Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Oona za Ndege Amakutetezani Bwanji?

Oona za Ndege Amakutetezani Bwanji?

Oona za Ndege Amakutetezani Bwanji?

YOLEMBEDWA KU PHILIPPINES

KODI munayamba mwadzifunsapo kuti oyendetsa ndege amadziwa bwanji kumene akupita? N’kutheka kuti mumaona kuti m’posavuta kuti ndege ziwombane chifukwa nthawi iliyonse ndege zambirimbiri zimakhala zikuuluka. Kodi n’chiyani chimathandiza kuti ndegezi zisawombane?

Anthu ambiri amadzifunsa mafunso amenewa. Komabe ofufuza anapeza kuti ulendo wa pandege si woopsa ngakhale pang’ono * poyerekezera ndi wa pa njinga yamoto kapena wa pagalimoto. Anthu oona za kayendedwe ka ndege ndiwo makamaka amathandiza kuti ulendo wa pandege ukhale wosaopsa.

Kuyendetsa Ndege Kuti Ikafike Bwinobwino

Woyendetsa ndege ndi amene amaonetsetsa kuti ndegeyo ikuyenda bwino. Komabe nthawi zambiri iyeyo satha kuona ndege zimene zikuuluka chapafupi ndi ndege yake. Chifukwa cha zimenezi, mabwalo a ndege a m’mayiko ambiri amakhala ndi anthu oona za kayendedwe ka ndege. Anthuwa amaonetsetsa ndege iliyonse kungoyambira pamene ikunyamuka mpaka pamene ikutera.

Samuel, wakhala akugwira ntchito imeneyi ku California kwa zaka 13. Iye anati: “Akatswiri oona za kayendedwe ka ndege amathandiza kwambiri kuti ndege ziziyenda bwino. Ntchito yawo yaikulu ndiyo kuonetsetsa kuti ndege zisamayandikane kwambiri.” Melba, yemwe amayang’anira ntchito imeneyi, anafotokozanso kuti: “Chinthu chofunika kwambiri kwa ife ndicho kuonetsetsa kuti ndege zisachite ngozi. Timaonetsetsanso kuti ndege zikuyenda mwachangu komanso mwadongosolo.” Motero, sikuti anthu oona za kayendedwe ka ndege amangothandiza kupewa ngozi zokha, koma amathandizanso kuti ndegezo ziziyenda mwachangu.

Zimenezi zikutanthauza kuti munthu akamayendetsa ndege, pamakhala anthu ena pansi amene amathandizana naye paulendowo. Woyendetsa ndegeyo kawirikawiri amagwiritsa ntchito wailesi polankhulana ndi anthu a kumene wachokera, a kumene akupita, komanso a m’mabwalo osiyanasiyana a ndege amene akudutsa.

Ndege zamasiku ano zimathamanga kwambiri, choncho m’pofunika anthu oti aziona zimene woyendetsa ndegeyo sangaone. Taganizirani kuti ndege ziwiri zikuluzikulu zikuuluka moyang’anizana. Woyendetsa ndegeyo sangaone ndege inayo mpaka kutangotsala masekondi ochepa chabe kuti ndegezo zigundane. Motero ndi udindo wa anthu oona za kayendedwe ka ndege kupewa kuti zoterezi zisachitike. Iwowa amawauza oyendetsa ndegewo kuti atalikirane asanafike n’komwe poyandikirana kwambiri.

Kudziwa Pamene Pali Ndege Yanu

M’madera osiyanasiyana anaikamo zipangizo zimene zimathandiza woyendetsa ndege kudziwa pamene pali ndegeyo. Ndege zimadutsa m’malo amenewa mpaka kukafika kumene zikupita. Tingati zipangizo zimenezi zachititsa kuti pakhale njira zodziwika zomwe ndege zimayendamo.

Ndiyeno anthu oona za kayendedwe ka ndege amaona ndege zonse zimene zili m’njira zimenezi. Ndege isananyamuke, oyendetsa ndegeyo amayenera kulemba njira imene akufuna kudutsa paulendo wawo. Munthu woona za kayendedwe ka ndegeyo amakhalanso ndi pepala losonyeza zinthu zosiyanasiyana zokhudza ndegeyo ndiponso ulendo wake. Salvador Rafael anali mkulu wa anthu oona za kayendedwe ka ndege ndipo anafotokoza kufunika kwa ntchito imeneyi. Iye anati: “Njira zam’mwambazi zili ndi nkhumano zosiyanasiyana, motero ndege ikafika pa nkhumano iliyonse, woyendetsa amayenera kudziwitsa munthu amene akuona za kayendedwe ka ndegeyo. Zikatero munthuyo amachonga zimenezi pa pepala losonyeza ulendo wa ndegeyo.” Choncho munthuyo amadziwa pamene ndegeyo yafika.

Kuti adziwe zinthu zonsezi amagwiritsa ntchito wailesi. Ndiyeno akadziwa pamene pali ndegeyo, amapereka malangizo kwa woyendetsayo, omuthandiza kuti asayandikane kwambiri ndi ndege zina. Nthawi zambiri anthu oona za kayendedwe ka ndege ndiponso oyendetsa ndege amamvana pogwiritsa ntchito mawailesi osiyanasiyana omwe amathanso kuwachuna m’njira zosiyanasiyana. Njira imodzi ikavuta amagwiritsa ntchito njira ina.

Nanga kodi anthuwa amamvana bwanji pankhani ya chinenero akamalankhulana ndi ndege zochokera kunja? Pofuna kupewa ngozi zochitika chifukwa chosamvana chinenero, bungwe loona za maulendo a ndege padziko lonse (International Civil Aviation Organization) linasankha kuti anthu onsewa azilankhula Chingelezi. Mukamalankhula pa wailesi mawu ndi manambala ena amamveka mofanana. Motero anthu oona za kayendedwe ka ndege amaphunzitsidwa ziganizo zosiyanasiyana zomwe amayenera kugwiritsa ntchito nthawi zonse. Amaphunzitsidwanso katchulidwe koyenerera ka mawu popereka malangizo kwa oyendetsa ndege. Pofuna kupeweratu ngozi, woyendetsa ndegeyo amauzidwa kuti azibwereza mawu amene munthu woona za kayendedwe ka ndegeyo akumuuza.

Anthu oona za kayendedwe ka ndege amathanso kuiona ndegeyo pakompyuta. Ndegeyo imangooneka ngati kadontho koma ndege iliyonse ili ndi chipangizo chothandiza kuti izidziwika pa kompyutapo. Zimenezi zimathandiza kuti athe kuona ndege imene kadonthoko kakuimira n’kudziwanso nambala yake, liwiro lake, pamene ili, komanso mtundu wake.

Munthu woona za kayendedwe ka ndege angathe kuuza woyendetsa ndege kuchita zinthu zingapo pofuna kuwongolera ndegeyo kuti isagundane ndi ndege ina. (1) Kukhota. (2) Kuchepetsa liwiro pamene mwina ndege ina ikufuna kupitirira inzake. (3) Kukwera kapena kutsika pang’ono. Iyi ndi njira yofala kwambiri yothandizira kuti ndege zisayandikane kwambiri.

Chinanso chimene chimathandiza kwambiri ndi chakuti makompyuta ambiri oterewa amatha kuchenjeza munthu woona za kayendedwe ka ndege ngati pangathe kuchitika ngozi. Mwachitsanzo, makompyutawa amatha kuliza alamu akaona kuti ndege ziwiri ziyandikana kwambiri zikafika penapake. Amatha kuliza alamu inanso ngati ndege ina ikuuluka pafupi kwambiri ndi nthaka.

Cholinga Chawo ndi Kukutetezani

Panopa ayamba kale kugwiritsira ntchito njira zatsopano zothandiza pantchito yoona za kayendedwe ka ndege. Njira zimene zakhala zikugwiritsidwa ntchito panopa, nthawi zambiri zimachititsa kuti ndege ziziyenda m’njira zinazake zokha komanso pamtunda winawake. Zimenezi zimachititsa kuti ndege zizingopanikizana malo amodzi m’mwambamo ngakhale kuti malo alimo ambirimbiri. Zimachititsanso kuti ndege ziziyenda ulendo wautali. Njira zatsopanozi zipangitsa kuti ndege ziyambe kudalira kwambiri makina okhala mumlengalenga amene athandize kuti ndegezo zikhale ndi njira zambiri zodutsamo. Zithandizanso kuti maulendo odutsa panyanja zikuluzikulu akhale osavuta.

Mfundo zochepa zimene taona zokhudza anthu oona za kayendedwe ka ndege zasonyeza kuti si woyendetsa ndege yekha amene amadziwa pamene ndegeyo ili. Kwenikweni m’mabwalo a ndege mumakhala anthu ena ambirimbiri amene amayang’anira mmene ndegeyo ikuyendera. Zinthu zimenezi zimathandiza kuchepetsa ngozi. N’chifukwa chake zili zosadabwitsa kuti ngozi za ndege zimakhala zochepa kwambiri.

Mukakwera ndege palibe chifukwa chodera nkhawa. Mukadzakhala pa ulendo wautali kwambiri wa pandege, dzakumbukireni kuti pali anthu ambiri amene akuyang’anira ndegeyo kuti mukafike bwino. Motero mtima wanu udzakhale m’malo n’kumangosangalala ndi ulendowo basi.

[Mawu a M’munsi]

^ ndime 4 Posachedwapa ku United States anapeza kuti chaka chimodzi chokha ndege zotenga anthu kumeneko zinayenda ulendo wa makilomita 11 biliyoni, ndipo pa maola 334,448 aliwonse pankachitika ngozi imodzi yokha.

[Chithunzi pamasamba 14, 15]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

MMENE AMADZIWIRA PAMENE PALI NDEGE YANU

Makina a mumlengalenga

 

 

 

 

 

 

 

Makina a pansi Chipangizo Nyumba yamphepo Chipangizo

choulutsira choonetsera

mawu pawailesi ndege pakompyuta

[Chithunzi patsamba 15]

Nsanja yothandiza kuona kayendedwe ka ndege

[Chithunzi patsamba 15]

Oona za kayendedwe ka ndege

[Chithunzi patsamba 15]

Ofesi yoona za kayendedwe ka ndege

[Mawu a Chithunzi patsamba 15]

Tower and controllers: NASA Ames Research Center; control center: U. S. Federal Aviation Administration