Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mungapeze Bwanji Chipembedzo Choona?

Kodi Mungapeze Bwanji Chipembedzo Choona?

Kodi Mungapeze Bwanji Chipembedzo Choona?

Anthu ena amafunsa kuti: ‘Ngati palidi choonadi chochokera kwa Mulungu,’ n’chifukwa chiyani ndiyenera kuchita kuchifufuza? Ngati Mulungu ali ndi uthenga wofunika kwa anthu onse, kodi sibwenzi ataunena momveka bwino kuti anthu aumve mosachita kuvutika n’kufufuza?’

INDE, Mulungu atafuna angathe kuchita zimenezi. Komano kodi imeneyi ndiyo njira imene iyeyo anasankha kuti atiuzire choonadi?

Mmene Mulungu Amatiuzira Choonadi

Kwenikweni Mulungu amapereka uthenga wake m’njira yakuti anthu ofunadi kudziwa choonadicho athe kuchifufuza n’kuchipeza. (Salmo 14:2) Taganizirani uthenga umene Mulungu anapereka kwa anthu ake osamvera zaka zambiri zapitazo, kudzera mwa mneneri Yeremiya. Ayudawo anali atapandukira Mulungu, motero uthenga wake unali wakuti Yerusalemu adzawonongedwa ndi Ababulo.—Yeremiya 25:8-11; 52:12-14.

Komabe, panthawi yomweyo, panalinso aneneri ena omwe ankanena kuti akulengeza uthenga wochokera kwa Mulungu. Mmodzi wa aneneri amenewa anali Hananiya, yemwe analosera kuti mzinda wa Yerusalemu udzakhala pa mtendere. Uthenga umenewu unali wosiyana kwambiri ndi uthenga umene Yeremiya anapereka. Motero, kodi anthu akanadziwa bwanji woyenera kumukhulupirira, pakati pa Yeremiya ndi aneneri amene ankamutsutsa?—Yeremiya 23:16, 17; 28:1, 2, 10-17.

Kuti adziwe amene ankanena zoona, Ayuda oona mtima anafunika kum’dziwa Yehova, ndi makhalidwe ake. Anafunika kumvetsa bwinobwino malamulo ndiponso mfundo zake, komanso maganizo ake pankhani ya kuchita zolakwa. Motero akanaona kuti zimene mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa Yeremiya anali oona. Mawu ake anali akuti panthawiyo “panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake.” (Yeremiya 8:5-7; 52:4-14) Komanso, akanatha kuona okha kuti zimenezi zinaipitsa zinthu mumzinda wa Yerusalemu komanso kwa anthu okhala mumzindawo.—Deuteronomo 28:15-68; Yeremiya 52:4-14.

Maulosi amene Yeremiya ananena okhudza Yerusalemu anakwaniritsidwa. Mzindawo unawonongedwa ndi Ababulo mu 607 B.C.E.

Ngakhale kuti anthuwa anali atauzidwa kalekale za chilango cha kusamvera, panafunikira khama kuti munthu adziwe kuti nthawi ya chilango cha Mulungu ija ndi imeneyi.

Nanga Bwanji za Choonadi Chachikhristu?

Nanga bwanji za choonadi chimene Yesu Khristu anaphunzitsa? Kodi aliyense anazindikira kuti uthenga wa Yesu unali wochokera kwa Mulungu? Ayi. Ngakhale kuti Aisiraeli ankachita kumuona Yesu ndi maso awo ndipo ankawaphunzitsa n’kumachita zozizwitsa zosiyanasiyana, ambiri mwa anthu amene ankamvetsera uthenga wake sanathe kuzindikira kuti iye anali Mesiya wolonjezedwa uja, kapena kuti Khristu, kutanthauza Wodzozedwa.

Afarisi ena atafunsa Yesu kuti atchule nthawi imene Ufumu wa Mulungu udzabwere, iye anayankha kuti: “Ufumu wa Mulungu sudzabwera mwa maonekedwe ochititsa chidwi ayi.” Iye ananenanso kuti: “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.” (Luka 17:20, 21) Inde, Yesu yemwe anali Wolamulira wosankhidwa ndi Mulungu, anali pakati pawo. Koma Afarisiwo anakana kutsegula maso awo kuti aone umboni wakuti Yesu anali kukwaniritsa maulosi onse amene Mesiya anayenera kudzakwaniritsa ndipo anakananso kuvomereza kuti Yesuyo ndiye “Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”—Mateyo 16:16.

Anthu anachitanso chimodzimodzi ndi uthenga umene otsatira a Khristu a m’nthawi ya atumwi ankalalikira. Ngakhale kuti zozizwitsa zimene ankachita zinathandiza kutsimikizira kuti ntchito yawoyo inkatsogoleredwa ndi Mulungu, ambiri mwa anthu a panthawiyo sanathe kuzindikira choonadi. (Machitidwe 8:1-8; 9:32-41) Yesu analamula ophunzira ake kuti ‘akapange ophunzira mwa anthu,’ powaphunzitsa. Anthu ambiri ofuna choonadi anakhala okhulupirira chifukwa anamvetsera ndi kuphunzira choonadi cha m’Malemba.—Mateyo 28:19; Machitidwe 5:42; 17:2-4, 32-34.

Umu ndi mmene zililinso masiku ano. Panopo ‘uthenga wabwino wa ufumu ukulalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.’ (Mateyo 24:14) Ntchitoyi sikuchitika “mwa maonekedwe ochititsa chidwi ayi,” motero sikuti aliyense amazindikira kuti ndi uthenga wochokera kwa Mulungu. Komabe, choonadi cha Mulungu chimadziwika, moti anthu oona mtima amatha kuchizindikira n’kuchitapo kanthu. Awa amakhala anthu amene akufuna kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka kwa iyeyo.—Yohane 10:4, 27.

N’kutheka kuti inuyo mukufunadi kudziwa choonadi ndipo n’chifukwa chake mukuwerenga magazini inoyo, yomwe ikunena za Baibulo. Komano kodi mungadziwe bwanji chipembedzo chimene chikuphunzitsa choonadi?

Njira Yothandiza Kudziwa Choonadi

Mtumwi Paulo anayamikira anthu ena a ku Bereya chifukwa cha zimene iwowo anachita atamva uthenga wake. Iwo sanafulumire kuvomereza kuti zonse zimene Paulo anawaphunzitsa zinali choonadi, komabe anamvetsera uthengawo mwaulemu. Tingaphunzirepo kanthu pa zimene anthuwa anachita atamva uthengawo.

Onani kuti Baibulo limafotokoza kuti: “Koma anthu a ku Bereya anali a maganizo apamwamba kuposa a ku Tesalonika aja. Pakuti iwowa analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri. Anali kufufuza Malemba mosamala tsiku ndi tsiku kuti aone ngati zinthuzo zinalidi choncho. Chotero ambiri a iwo anakhala okhulupirira.” (Machitidwe 17:10-12) Kutanthauza kuti anafufuza mozama zedi. Iwo sanaganize kuti angamvetse nthawi yomweyo zonse zimene Paulo anali kuwauza.

Onaninso kuti anthu a ku Bereya “analandira mawuwo ndi chidwi chachikulu kwambiri.” Zimenezi zikutithandiza kumvetsa mmene anthuwa ankaonera kuphunzira Malemba. Iwowa sankangokhulupirira zilizonse zimene Paulo anali kuwauza, komanso sankangokayikira zilizonse. Analibe mtima womangofuna kutsutsa chilichonse chimene Paulo, yemwe anali mmodzi wa anthu oimira Mulungu, ankanena.

Taganiziraninso mfundo ina: Iyi inali nthawi yoyamba kuti anthu a ku Bereya amve za Chikhristu. Zimene anauzidwazo anasangalala nazo kwambiri moti mwina anakayikira ngati zinalidi zenizeni. Ndipo m’malo mongotsutsa zilizonse, iwowa anafufuza Malemba mosamala kuti awone ngati ‘zinthu zimene Paulo anali kunena zinalidi choncho.’ Onaninso kuti anthu a ku Bereya ndi ku Tesalonika amene anafufuza uthengawo mwakhama, anakhala okhulupirira. (Machitidwe 17:4, 12) Iwo sanataye mtima poganiza kuti choonadi n’chosatheka kuchidziwa. Motero anazindikira chipembedzo choona.

Mmene Choonadi Chimakhudzira Anthu

Munthu akapeza choonadi, monga mmene anachitira anthu a ku Bereya, amakhudzidwa mtima kwambiri moti amauza ena choonadicho ndi mtima wonse. Ena ouzidwawo sizingawasangalatse, ndipo angaone kuti ndi bwino munthuyo atadzichepetsa n’kumaona kuti n’zotheka kuti zipembedzo zina zingakhalenso zolondola. Komabe, munthu akapeza choonadi cha m’Baibulo amakhudzidwa mtima kwambiri. Sakayikira zoti n’zotheka kupeza choonadi kapena kuti pali chipembedzo chimodzi chokha chopatsa anthu chipulumutso. Komabe, kuti munthu apeze choonadi m’pofunika kuti achifufuze mwakhama, ndipo sizingatheke kutero popanda kudzichepetsa.

A Mboni za Yehova afufuza choonadi m’njira imeneyi. N’chifukwa chake amakhulupirira kuti anapeza chipembedzo choona. Ndipo akukupemphani kuti nanunso mufufuze Malemba kuti mudziwe anthu amene akupembedza m’njira yoona masiku ano. Bokosi limene lili pa tsamba linoli likufotokoza za Akhristu a m’nthawi ya atumwi. Inde, sikuti kungoona ndandanda ya zinthu zothandiza kuzindikira anthu amene akutsatira choonadi n’kokwanira, komabe bokosili lingakupatseni poyambira.

Ngati mutavomera kumaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova kunyumba kwanu kwaulere, mungathe kufufuza mozama zimene Baibulo limaphunzitsa. Mukaphunzira zimenezi, mungathe kuzindikira chipembedzo choona.

[Bokosi patsamba 9]

Mmene Mungadziwire Chipembedzo Choona

Ganizirani zochita ndi ziphunzitso za Akhristu akale:

Iwo ankadalira Mawu a Mulungu.—2 Timoteyo 3:16; 2 Petulo 1:21.

Ankaphunzitsa kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu, osati kuti anali mbali inayake ya Mulungu ndipo ankaphunzitsanso kuti Yesu amagonjera Mulungu.—1 Akorinto 11:3; 1 Petulo 1:3.

Ankaphunzitsa kuti m’tsogolo akufa adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo.—Machitidwe 24:15.

Chinthu chachikulu chimene ankadziwika nacho chinali chikondi chimene anali nacho pakati pawo.—Yohane 13:34, 35.

Aliyense sankangopembedza payekhapayekha koma anali m’magulu a mipingo ndipo mipingo yonse inali ndi oyang’anira komanso panali bungwe lalikulu limodzi la akulu omwe Mutu wawo anali Yesu.—Machitidwe 14:21-23; 15:1-31; Aefeso 1:22; 1 Timoteyo 3:1-13.

Ankalalikira mwakhama uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndipo ankauza anthu kuti Ufumuwo ndiwo chiyembekezo chokhacho chodalirika chimene anthu ali nacho.—Mateyo 24:14; 28:19, 20; Machitidwe 1:8.

[Chithunzi patsamba 7]

Kodi anthu akanadziwa bwanji kuti Yeremiya anali mneneri woona, pomwe aneneri ena ankanena uthenga wotsutsana ndi uthenga wake?

[Zithunzi pamasamba 8, 9]

Anthu a ku Bereya anamvetsera uthenga wa Paulo koma kenaka anafufuza Malemba kuti atsimikizire ngati zimene Pauloyo ananena zinalidi zoona

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Kuphunzira Baibulo mosamala kungakuthandizeni kudziwa chipembedzo choona