Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuchokera kwa Owerenga

Kuthandiza Achinyamata Masiku Ano Kupeza Zomwe Amafunikira (March 2007) Ndili ndi zaka 18, motero mfundo zambiri zotchulidwa m’nkhaniyi zokhudza kugwiritsira ntchito foni ndiponso Intaneti zandithandiza kwambiri. Ndinkacheza ndi anthu osawadziwa pa Intaneti. Posakhalitsa mayanjano oipa amenewa anandigwetsa m’mavuto. Ndipo posapita nthawi moyo wanga wauzimu unayamba kulowa pansi. Ndinafika povomera kukumana pamasom’pamaso ndi anthu angapo oterewa. Ndikumva chisoni kuti zimenezi zinandifikitsa pochita zadama. Ndikupemphera kuti nkhani imeneyi ithandize ena kupewa mavuto amene ndikukumana nawo. Usiku ndimasowa tulo ndipo zinthu zonsezo ndimalephera kuzichotsa m’maganizo moti tsiku lililonse ndimavutika kwambiri, koma tsopano ndatsimikiza mtima kukanitsitsa kunyengedwa ndi Satana.

B. R., United States

Bwanji Ndimakomokakomoka? (April 2007) Ndinalimbikitsidwa kwambiri kudziwa kuti si ine ndekha amene ndimadwala matenda okomoka. Powerenga nkhani imeneyi ndinkangomva ngati Yehova akulankhula nane mwachindunji, n’kundiuza kuti: “Ndikudziwa zimene zikukuchitikira, n’chifukwa chake ndikukulimbikitsa ndi mawu awawa.”

I. R., Madagascar

Chinthu Chokhalitsa Kuposa Luso la Zosemasema ndi Zoumbaumba (April 2007) Ndikuchita kusowa chonena kuti ndikuthokozeni polemba nkhani imeneyi. Kwa zaka 6, ndinkagwira ntchito yoyang’anira malo awiri ojambula ndi kutsuka zithunzi. Ntchitoyi ndinkaikonda kwambiri chifukwa inkandipatsa mwayi wosonyeza luso langa. Koma ndinazindikiranso kuti utumiki wanga kwa Yehova wayamba kulowa pansi chifukwa choti ntchitoyi inkayenda bwino kwabasi ndipo ndinayamba kutchuka nayo kwambiri. Ndinkalimbikira kwambiri kupititsa patsogolo luso langali moti sindinkakhala ndi nthawi yokwanira yochitira zinthu zina. Ndinadziwa kuti m’pofunika kuti ndisinthe basi. Motero ndinasiya ntchitoyo n’kuyamba kulimbikira kwambiri zinthu zauzimu. Inde ndinkasangalala ndikatulutsa zithunzi zambambande, komatu chisangalalo chimene ndimakhala nacho panopa pochita utumiki wachikhristu n’chosasimbika ngakhale pang’ono.

A. P., United States

Mafunso Amene Achinyamata Amadzifunsa . . . Kodi Munthu Ameneyu Ndi Woyenera Kumanga Naye Banja? (May 2007) Posachedwapa ndinayamba kukondana ndi mnyamata wina amene ndinkaona kuti tingayenererane kwambiri. Komano, nditawerenga nkhani imeneyi, ndinazindikira kuti makhalidwe amene ndinakopeka nawo sanali ofunika kwenikweni. Nkhaniyi inandithandiza kuzindikira kuti chofunika kwambiri ndicho makhalidwe auzimu ndiponso mmene munthuyo amachitira zinthu ndi ena. Ndikuthokoza Yehova potipatsa nkhani ngati zimenezi chifukwa zimatiteteza ndi kutilangiza achinyamatafe.

E.  P., United States

Adziweni Anthu a ku East Timor

(May 2007) Nkhaniyi inandichititsa chidwi kwambiri poiwerenga. Ndinayamba kumva za dziko la East Timor panthawi imene pankafalitsidwa nkhani zokhudza kumenyana kumene kunkachitika m’dzikolo. Kuyambira nthawi imeneyo ndakhala ndikuda nkhawa poganizira za moyo wa anthu a ku East Timor ndiponso mmene nkhondoyi inakhudzira ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova. Ndinadabwa kwambiri ndi mzimu wawo, chifukwa sanalole kuti nkhondoyo isokoneze moyo wawo, koma akuchitabe khama kuti azikhala bwinobwino. Sindidzaiwala anthu a ku East Timor chifukwa cha mtima wawo wosagonja ndiponso sindidzaiwala nkhope zachimwemwe za Jacob ndi anthu a m’banja lake.

Y. M., Japan