Zochitika Padzikoli
Zochitika Padzikoli
▪ M’zaka 6 zapitazi, “anthu pafupifupi 100,000 . . . aphedwa ku United States.”—THE NEW YORK TIMES, U.S.A.
▪ Kampani ina yothandiza anthu kuti azitha kucheza pa Intaneti yafafaniza maina a makasitomala 29,000 omwe ali ndi milandu yokhudzana ndi za chiwerewere. Loya wa Boma ku Connecticut, dzina lake Richard Blumenthal, anati: “Panafunika kuchitapo kanthu mwamsanga chifukwa choti kampaniyi inayamba kukhala ndi makasitomala ambiri omwe anapalamulapo milandu ya zachiwerewere.—REUTERS NEWS SERVICE, U.S.A.
▪ “Ku China kuli vuto la maina . . . M’chaka cha 2006, ofufuza anapeza kuti ngakhale kuti m’dzikoli muli anthu pafupifupi 1 biliyoni ndi theka, anthu 85 pa anthu 100 aliwonse ali ndi limodzi mwa mayina 100 okha a m’dzikoli.”—CHINA DAILY, CHINA.
▪ Pa kilomita iliyonse anthu ambiri oyenda pa njinga zamoto angafe pangozi za pamsewu poyerekezera ndi anthu oyenda pagalimoto.—UC BERKELEY WELLNESS LETTER, U.S.A.
Mboni za Yehova Zaloledwa Mwalamulo ku Turkey
Pa July 31, 2007, a Mboni za Yehova ku Turkey analoledwa kukhala chipembedzo chovomerezeka m’dzikolo. Zimenezi zithandiza kuti azitha kugula malo, kuchita lendi malo a misonkhano, kulandira zopereka ndiponso kuteteza ufulu wawo m’makhoti.
“Anthu Sachita Manyazi” pa Intaneti
Bungwe lina la pa Intaneti ku Germany linafalitsa chikalata chofotokoza zimene lachita pothandiza anthu apabanja kupeza munthu woti achite naye chigololo. M’chikalatamo, bungwelo linati lili ndi anthu 310,000 ndipo tsiku lililonse limalandira anthu 1,000 atsopano. Bungwelo limadzitama kuti limathandiza anthu okwatira kupeza zibwenzi “zomwe palibe aliyense amene angazitulukire.” Mmodzi wa akuluakulu a m’bungweli anati: “Anthu sachita manyazi pa Intaneti chifukwa amaona kuti palibe amene akuwadziwa. Motero n’zosavuta kuyamba kuuzana zakukhosi, mosabisa mawu.”
Afukula Zinthu Zotsutsana ndi a Sayansi
Asayansi ambiri amati pali mtundu wina wa anyani akale umene unadzasanduka mtundu wa anyani ofanana kwambiri ndi anthu. Ndipo patapita zaka zambiri zedi mtundu wofanana kwambiri ndi anthuwu unadzasanduka anthu. Komabe, ku Kenya afukula mafupa akale a anyani awiri a mitundu iwiriyi pa malo oyandikana ndipo apeza kuti anyaniwo anakhalapo nthawi imodzi. “Poti mitundu iwiri ya anyaniwa inakhalapo panthawi imodzi, n’zosatheka kuti mtundu umodziwo unasanduka n’kukhala winawo.” Anatero Meave Leakey yemwe analemba nawo lipotili.
Kodi Nyengo Imaipa Kwambiri Loweruka ndi Lamlungu?
Anthu ambiri ku Germany amaona kuti nyengo imaipa kwambiri Loweruka ndi Lamlungu. Kafukufuku wa mmene nyengo yakhalira m’madera osiyanasiyana kwa zaka 15 wasonyeza kuti zimenezi zingakhale zoona, inatero nyuzipepala ina. Tsiku lotentha kwambiri ndi Lachitatu ndipo lozizira kwambiri ndi Loweruka. Loweruka mvula imagwa kwambiri kuposa Lolemba ndipo kawirikawiri Lolemba sikugwa mvula. Lachiwiri kumakhala dzuwa kwambiri kuposa Loweruka. Ofufuza akuganiza kuti mpweya ndi utsi zimene zimatuluka m’kati mwa mlungu zimasonkhana chakumapeto kwa mlungu ndipo izi n’zimene zimachititsa kuti kukhale mitambo.—Der Spiegel.