Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulalikira Uthenga Wabwino ku Madera Akutali

Kulalikira Uthenga Wabwino ku Madera Akutali

Kulalikira Uthenga Wabwino ku Madera Akutali

Yosimbidwa ndi Helen Jones

Tsiku lina chakumayambiriro kwa m’ma 1970, ndinkayenda mu msika wina wodzadza ndi anthu mumzinda wa Bangalore ku India. Mwadzidzidzi kunangotulukira njati ndipo inandigunda n’kundigwetsera pansi. Kenaka, ikuti iyambe kundipondaponda mayi wina wachimwenye anabwera n’kundipululmutsa. Kodi ndinkachitako chiyani ku India?

NDINABADWA mu 1931 ndipo ndinakulira mu mzinda wokongola wa Vancouver, ku Canada. Makolo anga anali a makhalidwe abwino koma sankapita ku tchalitchi chilichonse. Komabe, ndinkakonda kwambiri zinthu zauzimu ndipo ndili wachinyamata ndinkakonda kupita ku Sande Sukulu komanso ku maphunziro ena a za Mawu a Mulungu.

Mu 1950, ndili ndi zaka 19, ndinakwatiwa ndi Frank Schiller, amene anali kale ndi ana anayi kuchokera kwa mkazi wake woyamba. Patatha zaka ziwiri tinakhala ndi mwana wamwamuna. Tinkafuna kuti tizipemphera; koma palibe tchalitchi chimene chinalola kuti tizikapempherako, chifukwa choti Frank anali atasudzulana ndi mkazi wake woyamba. Zimenezi zinam’khumudwitsa kwambiri motero sankafuna kukambirana nkhani za chipembedzo ndi aliyense.

Tinaphunzira Choonadi

Mu 1954, mchimwene wanga anandiuza mosangalala zinthu zimene mnzake wakuntchito, yemwe anali wa Mboni za Yehova anamuonetsa m’Baibulo. Ngakhale kuti ndinali ndi mafunso ambiri ndipo ndinkadziwa kumene a Mboni ankachitira misonkhano yawo, sindinkapitako chifukwa choti Frank ankadana ndi zachipembedzo. Patapita nthawi, a Mboni awiri anafika pakhomo pathu. Ndinawafunsa kuti andiuze zimene Baibulo limanena pankhani ya kusudzulana, ndipo anandisonyeza m’Baibulo malemba osonyeza zifukwa zololeka zimene anthu angasudzulirane. (Mateyo 19:3-9) Anandilimbikitsanso kuti ngati nditalola kuphunzira nawo Baibulo nthawi zonse, ndingathe kumvetsa zinthu zambiri zimene zinkandivutitsa maganizo.

Nditayamba kuphunzira nawo, mwamuna wanga sanasangalale nazo ngakhale pang’ono, chifukwa iyeyo ankadana ndi a Mboni. Mu 1955, ndinapita ku mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Khristu, ndipo nditafika ku nyumba, ndinayamba kumuuza Frank mosangalala zinthu zonse za m’Baibulo zimene ndinakaphunzirako. Iye anakalipa n’kunena kuti: “N’zabodza zimenezo! Ngati utandionetsa lemba limene limanena zimenezo m’Baibulo, ndingalolere ngakhale kupita ku misonkhano yako yopusayo.”

Ndinam’patsa Baibulo, ndipo analilandira mwaulemu. Tinayamba kuona malemba onse amene ndinalemba, ndipo sindinalankhule zambiri, pofuna kuti adzionere yekha m’Baibulomo. Frank sanachite makani ndipo usiku wonsewo ankaoneka kuti akuganizira kwambiri zimene tinakambiranazo.

Patapita nthawi, ndinam’kumbutsa mawu amene ananena aja, akuti adzapita ku misonkhano yathu. Iye anavomera monyinyirika ponena kuti, “Chabwino, ndipita kamodzi kokha, kuti ndikangoona zimene mumachita.” Nkhani ya Baibulo imene inakambidwa inafotokoza zakuti akazi ayenera kugonjera amuna awo. (Aefeso 5:22, 23, 33) Nkhaniyi inam’sangalatsa kwambiri. Chapanthawi yomweyo, Frank anafika pa phunziro la Nsanja ya Olonda, ya mutu wakuti “Muzisangalala ndi Ntchito.” Frank anali munthu wokonda ntchito kwambiri moti anasangalala zedi ndi nkhaniyi. Kuchokera pamenepo, iye sanaphonyeko msonkhano uliwonse. Posakhalitsa Frank anayamba kulalikira mwakhama kwambiri, ndipo inenso ndinkaphunzira Baibulo ndi anthu angapo amene anapita patsogolo mpaka kubatizidwa. Chaka chomwecho, ineyo ndi Frank, komanso mayi anga ndi mchimwene wanga, tinabatizidwa posonyeza kudzipereka kwa Mulungu.

Tinkalakalaka Kuchita Zambiri

Pa msonkhano wathu wachigawo womwe unachitikira ku Seattle, ku Washington, m’dziko la United States m’chaka cha 1957, panakambidwa nkhani yomwe inalimbikitsa anthu kukatumikira ku madera kumene kunalibe anthu ambiri olalikira za Ufumu. Ndinapemphera kwa Yehova n’kumuuza kuti: ‘Chonde Yehova, ndithandizeni kuti ndikhale mmodzi wa anthu amenewa.’ Koma Frank ankada nkhawa poganizira za udindo wake wosamalira banja lathu.—1 Timoteyo 5:8.

Chaka chotsatira, banja lathu linapita ku msonkhano wa ku New York City womwe unachitikira ku Yankee Stadium ndi ku Polo Grounds panthawi imodzi. Pamsonkhanowu panali anthu 253,000 amenenso anamvetsera nkhani ya anthu onse. Frank anakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene anaona ndi kumva pamsonkhanowu. Motero pobwerera kwathu tinapangana kuti tidzapita ku Kenya n’kukakhazikika kumeneko, chifukwa choti m’dzikolo amalankhula Chingelezi motero tinadziwanso kuti ana athu sakavutika pankhani ya sukulu.

Mu 1959, tinagulitsa nyumba yathu n’kulongedza katundu wathu ndipo tinayamba ulendo wautali wa pagalimoto wopita ku Montreal m’dziko la Canada. Titachoka kumeneku, tinakwera sitima yapamadzi yopita ku London, m’dziko la England, ndipo titachoka ku England tinakweranso sitima ina yapamadzi yomwe inadutsa m’nyanja ya Mediterranean ndi ya Red Sea mpaka kukafika m’nyanja ya Indian. Pamapeto pake tinafika ku Mombasa, m’dziko la Kenya, lomwe lili m’mphepete mwa nyanja, cha kum’mawa kwa Africa. Tsiku lotsatira tinakwera sitima yapamtunda n’kukafika ku Nairobi, lomwe ndi likulu la dziko la Kenya.

Tinapeza Madalitso ku Africa

Panthawiyo ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova inali yoletsedwa ku Kenya, motero tinkalalikira mosamala. M’dzikoli munalinso mabanja ena ochokera kunja, chifukwa choti malamulo ake ankalola anthu akunja kukhalamo bwinobwino. Tinkaonetsetsa kuti misonkhano yathu izikhala ndi anthu osapitirira 10. Motero mabanja athu, kuphatikizapo ana athu, ankatenga nawo mbali kwambiri pamisonkhanoyo.

Titangokhala ku Kenya nthawi yochepa chabe, tinapeza malo ndipo Frank anapeza ntchito. Mayi amene ndinayamba kum’peza mu ulaliki wa khomo ndi khomo anavomera kuphunzira Baibulo ndipo pambuyo pake anadzakhala mpainiya, lomwe ndi dzina la atumiki a nthawi zonse a Mboni za Yehova. Ndinkaphunziranso ndi mtsikana wina wachimwenye, wachipembedzo chotchedwa Sikh, dzina lake Goody Lull. Iyeyu sanafooke ngakhale kuti anthu a m’banja mwake ndiponso a chipembedzo chake ankalimbana naye kwambiri. Pambuyo pake mtsikanayu anam’thamangitsa ku nyumba kwawo, moti anayamba kukhala ndi banja linalake la Mboni. Atatero anadzipereka kwa Yehova, n’kukhala mpainiya, ndipo kenaka anapita ku sukulu ya Gileadi, yophunzitsa umishonale.

Banja lathu linakumana ndi zovuta zingapo. Mwana wathu wamwamuna woyamba anadwala matenda enaake ophwanya m’thupi, ndiponso Frank anavulala kwambiri ndi moto wa mafuta a galimoto motero anam’chotsa ntchito. Pambuyo pake anapezanso ntchito ku Dar es Salaam, ulendo wa makilomita 1,000 kuchokera kumene tinkakhala. Mzinda umenewu unali likulu la dziko la Tanganyika (lomwe pano amati Tanzania). Choncho tinasamuka pagalimoto n’kupita kumeneku. Panthawiyo ku Dar es Salaam kunali mpingo wa anthu ochepa chabe, komabe anthuwo anatilandira ndi manja awiri.

Ngakhale kuti ntchito yathu inali italetsedwa ku Tanzania, aboma sankalimbana nafe kwambiri. Mu 1963, Milton Henschel, wochokera ku likulu la Mboni za Yehova, ku United States, anatiyendera. Akukamba nkhani yake pa holo yotchedwa Karimjee, yomwe ndi holo yabwino kwambiri m’dzikomo, bambo wina wachikulire wovala zonyozeka, anabwera n’kukhala pafupi ndi ine. Ndinam’patsa moni ndipo tinkaonera limodzi Baibulo ndi buku langa la nyimbo. Msonkhanowo utatha, ndinam’pempha kuti adzabwerenso. Munthuyo atapita, abale ndi alongo anabwera msangamsanga kudzalankhula nane.

Iwo anandifunsa kuti: “Kodi mukumudziwa amene uja? Amene ujatu ndiye meya wa mzinda wa Dar es Salaam!” Meyayu anali ataopseza kuti adzaletsa msonkhano wathu. Zikuoneka kuti anavala dala zonyozeka kuti atitole zifukwa ngati titamunyoza. Koma anachita chidwi kwambiri chifukwa chakuti tinamusamalira bwino kwambiri moti analola kuti msonkhanowo upitirire popanda kusokonezedwa. Pamsonkhanopo panabwera anthu 274 ndipo 16 anabatizidwa.

Tili ku Tanzania, dzikolo linalandira ufulu wodzilamulira. Zitatero nzika za dzikolo n’zimene zinkapeza ntchito mosavuta. Motero anthu ambiri akunja anayamba kuchoka m’dzikolo. Komabe khama la Frank pofufuza ntchito linapindula, moti anapeza ntchito ina yokonza injini za sitima. Zimenezi zinathandiza kuti tikhalebe m’dzikomo kwa zaka zinayi. Ntchito ya Frank itatha, tinabwerera ku Canada, ndipo tinakhala kumeneko mpaka pamene mwana wathu womaliza anapeza banja. Tinkaonabe kuti tidakali achinyamata ndithu moti pali zambiri zimene tingathebe kuchita muutumiki.

Tinapita ku India

Mu 1970, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Bombay (komwe tsopano amati ku Mumbai) inavomereza kuti tikachite utumiki mumzinda wa Bangalore, womwe panthawiyo unali ndi anthu opitirira 1 miliyoni ndi theka. Kumeneku n’kumene ndinapulumukira m’kamwa mwa mbuzi pamene njati inkafuna kundipondaponda, monga ndafotokozera poyamba paja. Panthawiyo kunali mpingo wa Chingelezi wa anthu 40 ndiponso kagulu kakutali komwe kankalankhula Chitamilu. Frank ankaphunzira Baibulo ndi anthu angapo amene anapita patsogolo kwambiri moti anadzakhala akulu mumpingo. Inenso ndinkaphunzira ndi mabanja ambiri amene anadzakhala atumiki a Yehova.

Mzimayi wina dzina lake Gloria ankakhala m’dera lina la anthu osauka kwambiri m’tauni ina ya kumeneku. Tsiku loyamba nditafika pakhomo pake anandiuza kuti ndilowe m’nyumba mwake. Tinakhala pansi chifukwa munalibe mipando. Ndinamusiyira Nsanja ya Olonda, ndipo anatenga magaziniyo n’kudula pamene panalembedwa lemba la Chivumbulutso 4:11 n’kumata kapepalako pakhoma kuti azitha kukaona tsiku ndi tsiku. Ena mwa mawu amene anali pa kapepalako anali mawu akuti: “Ndinu woyenera, inu Yehova,” chifukwa iyeyu ankawakonda kwambiri mawu amenewa. Patatha chaka chimodzi iye anabatizidwa.

Frank anaitanidwa kuti akagwire ntchito kwa chaka chimodzi pa ofesi yanthambi ku Bombay ndi kuti akayang’anire ntchito yomanga Nyumba ya Msonkhano yoyamba ya Mboni za Yehova ku India. Nyumbayi anaimanga powonjezera nsanja imodzi pamwamba pa nyumba ya ofesi ya nthambi. Panthawiyo n’kuti ku India, kuli Mboni zoposa 3,000 ndipo pa ofesi ya nthambi panali anthu osakwana 10. Mu 1975, ndalama zathu zinatha, motero zinali zachisoni kusamuka m’dzikolo n’kusiyana ndi anzathu apamtima.

Tinabwereranso ku Africa

Patatha zaka 10 Frank anayamba kulandira ndalama za anthu opuma pantchito. Motero tinadziperekanso kukathandiza pa ntchito yomanga maofesi a nthambi m’mayiko osiyanasiyana. Tinalandira kalata yotipempha kuti tipite ku Igieduma ku Nigeria, kukachita ntchito yotereyi. Tili kumeneko, Frank anaphunzira Baibulo ndi munthu wina wa m’mudzi wapafupi amene anapita patsogolo kwambiri moti m’tsogolo mwake anadzayamba kutumikira pa ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ku Nigeria.

Titachoka kumeneku tinapita ku Zaire kukathandiza pa ntchito yomanga ofesi ya nthambi. Posakhalitsa, kumeneku analetsa ntchito yolalikira ndipo boma linalanda mapasipoti athu. Frank anadwala matenda a mtima akugwira ntchito komabe anapeza bwino panthawi imene ntchito yathuyo inaletsedwa. Kenaka, tonse ogwira ntchito yomanga anatiuza kuti tichoke m’dzikomo ndipo ineyo ndi mwamuna wanga tinatumizidwa ku Liberia. Tinakakhala pa ofesi ya nthambi ku Monrovia, ndipo Frank anapemphedwa kuti akonze makina a jenereta. Ziphaso zathu zokhalira m’dzikomo zinatha mu 1986, motero tinabwereranso ku Canada.

Tinafika ku Ecuador

Posakhalitsa, tinamva kuti mnzathu wina, dzina lake Andy Kidd, wasamukira ku Ecuador ndipo akusangalala kwambiri ndi ntchito yolalikira kumeneko. Mpingo umene ankapitako unalibe akulu ena kupatulapo iyeyo basi, moti nthawi zambiri nkhani zambiri pampingopo ankakamba yekha. Iyeyu atatiitana, tinapita ku ofesi ya nthambi ya ku Ecuador mu 1988 ndipo tinalandiridwa ndi manja awiri.

Tinapeza nyumba yabwino ndithu yoti tizikhalamo, koma tinafunikira kuphunzira Chisipanishi ngakhale kuti Frank anali ndi zaka 71. Patatha zaka ziwiri, ngakhale kuti tinkalankhula Chisipanishi chothyokathyoka,tinali titathandiza anthu 12 n’kufika pobatizidwa. Frank anapemphedwa kuti athandize pa ntchito yomanga pa ofesi ya nthambi ya ku Ecuador. Ankaphunziranso Baibulo ndi mwamuna wina amene mkazi wake anali munthu woyamba wa ku Guayaquil kukhala wa Mboni za Yehova. Mwamuna ameneyu, yemwe anali kutsutsa mkazi wake kwa zaka 46, anakhala mnzathu wapamtima ndiponso m’bale wauzimu.

Ndinataya Mnzanga Wapamtima

Tinasamukira m’tauni yaing’ono yotchedwa Ancón, kufupi ndi nyanja ya Pacific Ocean, ndipo kumeneku tinathandizanso pa ntchito yomanga Nyumba ya Ufumu yatsopano. N’zachisoni kuti pa November 4, 1998, Frank anadwala matenda a mtima atangomaliza kukamba nkhani yotsiriza pa Msonkhano wa Utumiki, ndipo anamwalira usiku womwewo. Abale ndi alongo athu auzimu anatithandiza kwambiri. Tsiku lotsatira Frank anaikidwa m’manda omwe ali tsidya lina la msewu kuchokera pa Nyumba ya Ufumu yathu. Ndinali ndi chisoni chosaneneka.

Ndinabwereranso ku Canada, kungoti ulendo uno ndinali ndekha. Ulendowu unali wokasamalira anthu am’banja mwanga komanso kukasamalira nkhani zina ndi zina. Ngakhale kuti ndinali ndi chisoni chachikulu, Yehova sananditaye. Ndinalandira kalata kuchokera ku ofesi ya nthambi ya Ecuador yondidziwitsa kuti ndikufunikanso ku Ecuador ngati ndingakonde kubwererako. Motero ndinabwereradi ndipo ndinapeza kanyumba pafupi ndi ofesi ya nthambi. Ndinali wotanganidwa kwambiri panthambipo, komanso mu utumiki, ndipo zimenezi zinandithandiza kuti chisoni changa chisakule kwambiri chifukwa choganizira mwamuna wanga. Komabe nthawi zina ndinkasungulumwa kwambiri.

Kupitirizabe Utumiki

Patapita nthawi, ndinadziwana ndi Junior Jones. Iyeyu anafika ku Ecuador mu 1997 kuchokera ku United States, kuti adzachite upainiya. Tinali ndi zolinga zofanana komanso zokonda zathu zinali zimodzi. Motero, tinakwatirana mu October 2000. Junior anali ndi luso la zomangamanga, motero tinaitanidwa kukamaliza nawo ntchito yomanga Nyumba ya Msonkhano ku Cuenca, mzinda womwe uli m’dera la mapiri a Andes. Kenaka pa April 30, 2006, Geoffrey Jackson wa m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova anabwera kuchokera ku New York n’kudzakamba nkhani yopatulira nyumbayo, ndipo panasonkhana anthu 6,554.

Palibe amene ankadziwa kuti ntchito yolalikira za Ufumu ingapite patsogolo chonchi m’madera akutali ngati ku Africa, India, ndi South America. Ineyo ndi Junior tilibe maganizo aliwonse opuma pa utumiki wathu. Zaka 50 zimene ndakhala ndikutumikira Yehova zadutsa mwamsanga kwambiri moti zimangooneka ngati kuti ndayamba kutumikira dzulodzuloli. Ndipo ndikudziwa kuti dziko latsopano likadzabwera, nthawi imene tikukhala ino izidzangoonekanso ngati dzulodzuloli.—Chivumbulutso 21:3-5; 22:20.

[Mapu/Chithunzi patsamba 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Kumene Tatumikira

CANADA → ENGLAND → KENYA → TANZANIA

CANADA → INDIA

CANADA → NIGERIA → CONGO, DEM. REP. (ZAIRE) → LIBERIA

CANADA → ECUADOR

[Malo Ena]

UNITED STATES OF AMERICA

[Chithunzi]

Ndili ndi Frank ku India, tikupita ku msonkhano

[Chithunzi patsamba 15]

Ndili ndi mwamuna wanga Junior Jones