Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Muzichita Chiyani?

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Muzichita Chiyani?

Zimene Baibulo Limanena

Kodi Mulungu Amafuna Kuti Muzichita Chiyani?

MOYO wa masiku anowu uli ndi zambiri zotangwanitsa kwambiri. Motero nthawi zina zimativuta kukwaniritsa maudindo athu onse. Komatu tiyenera kukumbukira kuti moyowu ndi mphatso yomwe Mulungu anatipatsa. (Salmo 36:9) Kodi Mulungu amafuna kuti tizigwiritsa ntchito nthawi ndiponso mphamvu zambiri motani pomutumikira? Mulimbikitsidwa kudziwa yankho lochokera m’Baibulo la funso limeneli.

Yesu ankadziwa bwino kuposa munthu wina aliyense zimene Atate wake amafuna kuti anthufe tizichita. (Mateyo 11:27) Atafunsidwa kuti atchule lamulo lalikulu kwambiri, Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse, ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? Kodi tingati Mulungu amafuna kuti tizichita zinthu zovuta kwambiri?

Tanthauzo la Kukonda Mulungu ndi Moyo Wathu Wonse

Tingayambe kukonda kwambiri Mulungu poganizira zinthu zabwino zosasimbika zimene amatichitira. Ngati timakonda Mulungu ndi moyo wathu wonse, mtima wathu umatilimbikitsa kuchita zonse zomwe tingathe pomutumikira. Timamva mmene anamvera wolemba Baibulo wina, amene anafunsa kuti: “Ndidzabwezera Yehova chiyani chifukwa cha zokoma zake zonse anandichitira?” (Salmo 116:12) Kodi kukonda Mulungu kotereku kumakhudza bwanji mmene timagwiritsira ntchito nthawi?

Baibulo silitchula kuchuluka kwa nthawi imene tiyenera kugwiritsa ntchito mlungu uliwonse polambira. Komabe, limafotokoza zinthu zimene tiyenera kuziona kuti n’zofunika kwambiri pamoyo wathu ndipo limafotokoza chifuwa chake tiyenera kuziona choncho. Mwachitsanzo, Yesu anaphunzitsa anthu kuti m’pofunika kudziwa Mulungu kuti tidzakhale ndi “moyo wosatha.” (Yohane 17:3) Iye ananenanso kuti otsatira ake ayenera kuthandiza ena kudziwa Mulungu kuti adzapeze moyo. (Mateyo 28:19, 20) Baibulo limatilangiza kuti tizisonkhana nthawi zonse ndi Akhristu anzathu kuti tikhale olimba mwauzimu ndiponso kuti tizilimbikitsana. (Aheberi 10:24, 25) Zonsezi zimafuna nthawi.

Kodi Mulungu amafuna kuti nthawi zonse tizingokhalira kumulambira basi, osachitanso zinthu zina? Ayi, safuna zimenezo. Timafunikanso kuchita zinthu zina zotithandiza pamoyo wathu tsiku ndi tsiku. Mwachitsanzo, Baibulo limalamula mitu ya banja kupezera mabanja awo zinthu zofunika pa moyo wawo. Limati: “Ndithudi, ngati munthu sasamalira ake a iye mwini, makamaka a m’banja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wopanda chikhulupiriro.”—1 Timoteyo 5:8.

Mulungu analenga munthu kuti azisangalala ndi moyo. Motero sikulakwa kumasangalala ndi mabanja athu komanso anzathu pocheza nawo ndi kudyera limodzi chakudya. Mfumu Solomo analemba kuti: “Ndidziwa kuti iwo alibe ubwino, koma kukondwa ndi kuchita zabwino pokhala ndi moyo. Ndiponso kuti munthu yense adye namwe nawone zabwino m’ntchito zake zonse; ndiwo mtulo wa Mulungu.”—Mlaliki 3:12, 13.

Komanso Yehova Mulungu amazindikira zinthu zimene anthufe sitingakwanitse kuchita, chifukwa “akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Baibulo limasonyeza kuti munthu amafunika kupuma mokwanira. Panthawi inayake atagwira ntchito mwakhama, Yesu anauza ophunzira ake kuti apite ‘kwaokha kopanda anthu kuti apumule pang’ono.’—Maliko 6:31.

Motero moyo umene umasangalatsa Mulungu ndi moyo wochita zinthu zosiyanasiyana. Komabe zochita zathu zonse, kaya zikhale zokhudzana ndi kulambira kapena ayi, ziyenera kusonyeza kuti timakonda Mulungu ndi moyo wathu wonse. Baibulo limalangiza kuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu.”—1 Akorinto 10:31.

Kuzindikira Zinthu Zofunikira Kwambiri

Kodi mumaona kuti n’zovuta kwambiri kapena kuti n’zosatheka kuti kulambira Mulungu kukhale chinthu chofunikira kwambiri pa moyo wanu? N’zoona, kuti tikwanitse kuchita zimene Mulungu amafuna, tingafunike kusintha kwambiri mmene timagwiritsira ntchito nthawi yathu, zomwe nthawi ina zingakhale zovuta kwambiri. Komatu Mlengi wathu ndi wachikondi ndipo satiuza kuchita zimene sitingathe. Ndipotu amatithandiza kwambiri kuti tithe kuchita zimene amafuna. Tingathe kuchita zimenezi tikamadalira “mphamvu imene Mulungu amapereka.”—1 Petulo 4:11.

N’kutheka kuti mungavutike kusintha zochita zanu kuti muyambe kuchita zinthu zauzimu. Yesetsani kupeza nthawi yolankhula pafupipafupi ndi Yehova, yemwe ndi Mulungu, “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Popempherapo, mungathe kumuuza mavuto anu onse, podziwa kuti “amasamala za inu.” (1 Petulo 5:7) Mfumu Davide anapemphera kuti: “Mundiphunzitse chokonda Inu, popeza Inu ndinu Mulungu wanga.” (Salmo 143:10) Inunso mungam’pemphe Mulungu kukuthandizani kusintha moyo wanu.

M’Baibulo muli mawu olimbikitsa akuti: “Yandikirani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikirani.” (Yakobe 4:8) Mukayamba kuchita zinthu zosangalatsa Mulungu, monga kuphunzira Baibulo ndi kupita kumisonkhano yachikhristu, mudzayamba kuyandikira kwa Mulungu. Mukatero, iye adzakulimbikitsani kuti mupitirize kupita patsogolo.

Jelena, amene akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ananena izi pofotokoza khama lake pofuna kusintha zochita zake: “Kunena zoona, sizinali zophweka ngakhale pang’ono. Koma nditayamba kupita kumisonkhano yachikhristu, ndinayamba kulimbikitsidwa kutsatira zimene Baibulo limanena. Chimene chandithandizanso n’chakuti Akhristu anzanga sanafooke pondilimbikitsa.” Mumalimbikitsidwanso kwambiri mukayamba kupeza madalitso chifukwa chotumikira Mulungu. (Aefeso 6:10) Jelena anati: “Panopo, ndinayamba kugwirizana kwambiri ndi mwamuna wanga ndiponso ndimalangiza bwino ana anga.”

Mzimu woyera wa Yehova ndi wamphamvu kwambiri ndipo ungakupatseni mphamvu n’kukulimbikitsani kuti muyambe kuona kuti kuchita zimene Mulungu amafuna ndiko chinthu chofunika kwambiri pamoyo. Zimenezi zingakuthandizeni ‘kudziwombolera nthawi’ ngakhale kuti moyo wa masiku ano uli ndi zovuta zambiri. (Aefeso 3:16; 5:15-17) Yesu anati: “Zinthu zosatheka kwa anthu n’zotheka ndi Mulungu.”—Luka 18:27.

KODI MWAGANIZIRAPO IZI?

▪ N’chifukwa chiyani muyenera kuona kuti kuchita zimene Mulungu amafuna ndiko chinthu chofunikira kwambiri pa moyo?—Salmo 116:12; Maliko 12:30.

▪ Kodi Mulungu amafuna kuti muzichita nawo zinthu ziti?—Mateyo 28:19, 20; Yohane 17:3; Aheberi 10:24, 25.

▪ Kodi mungasinthe zinthu zotani kuti musangalatse Mulungu?—Aefeso 5:15-17; Yakobe 4:8.

[Chithunzi patsamba 20]

Mulungu amasangalala tikamachitanso zinthu zina