Kodi Mungayankhe Bwanji?
Kodi Mungayankhe Bwanji?
Fotokozani chithunzichi
1. Pankhani imene yalembedwa pa Mateyo 25:31-46, kodi “Mwana wa munthu” ndani?
ZOKUTHANDIZANI: Werengani Mateyo 16:13-17.
․․․․․
2. N’chiyani chidzachititsa munthu kuweruzidwa kuti ndi nkhosa kapena mbuzi?
․․․․․
3. N’chiyani chidzachitikire nkhosa, nanga n’chiyani chidzachitikire mbuzi?
․․․․․
KAMBIRANANI:
Kodi ndani kwenikweni akunenedwa kuti “abale anga”? Nanga mungatani kuti muwathandize?
Kuchokera M’magazini Ino
Yankhani mafunso awa ndipo tchulani mavesi a m’Baibulo amene akusowa.
TSAMBA 3 Kodi anthu onyodola adzanena kuti chiyani m’masiku otsiriza? 2 Petulo 3:․․․
TSAMBA 7 Kodi chiwonongeko chodzidzimutsa chidzafika panthawi iti? 1 Atesalonika 5:․․․
TSAMBA 20 N’chifukwa chiyani mutu wa banja uyenera kusamalira banja lake mwakuthupi? 1 Timoteyo 5:․․․
TSAMBA 28 Kodi tiyenera kuchita zinthu zonse motani? Aheberi 13:․․․
Zithunzi Zoti Ana Apeze
Kodi mungapeze zithunzi izi m’magazini ino? Fotokozani zimene zikuchitika pa chithunzi chilichonse.
Kodi Ndani Ali M’gulu la Makolo a Yesu?
Zokuthandizani. Werengani malemba amene angakuthandizeni kupeza yankho. Kenako lembani mayina olondola pa mizereyo.
4. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndine agogo a Abulahamu.
Werengani Genesis 11:24-26.
5. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Ndinasamuka ndi banja langa mumzinda wa Uri n’kupita kudziko la Kanani.
Werengani Genesis 11:31.
6. ․․․․․
ZOKUTHANDIZANI: Yehova anasintha dzina langa chifukwa anati ndidzakhala “atate wa khamu la mitundu.”
Werengani Genesis 17:5.
▪ Mayankho ali patsamba 19
MAYANKHO A MAFUNSO A PATSAMBA 31
1. Yesu.
2. Zimene munthuyo amachitira abale auzimu a Yesu.
3. Nkhosa zidzalandira moyo wosatha koma mbuzi zidzawonongedwa kotheratu.
4. Nahori.—Luka 3:34.
5. Tera.—Luka 3:34.
6. Abulahamu.—Luka 3:34.