Tsogolo Labwino mu Ulamuliro wa Mulungu
Tsogolo Labwino mu Ulamuliro wa Mulungu
POSACHEDWAPA sitidzadanso nkhawa poganizira za tsogolo lathu, chifukwa choti Mulungu adzayamba kulamulira dziko lonse pogwiritsa ntchito boma lake, lotchedwa Ufumu wa Mulungu. Poganizira za Ufumu umenewu, Yesu Khristu anauza otsatira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.”—Mateyo 6:9, 10.
Ufumu wa Mulungu sudzagwirizana kapena kuchita zinthu limodzi ndi atsogoleri andale. Koma mogwirizana ndi ulosi wa Danieli wonena za ‘masiku otsiriza,’ omwe ndi masiku athu ano, ufumuwo udzachotsa ulamuliro uliwonse wa anthu. (2 Timoteyo 3:1) Ulosiwu umati: “Masiku a mafumu aja Mulungu wa Kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthawi zonse . . . udzaphwanya ndi kutha maufumu [a anthu] nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Anthu amene amakonda ulamuliro wa anthu sangalimbikitsidwe ndi mawu amenewa. Koma mawuwa amalimbikitsa anthu onse amene amafuna kulamuliridwa ndi Ufumu wa Mulungu.
Tsogolo Labwino Kwambiri
Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira dziko lapansi, anthu onse sadzagawanikanso chifukwa cha ndale, fuko, chipembedzo, kapena malire a mayiko amene anthu anaika. Koma adzakhala ogwirizana padziko lonse chifukwa chodziwa choonadi chonena za Mulungu ndiponso chifukwa cha chikondi chenicheni. (Yohane 13:34, 35; 17:3, 17) Inde, mu Ufumu wa Mulungu, “wolungama adzakhazikika,” ndipo padzakhala “mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.”—Salmo 72:7.
Ufumu wa Mulungu udzachititsanso kuti anthu onse omvera akhale ndi matupi ndiponso maganizo angwiro, ndipo udzachotsa matenda onse, kuvutika ndiponso imfa. (Chivumbulutso 21:3, 4) Ndiyeno chidzachitike n’chiyani? Dziko lathu lonse lidzakhala paradaiso weniweni pokwaniritsa cholinga chimene Mulungu ananena mu Edeni. *—Genesis 1:28.
Uthenga Wabwino Weniweni
Ponena za chizindikiro cha “mapeto a dongosolo lino la zinthu,” Yesu anatchulanso chinthu china chochititsa chidwi. (Mateyo 24:3-7) Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukakhale umboni ku mitundu yonse; kenako mapeto adzafika.”—Mateyo 24:14.
Mogwirizana ndi cholinga cha Mulungu, m’chaka cha 2007, Mboni za Yehova pafupifupi 7 miliyoni zopezeka m’mayiko 236 zinalalikira uthenga wa Ufumu kwa anthu anzawo. Iwowa anatha maola pafupifupi 1 biliyoni ndi theka kuchita ntchito yosangalatsayi. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova sakayikira ngakhale pang’ono za malonjezo a m’Baibulo? Yankho la funso limeneli n’losavuta. Monga mmene nkhani yotsatirayi ikufotokozera, nthawi zonse Mulungu amachita zimene walonjeza.—Aroma 3:4.
[Mawu a M’munsi]
^ ndime 6 Onani nkhani yakuti “Zimene Baibulo Limanena: Kodi Dzikoli Lidzakhala Paradaiso?” patsamba 10.
[Mawu Otsindika patsamba 7]
Baibulo limanena kuti padzikoli padzakhala “mtendere wochuluka”