Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Ndi Masiku Otsiriza a Chiyani?

Kodi Ndi Masiku Otsiriza a Chiyani?

Kodi Ndi Masiku Otsiriza a Chiyani?

TAYEREKEZERANI kuti pawindo la sitolo ina pali chikwangwani chakuti “Masiku Otsiriza.” Mwina mungaganize kuti nthawi yogulitsa zinthu motchipa yatsala pang’ono kutha kapena sitoloyo aitseka posachedwa. Koma bwanji wina atanena kuti: “Tikukhala m’masiku otsiriza”? Kodi mungati akutanthauza chiyani?

Anthu akhala akugwiritsa ntchito mawu akuti “masiku otsiriza” ndi “nthawi ya chimariziro” kwanthawi yaitali. (2 Timoteyo 3:1; Danieli 12:4) Zaka zoposa 2,500 zapitazo, mneneri Danieli anaona masomphenya a maulamuliro apadziko lapansi ndiponso nkhondo zimene zidzachitike pakati pa maulamulirowo mpaka “nthawi ya chimariziro.” Iye anauzidwa kuti tanthauzo la masomphenya amenewa lidzadziwika bwinobwino panthawi ya chimaliziroyo. (Danieli 8:17, 19; 11:35, 40; 12:9) Danieli analembanso kuti: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse. Nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.

Yesu Khristu anatchula za “mapeto” poyankha funso lokhudza “chizindikiro cha kukhalapo [kwake] ndi cha mapeto a dongosolo lino la zinthu.” (Mateyo 24:3-42) Zikuoneka kuti Danieli komanso Yesu anali kunena za mapeto enaake, kapena kuti kusintha kwa zinthu kumene kudzakhudze anthu onse amene adzakhale ndi moyo ndiponso amene anakhalapo ndi moyo padzikoli. Danieli analemba za kutha kwa maboma onse apadziko lapansi. Yesu ananena za “mapeto a dongosolo lino la zinthu.”

Kodi pali chifukwa choti muziganizira nkhani imeneyi? Inde, chifukwatu munthu aliyense ikumukhudza. Komabe anthu ambiri alibe nayo chidwi nkhani imeneyi. Baibulo linalosera kuti: “M’masiku otsiriza kudzakhala onyodola ndi kunyodola kwawo, otsatira zilakolako zawo, amene azidzati: ‘Kuli kuti kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja? Taonani, kuchokera tsiku limene makolo athu anamwalira, zinthu zonse zikupitirirabe chimodzimodzi monga kuyambira pachiyambi cha chilengedwe.’” (2 Petulo 3:3, 4) N’zoona kuti anthu ambiri masiku ano amaona kuti zinthu zikungochitika mmene zakhala zikuchitikira kuyambira kale ndipo amati moyo ukhala chonchi mpaka kalekale.

Kodi pali umboni uliwonse wakuti tilidi m’masiku amene Baibulo limati otsiriza? Tiyeni tione.