Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Tsiku Limene Kunada Masana”

“Tsiku Limene Kunada Masana”

“Tsiku Limene Kunada Masana”

YOLEMBEDWA KU BENIN

“KADAMSANA Akopa Chidwi cha Anthu Osaneneka.” Uwu unali mutu wa nkhani m’nyuzipepala ina ya ku Ghana (Daily Graphic) tsiku lotsatira pa March 29, 2006, pamene m’dzikoli munachitika kadamsana, dzuwa lonse n’kuphimbikiratu. Kadamsanayu, anayamba kuonekera cha kum’mawa kwa dziko la Brazil ndipo anayenda mpaka kufika m’mayiko a tsidya lina la nyanja ya Atlantic, pa liwiro la makilomita 1,600 pa ola limodzi, moti cha m’ma 8 koloko m’mawa anali atafika m’mayiko a m’mphepete mwa nyanjayi, monga Ghana, Togo, ndi Benin. Kodi kadamsanayu ankaoneka bwanji m’mayiko amenewa?

Nthawi yomaliza imene kadamsana wophimbiratu dzuwa lonse anaoneka ku Ghana inali mu 1947. Panthawiyo n’kuti gogo wina, dzina lake Theodore, ali ndi zaka 27 ndipo iyeyu akukumbikira kuti: “Ambiri panthawiyo anali asanaonepo kadamsana wotereyu chibadwire, motero sankadziwa kuti chikuchitika n’chiyani. N’chifukwa chake ambiri ankangoti tsiku limeneli ndi ‘tsiku limene kunada masana.’”

Kuyesetsa Kudziwitsa Anthu

Aboma anachita khama kwambiri kudziwitsa anthu za kuopsa koyang’ana dzuwa panthawi ya kadamsana. Iwo anamatamata zimapepala zokopa chidwi zolembedwa kuti: “Samalani! Mufa Maso.”

Aboma analimbikitsa anthu kusankhapo pakati pa zinthu ziwiri. Choyamba kukhala m’nyumba n’kumangoonerera kadamsanayo pa TV. Chachiwiri kukhala panja koma atavala magalasi oteteza maso ku kadamsana. Anthu ambiri anaonera kadamsanayu pa TV ndi pamakompyuta chifukwa ankaonetsapo zithunzi zochititsa chidwi kwambiri. Komatu zinali zosatheka kuonetsa pa TV chisangalalo ndiponso chidwi cha anthu pamene anali pakalapakala kukonzekera kuona kadamsanayu. Tatiyeni tioneko pang’ono chabe zina mwa zinthu zimenezi.

Kuyembekezera Mwachidwi

Patsikuli kunja kunacha bwinobwino ngati masiku ena onse. Moti panalibe chilichonse chachilendo choonetsa kuti kuchitika kadamsana. Nthawi imene analengeza kuti kuchitika kadamsana itayandikira, anthu onse amene anali panja anavalavala magalasi awo n’kuyamba kuyang’ana kumwamba. Ena anali kulankhula ndi anzawo pa mafoni a m’manja n’kumawafunsa ngati akumuona kadamsanayo kumene ali.

Panthawiyi m’mwambamo, pa mtunda wa makilomita 350,000, mwezi unali kuyenda pang’onopang’ono kuyandikira malo amene umati ukafikapo kumachitika kadamsana. Mwadzidzidzi unayamba kuonekera pang’ono kwambiri, kuti bii n’kuyamba kuphimba dzuwa lija. Kenaka kunamveka chiphokoso chachikulu chifukwa aliyense anayamba kuona kanthu koti bii kaja.

Pa ola loyambirira, kunja sikunasinthe kwenikweni. Koma mwezi uja utayamba kuphimba dzuwa, kunja kunasintha. Mtambo wobiriwira uja unayamba kuda. Kunja kunayamba kuzizira. M’dima unayamba kugwa ngakhale kuti unali m’mawa ndipo magetsi omwe amayaka okha kukayamba mdima komanso magetsi ena a mu msewu anayamba kuyaka. Kenako m’misewu munangoti zii. Malo onse a malonda anatsekedwa. Mbalame zinasiya kuimba, ndipo nyama zinayamba kukonzekera kugona. Mdima wandiweyani unawodira ndipo posakhalitsa unafika. Ndiyetu kunangoti zii.

Unali Mdima Wosaiwalika

Nyenyezi zinayamba kuoneka. Kuwala kwa dzuwa kunkangoonekera mozungulira mwezi wakudawo. * Kuwala kwa dzuwako kunaunika zigwa ndi mapiri osiyanasiyana a ku mwezi. Panaoneka kunyezimira kwinakwake kwangati kunyezimira kwa mwala wa dayamondi. Panaonekanso kuwala kwina kofiirira mozungulira mweziwo. Munthu wina yemwe anaona kadamsanayu anati: “Sindinaonepo zinthu zochititsa chidwi ngati zimenezi m’chilengedwe chonse.”

Mdima wandiweyani uja unakhala pafupifupi mphindi zitatu. Kenaka dzuwa linayambanso kukula mphamvu. Anthu ambiri oonerawo anayamba kulichemerera. Kunja kunawalanso ndipo nyenyezi zija zinazimilirika. Kunangokhala ngati kuti kwachanso.

Mwezi ndi “mboni yokhulupirika kuthambo.” Motero, n’zotheka kuwerengetseratu deti limene kudzachitike kadamsana, ngakhale zaka zambirimbiri m’tsogolo. (Salmo 89:37) Anthu a m’mayiko a kumadzulo kwa Africa anadikira zaka 60 kuti aone kadamsana ameneyu. Kumeneku kadamsana wina adzachitika m’chaka cha 2081. Koma n’kutheka kuti kwanuko achitika posachedwa ndithu ndipo mudzakhala ndi mwayi wodzamuona.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 13 Katswiri wina wa sayansi ya zakuthambo wa ku Britain, dzina lake Francis Baily, anali munthu woyamba kulemba za kuwala kumeneku, ataona kadamsana mu 1836.

[Bokosi/Chithunzi patsamba 29]

Kodi Mmene Yesu Ankafa Panachitika Kadamsana?

Lemba la Maliko 15:33 limati: “Nthawi itafika cha m’ma 12 koloko masana, kunagwa mdima m’dziko lonse mpaka 3 koloko masana.” Mdima wa maola atatu umenewu unali wozizwitsa. Sunachitike chifukwa cha kadamsana ayi. Choyamba, dziwani kuti kadamsana wokhala nthawi yaitali kwambiri, amakhala kwa mphindi 7 ndi theka basi. Chachiwiri, n’chakuti Yesu anafa pa tsiku la 14 la mwezi wa Nisani pa kalendala yoyendera mwezi. Tsiku loyamba la mwezi wa Nisani amaliwerengetsera mogwirizana ndi tsiku limene mwezi umakhala, ndipo patsikuli mwezi umakhala pakati pa dziko ndi dzuwa motero ungathe kuchititsa kadamsana. Koma pofika tsiku la 14, mwezi umakhala utayenda kale theka la ulendo wake wozungulira dziko. Choncho dziko ndilo limakhala pakati pa dzuwa ndi mwezi, motero mwezi suphimba dzuwalo ayi, koma umaonetsa kunyezimira konse kwa kuwala kwa dzuwa. Panthawiyi timatha kuona mwezi wathunthu. Iyitu imakhala nthawi yoyenerera kwambiri kuchita mwambo wa Chikumbutso cha imfa ya Yesu.

[Chithunzi]

Pa Nisani 14 mwezi umakhala wathunthu, apo ayi umakhala wokulirapo ndithu

[Chithunzi/Mapu pamasamba 28, 29]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

Mmene kadamsanayu anadutsa

⇧ AFRICA

BENIN ●

TOGO ●

GHANA ●

[Mawu a Chithunzi]

Map: Based on NASA/​Visible Earth imagery

[Chithunzi patsamba 28]

Kadamsana amene anaoneka pa March 29, 2006

[Chithunzi patsamba 28]

Anthu anavala magalasi oteteza maso kuti aone okha kadamsanayo