Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Zikhulupiriro za Makolo N’zogwirizana ndi Baibulo?

Kodi Zikhulupiriro za Makolo N’zogwirizana ndi Baibulo?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Zikhulupiriro za Makolo N’zogwirizana ndi Baibulo?

MTOLANKHANI wina anasiya kuyenda pandege kwa chaka chathunthu chifukwa choti munthu wina wolosera za m’tsogolo anamuuza kuti adzafa pangozi yandege. Anthu osiyanasiyana monga andale, abizinesi, ochita zisudzo, akatswiri a masewera osiyanasiyana komanso ophunzira a ku koleji, amatsatira zikhulupiriro zosiyanasiyana za makolo. Akathedwa nzeru, akakhala pavuto, kapena akakhala ndi nkhawa, amaona kuti zikhulupiriro zimenezi zimawateteza kapenanso zimawathandiza kukwaniritsa zolinga zawo.

Anthu ochuluka amaona kuti zambiri mwa zikhulupiriro zoterezi zilibe vuto lililonse, ndipo amaona kuti zimawalimbitsa mtima. Malemu Margaret Mead, yemwe anali katswiri wa chikhalidwe cha anthu anati: “Kukhulupirira zimenezi, kwenikweni n’kungolakalaka kuti zinazake zichitike kapena zisachitike. Ngakhale kuti ambirife timadziwa kuti zikhulupirirozi ndi zabodza, zimatipatsabe kanthu kenakake kodalira.” Ngakhale zili choncho, anthu amene akufunadi kusangalatsa Mulungu, ayenera kudzifunsa kuti, ‘kodi zikhulupiriro zimenezi n’zogwirizana ndi Chikhristu?’

Amene Anayambitsa Zikhulupirirozi

Anthu akhala akuvutika chifukwa choopa zinthu zosiyanasiyana monga imfa ndi zinthu zina zosadziwika. Akhalanso akuopa zimene zimachitika munthu akafa. Satana, yemwe anapandukira Mulungu, akuyesetsa kuchititsa anthu kukhala akapolo a zikhulupiriro zochititsa mantha, powauza mabodza ambirimbiri. (Yohane 8:44; Chivumbulutso 12:9) Satana sakuchita yekha zimenezi. M’Baibulo, Satana amatchedwa kuti “wolamulira ziwanda.” ( Mateyo 12:24-27) Kodi ziwanda ndi ndani? M’nthawi ya Nowa, angelo ena anagwirizana ndi Satana, ndipo anakhala ziwanda. Kuchokera nthawi imeneyo, ziwanda zakhala zikukopa anthu kuti apandukirenso Mulungu. Njira imodzi imene ziwanda zimagwiritsa ntchito ndiyo zikhulupiriro za makolo.—Genesis 6:1, 2; Luka 8:2, 30; Yuda 6.

Limodzi mwa mabodza a Satana amene amachititsa anthu kukhulupirira zoterezi ndi bodza lakuti chinthu chinachake chosaoneka chimakhalabe ndi moyo pamene munthu wafa ndiponso kuti chingabwere kudzavulaza kapena kudzathandiza anthu otsala. Koma Baibulo limati: “Akufa sadziwa kanthu bi.” Limanenanso kuti kumanda kulibe “ntchito ngakhale kulingirira ngakhale kudziwa, ngakhale nzeru.”—Mlaliki 9:5, 10.

‘Yehova Amanyansidwa Nazo’

Pali anthu ambiri amene asankha okha kukhulupirira mabodza a Satana. Komatu zaka zambirimbiri zapitazo, Mulungu anauza Aisiraeli, omwe anali anthu ake, malangizo omveka bwino pankhani imeneyi. Mawu ake anati: “Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wake wamwamuna kapena mwana wake wamkazi ku moto wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza aliyense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”—Deuteronomo 18:10-12.

N’zomvetsa chisoni kuti Aisiraeli nthawi zina sankamvera chenjezo limeneli. Mwachitsanzo, m’masiku a mneneri Yesaya, ena ankakhulupirira kuti angathe kukolola zambiri ngati atasangalatsa ‘mulungu wa mwayi,’ ndipotu chikhulupiriro chimenechi n’chimene chinawalowetsa m’mavuto adzaoneni chifukwa Yehova anasiya kuwadalitsa ndi kuwayanja.—Yesaya 65:11, 12.

Chikhristu chitayamba, Yehova sanasinthe mmene amaonera zikhulupiriro zimenezi. Mtumwi Paulo analimbikitsa anthu otsatira zikhulupiriro zoterezi a mumzinda wa Lusitara kuti asiye “zachabechabe [kapena kuti “zikhulupiriro za makolo,” Baibulo la The Emphatic Diaglott] zimenezi ndi kutembenukira kwa Mulungu wamoyo. Inde, amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.”—Machitidwe 14:15.

Kusiya Zikhulupirirozi

Pali zikhulupiriro zambirimbiri zomwe anthu amatsatira ndipo zonsezi n’zofanana m’njira yakuti sizikhala ndi mfundo zomveka zotsimikizira kuti ndi zoona. Mwa zinthu zina, zikhulupirirozi zingathe kuchititsa anthu kuona kuti akamakumana ndi mavuto ndiye kuti ali ndi tsoka, m’malo movomereza kuti atuta zimene anafesa.

N’zosangalatsa kuti anthu ambiri asiya zikhulupiriro zamakolo. Yesu anati: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Clementina, yemwe amakhala ku Brazil, anali wolosera za m’tsogolo kwa zaka 25. Iye anati: “Ntchito yolosera zam’tsogolo inali ntchito yokhayo imene ndinkapezera ndalama pa moyo wanga. Koma choonadi cha m’Baibulo chinandimasula ku zikhulupiriro za makolozi.” Kunena zoona, kuphunzira Baibulo nthawi zonse ndiponso kupemphera kwa Yehova Mulungu mochokera pansi pa mtima ndiko kungatithandizedi kukhala olimba mtima. Zimenezi zingatithandize kukhazika pansi maganizo ndiponso kuchita zinthu moganizira bwino n’kupewa mavuto ndi kutichepetsera nkhawa.—Afilipi 4:6, 7, 13.

Baibulo limafunsa kuti: “Pali kuyanjana kwanji pakati pa kuwala ndi mdima? Ndiponso, pali m’gwirizano wanji pakati pa Khristu ndi Beliyali [Satana]?” Motero, Akhristu oona ayenera kupewa zikhulupiriro za makolo.—2 Akorinto 6:14-16.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ M’malo modalira Mulungu, kodi Aisiraeli a m’nthawi ya Yesaya ankakhulupirira ndani?—Yesaya 65:11, 12.

▪ Kodi mtumwi Paulo anawalimbikitsa kuchita chiyani anthu a ku Lusitara amene anali ndi zikhulupiriro za makolo?Machitidwe 14:15.

▪ Kodi zikhulupiriro za makolo n’zogwirizana ndi Chikhristu choona?—2 Akorinto 6:14-16.

[Chithunzi patsamba 10]

Zikhulupiriro za makolo zimachititsa anthu kudzinamiza kuti sangakumane ndi chovuta chilichonse