Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Masiku Otsiriza Akadzatha Zinthu Zidzakhala Bwanji?

Masiku Otsiriza Akadzatha Zinthu Zidzakhala Bwanji?

Masiku Otsiriza Akadzatha Zinthu Zidzakhala Bwanji?

ANTHU ena amachita mantha akaganizira za “masiku otsiriza.” (2 Timoteyo 3:1) Iwo amangoona kuti ndi nthawi ya mavuto okhaokha. Nanga n’chifukwa chiyani anthu ambiri akhala akuyembekezera masiku amenewa kuyambira kalekale? N’chifukwa chakuti masiku otsiriza amasonyeza kuti zinthu zabwino zayandikira.

Mwachitsanzo, Sir Isaac Newton ankakhulupirira kuti masiku otsiriza akadzatha dziko lonse lidzakhala pamtendere ndipo lidzatukuka mu Ulamuliro wa zaka 1,000 wa Ufumu wa Mulungu. Iye ananena kuti pa nthawi imeneyi, ulosi wa pa Mika 4:3 komanso wa pa Yesaya 2:4 udzakwaniritsidwa. Ulosiwo umati: “Iwo adzasula malupanga awo akhale zolimira, ndi nthungo zawo zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.”

Pamene Yesu ananena za nthawi ya chimaliziro, analimbikitsa otsatira ake kuti asaope. Atatha kunena za mavuto, nkhawa ndi mantha zimene zidzakhalapo pa chisautso chachikulu, Yesu ananena kuti: “Zinthu izi zikadzayamba kuchitika, mudzaimilire chilili ndi kutukula mitu yanu, chifukwa chipulumutso chanu chikuyandikira.” (Luka 21:28) Kodi anthu adzapulumutsidwa ku chiyani?

Zimene Mulungu Walonjeza

Nkhondo, upandu, ziwawa ndiponso njala ndi zina mwa zinthu zimene zikuvutitsa anthu masiku ano ndipo zikuchititsa anthu ambiri kukhala amantha. Kodi munakumanapo ndi ena mwa mavuto amenewa? Ngati ndi choncho, taonani zimene Mulungu walonjeza.

“Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti . . . Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:10, 11.

“Anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.”—Yesaya 32:18.

“[Yehova] aletsa nkhondo ku malekezero adziko lapansi; athyola uta, nadula nthungo; atentha magareta ndi moto.”—Salmo 46:9.

“Adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwawopsa.”—Mika 4:4.

“M’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri; zipatso zake zidzati waa.”—Salmo 72:16.

“Koma wondimvera ine adzakhala osatekeseka, nadzakhala phe osaopa zoipa.”—Miyambo 1:33.

Ngakhale titakhala kuti tili pabwino ndithu, tonse timadwala ndiponso timamwalira. Mavuto amenewanso sadzakhalamo m’dziko latsopano la Mulungu. Motero tingayembekezere mwachidwi kudzaonana ndi abale athu amene anamwalira. Taonani mfundo zotsatirazi:

“Wokhalamo sadzanena, ine ndidwala.”—Yesaya 33:24.

“[Mulungu] adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

“Imfa nayonso, monga mdani womalizira, idzawonongedwa.”—1 Akorinto 15:26.

“Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda a chikumbutso adzamva mawu [a Yesu] ndipo adzatuluka.”—Yohane 5:28, 29.

Mtumwi Petulo anafotokoza mwachidule mfundo zimenezi polemba kuti: “Pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuyembekeza malinga ndi lonjezo lake, ndipo mmenemo mudzakhala chilungamo.” (2 Petulo 3:13) Kuti padziko lonse padzakhale chilungamo anthu osokoneza mtendere afunika kuchotsedwa kaye. Padzafunikanso kuchotsa maulamuliro amasiku anowa amene amayambitsa nkhondo ndi kupha anthu osalakwa chifukwa cha dyera lawo. Maulamuliro onse padzikoli adzalowedwa m’malo ndi Ufumu wa Mulungu umene mfumu yake ndi Khristu. Ponena za ufumu umenewu, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Za kuyenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthawi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”—Yesaya 9:7.

Inunso mukhoza kukhala ndi chiyembekezo chimenechi chifukwa Baibulo limatitsimikizira kuti: “Chifuniro [cha Mulungu] n’chakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziwa choonadi molondola.” (1 Timoteyo 2:4) Musachedwe, phunzirani zinthu zimene zingakuthandizeni kudzapeza moyo wosatha. (Yohane 17:3) Monga poyambira, tipezeni kapena tilembereni kalata ngati mukufuna kuti wina aziphunzira nanu Baibulo kwaulere panyumba panu.

[Chithunzi pamasamba 8, 9]

Mungayembekezere kudzakhala kosatha mwamtendere ndiponso popanda matenda m’Paradaiso padziko lapansi