”—Luka 22:19, 20.

Kodi inuyo Mudzapezeka pa Mwambowu?

Mboni za Yehova zikukulimbikitsani kuti mudzakhale nawo pamwambo wofunika kwambiri umenewu. Chaka chino mwambo wokumbukira imfa ya Yesu udzachitika Loweruka, pa March 22 dzuwa litalowa. Kuti mudziwe malo amene mwambowu ukachitikire ndiponso nthawi imene ukayambe, kafunseni ku Nyumba ya Ufumu ya m’dera lanu. Pa mwambowu simudzauzidwa kuti mupereke ndalama ndipo aliyense akuitanidwa kuti adzamvetsere nkhani yochokera m’Baibulo ndiponso kuti adzaonere nawo mwambo wosachulukitsa zochita zambirimbiriwu.