Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Zochitika Padzikoli

Atafufuza ku United States anapeza kuti “amuna 29 pa 100 alionse anati pamoyo wawo anagonapo ndi akazi 15 kapena kuposa pamenepo. Pamene akazi amene anagonapo ndi amuna 15 kapena kuposa anali akazi 9 pa 100 alionse.”—CENTERS FOR DISEASE CONTROL AND PREVENTION, U.S.A.

Ku Greece, “ana 62 pa ana 100 alionse a zaka 16 ananena kuti alowetsapo zinthu zolaula m’mafoni awo kuchoka pa Intaneti.”—ELEFTHEROTYPIA, GREECE.

Ku Britain, anthu 82 pa anthu 100 alionse amene anafunsidwa pa kafukufuku wina anati “chipembedzo ndicho chimagawanitsa anthu ndi kuchititsa kuti azidana.”—THE GUARDIAN, BRITAIN.

Zaka 64 Akudwala Mutu

Mayi wina wa ku China wadziwa chimene “chakhala chikumudwalitsa mutu” kwa zaka zoposa 60. Madokotala anapeza chipolopolo chotalika masentimita atatu m’mutu mwa mayiyu. Akuti iyeyu anavulazidwa ali ndi zaka 13 mu September 1943, pomwe asilikali a ku Japan analanda dera lotchedwa Xinyi, m’dziko la China. Palibe aliyense amene anaganizako zoti mwina chipolopolo n’chimene chikumudwalitsa mayiyo. Bungwe lina lofalitsa nkhani (Xinhua News Agency) linati mayiyu anapita kuchipatala ataona kuti mutuwo sukusiya, ndipo atamuyeza anapeza kuti m’mutu mwake muli chipolopolo. Panopo akuti mayiyu, yemwe ali ndi zaka 77, “ali bwino.”

Nangumi Wakalekale

Mu 2007 asodzi ena ku Alaska anapha nangumi wa mtundu winawake ndipo m’kati mwake anapezamo tizidutswa ta muvi wakale. Magazini ina (The Boston Globe) inanena kuti muviwu unali “mbali ya chida chophera anangumi chomwe anachipanga mumzinda wa New Bedford, [ku Massachusetts, m’dziko la United States], cha kumapeto kwa zaka za m’ma 1800.” Patapita nthawi, muvi wa mtunduwu anasiya kuugwiritsa ntchito. Motero, akatswiri a mbiri yakale a m’bungwe lina mumzindawu (New Bedford Whaling Museum) akuganiza kuti nangumiyu anabayidwa “m’zaka zapakati pa 1885 ndi 1895.” Iwo akuganiza kuti nthawi yomwe nangumiyu amafa, n’kuti ali ndi zaka 115. Magazini ija inanenanso kuti: “Kupezeka kwa zidutswa za muvi umenewu kukutsimikizira zimene anthu ambiri akhala akukhulupirira kuti anangumi amtunduwu ali m’gulu la anangumi omwe amakhala ndi moyo nthawi yaitali kwambiri pa dziko lonse. Anangumiwa amatha kukhala ndi moyo zaka 150.”

Akatswiri Ofukula Zinthu Zakale Apeza Nkhalango

Akatswiri ofukula zinthu zakale apeza nkhalango yoworerana ya zomera zosiyanasiyana. Zambiri mwa zomerazi zinkakula kufika mamita 40 kapena kuposa pamenepa. Komabe zomera zimenezi sizipezeka masiku ano. Nkhalango yochititsa chidwiyi imapezeka m’tinjira ta pansi pa mgodi wina wa malasha ku Illinois, m’dziko la United States. Asayansi akukhulupirira kuti nkhalangoyi inakwiririka kutachitika chivomezi champhamvu kwambiri. Mkulu wa gulu la akatswiriwo, dzina lake Bill DiMichele anati: “Izitu n’zodabwitsa kwambiri. Tsopano tili ndi chithunzithunzi cha mmene zinkakhalira kuyenda m’nkhalangoyi.”

Kukumba Vinyo Wakale Wabwino Kwambiri

Alendo ochuluka ayamba kupita ku Macedonia, dziko lomwe poyamba linkalamulidwa ndi dziko la Yugoslavia, pofuna “kukakumba vinyo wakale wabwino kwambiri yemwe anasiyidwa ndi . . . asilikali, pa nkhondo yoyamba ya padziko lonse,” inatero nyuzipepala ina (Kathimerini—English Edition). Ambiri mwa alendowa amachokera ku France ndipo amatengeratu mapu a malo amene asilikaliwo ankasungirako zinthu, kuti akakumbe kumalowa. Pakali pano, botolo lililonse la vinyo limene lingapezeke kumeneku ndiye kuti latha zaka zosachepera 90, ndipo nyuzipepala ina inati, “botolo labwinobwino lotereli lingathe kugulitsidwa . . . mayuro 2,000 (madola 2,675).” Ena mwa anthu a kumeneku omwe anakumbapo vinyo ndiponso mowa wina wotere anati “sanamweko vinyo kapena mowa wina uliwonse wokoma chonchi.”