Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndani Angatisonyeze Chipembedzo Choona?

Ndani Angatisonyeze Chipembedzo Choona?

Ndani Angatisonyeze Chipembedzo Choona?

YESU ananena momveka bwino kuti kulambira kwina n’kosavomerezeka kwa Mulungu. Iye anatchulapo za “aneneri onyenga,” ndipo anawayerekezera ndi mtengo wobala zipatso zopanda pake womwe “amaudula ndi kuuponya pamoto.” Iye anatinso: “Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa ufumu wa kumwamba ayi.”—Mateyo 7:15-22.

Ndipotu ponena za anthu ena amene amati ndi otsatira ake, Yesu anati: “Pamenepo ine ndidzawauza mwachimvekere kuti: ‘Sindinakudziweni konse chiyambire! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.’” (Mateyo 7:23) Komanso, polankhula ndi atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake, Yesu anagwira mawu amene Mulungu ananena kwa Aisiraeli opanduka. Iye anati: “Amandilambira ine pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu monga ziphunzitso za Mulungu.”—Maliko 7:6, 7.

Pamenepa n’zoonekera kuti Mulungu ndiponso Mwana wake savomereza kupembedza konse. Choncho, si kupembedza konse kumene kuli koona. Kodi zimenezi zikutanthauza kuti pali chipembedzo chimodzi chokha chimene chimaphunzitsa choonadi? Kodi mwina Mulungu amagwiritsa ntchito zipembedzo zochepa chabe koma zina zonse sazivomereza? Kapena mwinanso amavomereza kulambira kwa anthu enaake a m’zipembedzo zosiyanasiyana, mosaganizira ziphunzitso za zipembedzozo?

Mouziridwa ndi Mulungu, mtumwi Paulo analemba mawu otsatirawa: “Tsopano ndikukudandaulirani abale, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula chinthu chimodzi, ndi kuti pasakhale magawano pakati panu, koma kuti mukhale ogwirizana bwino lomwe pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” (1 Akorinto 1:10) Baibulo limalimbikitsanso Akhristu kuti ‘akhale ndi maganizo amodzi, ndi chikondi chofanana komanso ogwirizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi.’—Afilipi 2:2.

Pakakhala umodzi woterewu, zotsatira zake zimakhala chipembedzo chimodzi. Mogwirizana ndi mfundo imeneyi, Baibulo limati palinso “Ambuye mmodzi, chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi.”—Aefeso 4:4, 5.

Zimene Baibulo Limanena

Tikamawerenga Baibulo timapeza umboni wotsimikizira kuti mfundo tatchula pamwambayi ndi yogwirizanadi ndi Malemba. Timaona kuti Mulungu ankagwiritsa ntchito chipembedzo chimodzi chokha pochita zinthu ndi anthu ake. Kalekale, Mulungu ankagwiritsira ntchito makolo, kapena mitu ya mabanja monga anthu omuimira. Makolo ena otere omwe ali odziwika bwino, ndi anthu monga Nowa, Abulamu, (Abulahamu), Isake, ndi Yakobo.—Genesis 8:18-20; 12:1-3; 26:1-4; 28:10-15.

Ana a Yakobo anakhala akapolo ku Iguputo. Ali kumeneko, anazunzidwa kwambiri komabe anachuluka mpaka mamiliyoni. Mulungu anawawombola mu ukapolowu ndipo anawawolotsa modabwitsa pa Nyanja Yofiira. Kenaka anawasankha kuti akhale anthu ake ndipo anawapatsa malamulo kudzera mwa Mose, yemwe anali mkhalapakati. Pamenepa, anthuwa anakhala mtundu wa Isiraeli, womwe unali mtundu wosankhidwa ndi Mulungu.—Eksodo 14:21-28; 19:1-6; 20:1-17.

Mfundo yofunika kuiganizira bwino ndi yakuti Mulungu sanavomereze kulambira kwa mitundu ya anthu ozungulira Aisiraeli. Ndipotu analanga anthu akewa atapanduka posiya malamulo ake n’kutengera kupembedza kumeneko.—Levitiko 18:21-30; Deuteronomo 18:9-12.

Nanga bwanji za anthu osiyanasiyana a mitundu ina amene ankafuna kupembedza Mulungu woona? Iwo anafunikira kusiya kaye kupembedza konyengako, n’kuyamba kupembedza Yehova Mulungu pamodzi ndi Aisiraeli. Ambiri mwa anthu amenewa anayamba kuyanjidwa ndi Mulungu ndipo anali atumiki ake okhulupirika. Ena mwa anthu amenewa anali akazi monga Rahabi, yemwe anali wachikanani, ndi Rute, yemwe anali wachimoabu, komanso amuna monga Uriya, yemwe anali Mhiti, ndi Ebedimeleki, yemwe anali Mkusi limodzinso ndi magulu ena a anthu, monga Agibeoni. Nthawi ina, mfumu ya Isiraeli, Solomo, inapereka pemphero lochokera pansi pamtima loimira anthu onse amenenso panthawiyo anayamba kulambira Yehova pamodzi ndi anthu a Mulungu. *2 Mbiri 6:32, 33.

Yesu Atabwera Padziko Lapansi

Pambuyo pake, Yesu anatumizidwa padziko lapansi, ndipo anakhazikitsa kulambira koona mwa zimene ankaphunzitsa. Iye anafotokozanso momveka bwino za cholinga cha Mulungu. Patapita nthawi, olambira oona anayamba kutchedwa kuti “Akhristu.” (Machitidwe 11:26) Motero, Ayuda amene ankafuna kuyanjidwa ndi Mulungu anayenera kusiya kulambira kwawo kwakale. Mulungu sanalole kuti asankhe okha pakati pa Chiyuda ndi Chikhristu, kapena kuwalola kuti azitha kumapembedza pawokhapawokha. Monga taonera m’Mawu a Mulungu, olambira oona anali ogwirizana pa “chikhulupiriro chimodzi.”—Aefeso 4:4, 5.

Masiku ano, ena angaone kuti maganizo akuti Mulungu amagwiritsira ntchito chipembedzo chimodzi chokha ndi okokomeza zinthu ndipo sangasangalale nawo. Komatu zimenezi ndi zimene Baibulo limanena. Kale, anthu ambiri amene ankalambira mmene iwowo akufunira anafika pozindikira mfundo imeneyi. Iwo anayamba kulambira Yehova pamodzi ndi anthu ake, ndipo anadalitsidwa n’kukhala osangalala kwambiri atakhutira ndi zimene anaphunzitsidwa. Mwachitsanzo, Baibulo limati munthu wina wa ku Aitiopiya ataphunzira Chikhristu n’kubatizidwa, “anapitiriza ulendo wake akusangalala.”—Machitidwe 8:39.

Masiku ano, aliyense amene amavomereza ndi kutsatira mfundo za chipembedzo choona amapezanso madalitso ngati amenewa. Komano poti masiku ano zipembedzo zangoti mbwee, kodi mungadziwe bwanji chipembedzo choona?

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 11 Mungathe kuwerenga nkhani zokhudza anthu amenewa m’malemba otsatirawa: Yoswa 2:1-7; 6:22-25; Rute 1:4, 14-17; 2 Samueli 11:3-11; Yeremiya 38:7-13; ndi Yoswa 9:3-9, 16-21.

[Chithunzi patsamba 5]

Ngati chipembedzo chikubala zipatso zopanda pake, kodi chidzakumana ndi zotani m’tsogolo muno?