Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Masiku Otsiriza Ndi Ati?

Kodi Masiku Otsiriza Ndi Ati?

Kodi Masiku Otsiriza Ndi Ati?

MAGAZINI ina yaposachedwapa inanena kuti: “Tikuona kuti mwina pofika zaka 1 biliyoni, dzikoli lidzapsa n’kukhala chipululu cha fumbi lokhalokha. Sitikudziwa ngati zamoyo zambiri zidzapulumuke.” (Sky & Telescope) N’chifukwa chiyani tikutero? Magazini inanso inati: “Dzuwa lidzatentha kwambiri ndipo lidzapsereza dziko lonse. Zimenezi n’zovutitsa maganizo kwambiri koma n’zosapeweka.”—Astronomy.

Komabe Baibulo limati: “[Mulungu] anakhazika dziko lapansi pa maziko ake, silidzagwedezeka ku nthawi yonse.” (Salmo 104:5) Ndithudi Mlengi wa dzikoli adzachita zonse zotheka kuti dzikoli likhalepobe. Ndipotu “analikhazikitsa . . . akhalemo anthu.” (Yesaya 45:18) Koma sanafune kuti mukhale anthu oipa komanso kuti anthu azifa. Mulungu ali ndi nthawi imene adzabwezeretse ulamuliro wake ndipo adzagwiritsa ntchito Ufumu umene watchulidwa pa Danieli 2:44.

Yesu analalikira za Ufumu wa Mulungu. Ananena za nthawi imene adzaweruze mitundu ndi anthu. Anachenjeza za chisautso chachikulu chimene sichinachitikepo. Iye anafotokoza zizindikiro zosonyeza kuti mapeto adzikoli ayandikira.—Mateyo 9:35; Maliko 13:19; Luka 21:7-11; Yohane 12:31.

Anthu ambiri amachita chidwi ndi nkhani ya masiku otsiriza chifukwa choti inatchulidwa ndi Yesu, yemwe ndi munthu wodziwika kwambiri. Kodi zizindikirozo zidzachitika liti? Anthu ena ayesa kufufuza kuti apeze nthawi imene mapeto adzafike, mwa kuphunzira zochitika za m’mbiri ya anthu ndiponso ulosi wa Baibulo. Mmodzi wa anthu amene anafufuza nkhaniyi ndi Sir Isaac Newton, yemwe anali katswiri wa masamu m’zaka za m’ma 1600 ndipo anatulukira zoti pali mphamvu ya chilengedwe imene imakokera zinthu pansi.

Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Si kwa inu kudziwa nthawi kapena nyengo zimene Atate waziika m’mphamvu ya iye yekha.” (Machitidwe 1:7) Ndipo ponena za “chizindikiro cha kukhalapo [kwake] ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu,” Yesu anati: “Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, koma Atate yekha.” (Mateyo 24:3, 36) Ndiyeno atayerekezera chiwonongeko cha anthu oipa m’masiku a Nowa ndi chiwonongeko cha m’nthawi ya “kukhalapo kwa Mwana wa munthu,” Yesu anati: “Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwera.”—Mateyo 24:39, 42.

Ngakhale kuti sitinauzidwe nthawi yeniyeni ya mapeto a “dongosolo lino la zinthu,” “chizindikiro” chimene Yesu anapereka chingatidziwitse kuti tili pati m’nthawi imene imatchedwa kuti “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Imeneyi ndi nthawi yofunika ‘kukhala maso’ kuti tidzathe “kuthawa zinthu zonsezi zoyembekezeka kuchitika.”—Luka 21:36.

Asananene chizindikiro chenicheni Yesu anachenjeza kuti: “Samalani kuti asadzakusocheretseni; pakuti ambiri adzabwera m’dzina langa, n’kumati, ‘Khristu uja ndine,’ adzanenanso kuti, ‘Nthawi ija yayandikira.’ Musadzawatsatire. Komanso, mukadzamva nkhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha. Pakuti zimenezi ziyenera kuchitika choyamba, koma mapeto sadzafika nthawi yomweyo.”—Luka 21:8, 9.

Kodi Chizindikiro Chake N’chiyani?

Ponena zimene zidzasonyeze kuti tili m’masiku otsiriza, Yesu ananenanso kuti: “Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndipo ufumu ndi ufumu wina; kudzachitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala miliri ndi njala m’malo osiyanasiyana. Kudzaoneka zoopsa ndipo kumwamba kudzaoneka zizindikiro zodabwitsa.” (Luka 21:10, 11) Yesu anatinso: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.” (Mateyo 24:14) Zinthu zimene Yesu anatchula monga nkhondo, zivomezi, miliri, njala, si zachilendo ayi. Zakhala zikuchitika kuyambira kale. Kusiyana kwake n’kwakuti iye anati zonsezi zidzachitika panyengo imodzi.

Ndiyeno dzifunseni kuti: ‘Ndi nyengo iti imene zizindikiro zonse zotchulidwa m’Mauthenga Abwino zachitikira pamodzi? Kuyambira mu 1914 pakhala nkhondo za padziko lonse zosakaza kwabasi; zivomezi zoopsa kwadzaoneni, nyanja zosefukira, njala yopha anthu ambirimbiri ndiponso miliri ya malungo, chimfine ndi EDZI. Komanso anthu ambiri akhala akuopa uchigawenga ndi zida zoopsa. Panthawi yomweyi, Mboni za Yehova zakhala zikulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse. Zinthu zimenezi zakhala zikuchitika monga Yesu ananenera.

Komanso kumbukirani mawu a mtumwi Paulo akuti: “Dziwa kuti, m’masiku otsiriza, idzafika nthawi yovuta yoikika. Pakuti anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza, onyoza, osamvera makolo, osayamika, osakhulupirika, opanda chikondi chachibadwa, osagwirizanitsika, odyerekeza, osadziletsa, owopsa, osakonda zabwino, achiwembu, aliuma, otukumuka chifukwa cha kunyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu, ooneka ngati odzipereka kwa Mulungu koma mphamvu ya kulambira Mulungu siitha kuwasintha.” (2 Timoteyo 3:1-5) Inde, ulosiwu unasonyeza kuti padziko lonse padzakhala “nthawi yovuta yoikika,” yodziwika ndi zinthu monga kufala kwa khalidwe la kusamvera malamulo, kusakonda Mulungu, nkhanza, ndiponso kuchita zinthu mosaganizira ena. *

Kodi “masiku otsiriza” amene adzatifikitse pa mapeto a zonse adakali m’tsogolo? Kodi pali umboni wina wosonyeza nthawi imene masiku amenewa adzayambire?

Kodi Ulosi Unati “Nthawi Yotsiriza” Idzayamba Liti?

Ataona masomphenya a zomwe zidzachitike m’tsogolo, mneneri Danieli anauzidwa kuti: “Ndipo nthawi yomweyi [“nthawi yotsiriza” yotchulidwa pa Danieli 11:40] adzauka Mikaeli [Yesu Khristu] kalonga wamkulu wakutumikira ana a anthu a mtundu wako.” (Danieli 12:1) Kodi ulosi unati Mikaeli adzachita chiyani?

Buku la Chivumbulutso limatchulapo za nthawi imene Mikaeli adzayambe kulamulira. Limati: “Kunabuka nkhondo kumwamba: Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Nacho chinjoka ndi angelo ake chinamenya nkhondo, koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. Choncho, chinjokacho chinaponyedwa pansi, inde njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Inde, anaponyedwa kudziko lapansi, ndi angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. Pa chifukwa chimenechi, kondwerani miyamba inu ndi inu okhala mmenemo! Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ali ndi mkwiyo waukulu, podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”—Chivumbulutso 12:7-9, 12.

Tikawerengetsera zaka zotchulidwa m’Baibulo timaona kuti nkhondo imeneyi, yochotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba, idzabweretsa masoka adzaoneni padziko lapansi. Mdyerekeziyo adzakwiya podziwa kuti nthawi yake yolamulira dziko yam’tsalira yochepa. Mkwiyo wakewo udzapitirira kukula m’nthawi ya masiku otsiriza mpaka panthawi imene adzagonjetsedweretu pa nkhondo ya Armagedo.—Chivumbulutso 16:14, 16; 19:11, 15; 20:1-3.

Atatchula zimene zidzachitike pa nkhondo ya kumwambayo, mtumwi Yohane anati: “Ndinamva mawu ofuula kumwamba, amvekere: ‘Tsopano chakwaniritsidwa chipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Khristu wake, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iyeyo anali kuwaneneza usana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu!’” (Chivumbulutso 12:10) Kodi mwaona kuti lembali likulengeza za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Khristu? Inde, Ufumu umenewu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914. * Komabe, lemba la Salmo 110:2 limasonyeza kuti Yesu adzayamba kulamulira ‘pakati pa adani ake’ mpaka nthawi imene Ufumu wake udzayambe kulamulira dziko lapansi monga zilili kumwamba.—Mateyo 6:10.

N’zochititsa chidwi kuti mngelo amene anauza mneneri Danieli za zinthu zimenezi, ananenanso kuti: “Koma iwe Danieli, tsekera mawu awa, nukhomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimariziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.” (Danieli 12:4) Uwu ndi umboni wakuti tsopano tikukhala mu “nthawi ya chimariziro.” Matanthauzo a maulosi amenewa adziwika kale ndipo akulengezedwa pa dziko lonse. *

Kodi “Masiku Otsiriza” Adzatha Liti?

Baibulo silitchula kuti masiku otsiriza adzatha liti. Koma limanena kuti m’masikuwa zinthu zidzapitirira kuipa chifukwa nthawi ya Satana idzakhalanso ikucheperachepera. Mtumwi Paulo anachenjeza kuti “anthu oipa ndi onyenga adzaipiraipirabe.” (2 Timoteyo 3:13) Ndipo ponena zam’tsogolo, Yesu anati: “Masiku amenewo adzakhala masiku a chisautso chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu analenga kudzafika nthawi imeneyo, ndipo sichidzachitikanso. Kunena zoona, Yehova akanapanda kufupikitsa masikuwo, palibe aliyense akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhikawo, amene iye anawasankha, wafupikitsa masikuwo.”—Maliko 13:19, 20.

Zina mwa zinthu zimene sizinachitike ndi “chisautso chachikulu,” nkhondo ya Armagedo, ndiponso kuletsa Satana ndi ziwanda zake kuchita chilichonse kwa anthu padziko lapansi. (Mateyo 24:21) “Mulungu, amene sanganame,” watitsimikizira kuti zinthu zimenezi zidzachitika ndithu. (Tito 1:2) Mulungu ndi amene adzachititse nkhondo ya Armagedo ndiponso kuti Satana aponyedwe m’phompho.

Mtumwi Paulo anauziridwa kutilembera zimene zidzachitike Mulungu asanawononge dzikoli. Ponena za “nthawi ndi nyengo,” yake iye analemba kuti: “Tsiku la Yehova lidzabwera ndendende ngati mbala usiku. Pamene azidzati: “Bata ndi mtendere!” chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zopweteka za mkazi wapathupi, ndipo sadzapulumuka konse.” (1 Atesalonika 5:1-3) Baibulo silitchula chimene chidzachititse kuti azidzati “bata ndi mtendere” moti tidzangozionera tokha panthawiyo. Komabe, zimenezi sizidzalepheretsa kubwera kwa tsiku la chiweruzo cha Yehova. *

Ngati sitikayikira kuti maulosi amenewa adzakwaniritsidwa, tiyeni tichitepo kanthu pa mfundo zimene tadziwazi. Kodi tingachite chiyani? Petulo akuyankha kuti: “Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, lingalirani za mtundu wa munthu amene muyenera kukhala pa khalidwe loyera ndi pa ntchito za kudzipereka kwanu kwa Mulungu. Teroni poyembekezera ndi kukumbukira nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” (2 Petulo 3:11, 12) Komabe mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi zimenezi zingandithandize bwanji ineyo?’ Nkhani yotsatirayi iyankha funso limeneli.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 12 Kuti muone umboni wina wokhudza “masiku otsiriza,” werengani Galamukani! ya April 2007, masamba 8 mpaka 10, ndiponso Nsanja ya Olonda ya September 15, 2006 masamba 4 mpaka 7, ndi ya October 1, 2005, masamba 4 mpaka 7. Magazini onsewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 18 Kuti mumve tsatanetsatane wa nkhani ya kuwerengera zaka za m’Baibulo, onani masamba 215 mpaka 218 m’buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 19 Onani buku lakuti Samalani Ulosi wa Danieli! ndi buku la 2008 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 31 mpaka 39. Mabuku onsewa ndi ofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 23 Onani buku la Revelation—Its Grand Climax At Hand! (losindikizidwa mu 2006), masamba 250 ndi 251, ndime 13 ndi 14.

[Mawu Otsindika patsamba 5]

Yesu ananena kuti Mulungu yekha ndi amene akudziwa “tsikulo ndi ola lake”

[Chithunzi patsamba 4]

Sir Isaac Newton

[Mawu a Chithunzi]

© A. H. C./age fotostock

[Zithunzi patsamba 7]

Kuyambira 1914 takhala tikuona chizindikiro chimene Yesu ananena

[Mawu a Chithunzi]

© Heidi Bradner/Panos Pictures

© Paul Smith/Panos Pictures