Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mmene Achinyamata Angathetsere Kuvutika Maganizo

Mmene Achinyamata Angathetsere Kuvutika Maganizo

Mmene Achinyamata Angathetsere Kuvutika Maganizo

OPHUNZIRA Chingelezi ku Mexico anauzidwa kuti akonzekere kukamba nkhani ya mutu uliwonse umene angasankhe. Mtsikana wina dzina lake Maritza ananena kuti: “Ineyo ndinagwiritsa ntchito mfundo za m’magazini ya Galamukani! ya September 8, 2001 yakuti, ‘Kuthandiza achinyamata amene akuvutika maganizo.’ Ndinatero chifukwa chakuti nthawi ina nditavutika maganizo kwa nthawi yaitali nkhani za m’magazini imeneyi zinandithandiza kwambiri. Aphunzitsi anati nkhani imene ndinakambayo ndi imene inali yabwino kwambiri pa zonse. Kenako ndinapatsa wophunzira aliyense fotokope ya nkhanizo.”

Patapita zaka ziwiri, Maritza ali muutumiki anakumana ndi wophunzira wina yemwe ankaphunziranso Chingelezi. Maritza anadabwa kwambiri wophunzirayo atamusonyeza fotokope ya nkhani zokhudza kuvutika maganizo za mu Galamukani! ija. Zikuoneka kuti mphunzitsi uja anasangalala nayo kwambiri moti anapereka fotokope ya nkhanizo kwa wophunzira aliyense.

Kuti mumve zambiri pankhani ya mmene achinyamata angathetsere kuvutika maganizo, werengani buku la Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. M’bukuli muli mitu monga yakuti: “Kodi Nchifukwa Ninji Sindimadzikonda?,” “Kodi Nchifukwa Chiyani Ndimachita Tondovi Kwambiri?” ndi “Kodi Ndingachititse Motani Kusukidwa Kwanga Kuchoka?” Ngati mukufuna kuitanitsa bukuli, lembani zofunika m’mizere ili panoyi ndipo tumizani ku adiresi imene ili pomwepoyo kapena ku adiresi yoyenerera imene ili pa tsamba 5 la magazini ino.

□ Ndikupempha kuti munditumizire buku lasonyezedwa panoli.

□ Nditumizireni munthu kuti ayambe kuphunzira nane Baibulo kwaulere.